Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Yeniyeni Yothetsera Umphawi

Njira Yeniyeni Yothetsera Umphawi

Njira Yeniyeni Yothetsera Umphawi

ANTHU ambirimbiri padziko lonse lapansi amavutika pamoyo wawo tsiku ndi tsiku chifukwa choti ali pa umphawi wadzaoneni. N’zachionekere kuti anthu akufunikira boma lachilungamo ndiponso lopanda katangale lofunitsitsadi kuthetsa kupanda chilungamo kumeneku. Boma limenelo liyeneranso kukhala lamphamvu mokwanira kuti lithe kukwaniritsadi zolinga zake zabwinozo. Kodi n’chinthu chanzeru kuyembekezera anthu kubweretsa boma loterolo?

Zomwe zachitika m’mbiri ya anthu zasonyeza kuti chenjezo la m’Baibulo lotsatirali n’loona: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Salmo 146:3) Kodi inuyo mwaonapo kuti kukhulupirira maboma a anthu kapena atsogoleri, nthawi zambiri kumakhumudwitsa? Komabe, kodi winanso ndani amene angatithandize?

Anthu ambirimbiri apempherapo kuti kubwere boma lachilungamo loti lisinthe kupanda chilungamo kumene kulipoku. Mwina inunso munapempherapo pemphero lachitsanzo limene Yesu anaphunzitsa, loti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu. Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.”—Mateyu 6:9-13.

Kodi Ufumu umenewu ndi umene tikufunikira? Kodi ndi wolungama ndiponso woti sungayambe kuchita zinthu zakatangale? Kodi ndi wamphamvu mokwanira moti ungakwanitsedi zolinga zake zabwino? Inde, ndi woterodi. Mulungu, “Atate wathu wa Kumwamba” amene anakhazikitsa boma limeneli, ndi “Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi,” ndipo ali “wolungama mu ntchito zake zonse.” (Yesaya 45:21; Danieli 9:14) Baibulo limamufotokoza kuti: “Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa.” (Habakuku 1:13) Choncho tingakhale n’chikhulupiriro kuti boma lake silidzayamba kuchita zinthu zakatangale. Ndipo popeza “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye,” tikudziwa kuti iye mosakondera amafuna kuti munthu aliyense padziko lapansi pano akhale ndi moyo wabwino.—Machitidwe 10:34, 35; Aroma 2:11.

Unakhazikitsidwa Kale Ndipo Ukugwira Ntchito

Ngakhale kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba, udzayendetsa zinthu padziko pano kuti ukwaniritse zolinga za Mulunguyo. Chimodzi mwa zolinga zimenezi ndicho kuchotsa maboma a anthu operewerawa n’kukhazikitsa boma la Mulungu. Pa Danieli 2:44 pali lonjezo lakuti: “Ndipo masiku a mafumu [maboma] aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.”

Mu Ufumu umenewu, chifuniro cha Mulungu chidzachitikadi kumwamba ndi padziko lapansi pano. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti limeneli ndi boma lomwe lidzathe kuchotseratu zoipa zonse zomwe zabwera chifukwa cha kupanda chilungamo komwe kwachititsa kuti pakhale kusiyana kwakukulu pakati pa anthu olemera ndi osauka. Sipadzakhalanso anthu ochepa okha olemera ndi anthu ambirimbiri osauka.

Ndipo n’zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti boma lakumwamba la Mulungu lakhazikitsidwa kale kuti lithetse mavuto amenewa kwamuyaya. Kuwerengera nthawi ya zochitika za m’Baibulo, ndiponso kuona zinthu zimene zakhala zikuchitika padziko lapansili, kumasonyeza bwino kuti chaka cha 1914 n’chimene boma la Mulungu linakhazikitsidwa kumwamba. * Choncho, kwa zaka pafupifupi 100, boma limeneli lakhala likukonza maziko a dziko latsopano lachilungamo.

Anthu amene azindikira za kukhazikitsidwa kwa Ufumu umenewu ndiponso amene akumvera malangizo ake alibe tsankho. Mboni za Yehova zimagwira ntchito yawo yolalikira pafupifupi m’dziko lililonse. Anthu okhala m’mayiko amenewa, kaya akhale olemera kapena osauka, amapatsidwa mwayi wodziwa momwe angapezere moyo wosatha. (Yohane 17:3) Popatsa anthu maudindo mu mpingo, Mboni sizitengera kuti kaya munthuyo ndi wopeza bwino kapena wosauka. Anthu sapatsidwa ulemu chifukwa cha zinthu zimene ali nazo, koma amalemekezedwa chifukwa cha makhalidwe awo. Katundu ndi ndalama saziwerengera koposa makhalidwe auzimu.

Kodi mungakonde kudziwa zomwe mungachite kuti mudzakhale m’dziko lolamulidwa ndi boma lachilungamo limeneli? Ngati ndi choncho, yambani lero kufufuza. Phunzirani zomwe mungachite kuti mudzathe kudzakhala ndi moyo mosangalala panthawi imene dziko lapansi silidzakhalanso logawanika chifukwa cha chuma.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Onani masamba 95 mpaka 107 a buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 8, 9]

Onse ndi Abale, Kaya Akhale Olemera Kapena Osauka

▪ Kumapeto kwa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, Mboni za Yehova zambiri ku Ulaya ndi ku Asia zinkafunikira thandizo la chakudya, zovala, ndi nyumba. Mboni za m’mayiko ena zinatumiza zovala ndi zakudya zambirimbiri kwa abale awo auzimu ku Ulaya, ku Philippines, ndi ku Japan. Mboni za ku United States ndi ku Canada zinasonkha chithandizo chomwe chinatumizidwa ku Austria, Belgium, Czechoslovakia (tsopano ndi Czech Republic ndi Slovakia), England, Finland, France, Germany, Greece, Holland, Hungary, Italy, Poland, ndi Romania.

[Zithunzi]

United States

Switzerland

Germany

▪ Posachedwapa, mu 1994, gulu la anthu ongodzipereka a Mboni ochokera ku Ulaya linapititsa thandizo mwamsanga kwa abale ndi alongo awo auzimu ku Africa. Mboni zinakonza misasa ndi malo operekerapo chithandizo cha mankhwala kuti zithandize anthu othawa kwawo a ku Rwanda. Zinatumiza zovala, mabulangete, chakudya, ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo ambirimbiri kuti akathandize anthu opitirira 7,000 amene anali kuvutika. Anthu amenewa anali owirikiza pafupifupi katatu chiwerengero cha Mboni za Yehova za ku Rwanda panthawi imeneyo.

▪ Patatha zaka ziwiri kuchokera pamenepa, mu 1996, nkhondo inayambika ku dera lakum’mawa kwa dziko la Democratic Republic of Congo. Mbewu za m’munda zinawonongedwa, chakudya chimene anthu anasunga chinabedwa, ndipo njira zodutsa pokatula chithandizo zinatsekedwa. Anthu ambiri ankangodya kamodzi kokha patsiku, motero ambiri anali ndi vuto la kuperewera kwa zakudya m’thupi ndipo anadwala matenda osiyanasiyana. Mboni za Yehova za ku Ulaya zinachitapo kanthu mwamsanga. Gulu la anthu a Mboni oti akathandize, kuphatikizapo madokotala, linafika kumeneku pandege litatenga ndalama ndiponso chakudya. Pofika mu June 1997, Mboni za ku Belgium, France, ndi Switzerland zinali zitapereka mankhwala olemera makilogalamu 500, matani 10 a mabisiketi opatsa thanzi, matani 20 a zakudya zina, matani 90 a zovala, mapeyala 18,500 a nsapato, ndi mabulangete 1,000. Zonsezi mtengo wake unali pafupifupi madola 1,000,000.

▪ Kuwonjezera pa kupereka chithandizo kwa anthu, Mboni za Yehova zimalimbikira makamaka kuthandiza anthu mwauzimu. N’chifukwa chake zimafunitsitsa kumanga Nyumba za Ufumu kuti anthu aziphunziriramo zinthu zauzimu. Mu 1997, lipoti lina linati: “Ndi thandizo lochokera kwa abale m’mayiko ena, bungwe la [Watch Tower] Society lathandiza kumanga Nyumba za Ufumu zatsopano zokwana 413 ndi kukonzanso zina 727 pa miyezi inayi yokha m’mayiko 75.” Pofika mu 2003, lipoti linanso linati: “Limodzi mwa mayiko a ku Ulaya amene akupindula ndi njira yothandiza kuti m’mayiko osauka mumangidwe Nyumba za Ufumu ndilo dziko la Romania, kumene Nyumba za Ufumu 124 zamangidwa kuyambira mu July 2000. M’dziko la Ukraine anagwiritsira ntchito pulani yomangira nyumba zosasiyana kwenikweni mamangidwe ake, motero anamanga Nyumba za Ufumu 61 mu 2001 ndipo m’chaka cha 2002 anamanga zinanso 76. Pogwiritsira ntchito ndalama zimene zinasonkhedwa ku Thumba la Nyumba za Ufumu, Nyumba za Ufumu zambiri zamangidwa ku Bulgaria, Croatia, Macedonia, Moldova, Russia, ndiponso ku Serbia ndi Montenegro.”

[Zithunzi]

Croatia

Bulgaria

Romania

[Chithunzi patsamba 7]

Munthu wongodzipereka akusamalira ana amasiye awiri othawa kwawo

[Mawu a Chithunzi]

© Liba Taylor/Panos Pictures

[Chithunzi patsamba 10]

Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wa chiyembekezo

[Chithunzi patsamba 10]

Ufumu wa Mulungu udzathetsa umphawi