Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhondo Imene Inasintha Moyo Wanga

Nkhondo Imene Inasintha Moyo Wanga

Nkhondo Imene Inasintha Moyo Wanga

YOSIMBIDWA NDI MICHAEL MOLINA

‘Dziko la Viet Nam linapatsa a Molina, mendulo yaulemu chifukwa cha kulimba mtima kwawo pa nkhondo ya ku Vietnam,’ inatero nyuzipepala ya asilikali yotchedwa “Tester,” ya m’boma la Maryland, ku United States. ‘Pambuyo pake a Molina anapatsidwanso mendulo ina ya golide yomwe inali mphoto yachiwiri imene anapatsidwa chifukwa cha kulimba mtima ndiponso kumenya nkhondo mosaopa pa nkhondo inanso imene panali kuwomberana kwadzaoneni. Pa June 6, 1968, a Molina analandiranso mendulo yagolide yachiwiri chifukwa choti anagonjetsa zigawenga za Viet Cong zomwe zinkafuna kulanda kampu ya asilikali.’

NDINAPITA kukamenya nkhondo maulendo 284 ndipo ndinalandira mamendulo 29. Panopo ndine mtumiki wachikristu ndipo ndikumenya nkhondo yamtundu wina. Pa za nkhondo imeneyi Baibulo limati: “Zida za nkhondo yathu sizili za thupi.” (2 Akorinto 10:4) Lekani ndilongosole mmene ndinasinthira kuti moyo wanga ufike pamenepa.

Mzinda wa Chicago uli kumpoto kwa boma la Illinois, ku United States, ndipo nthawi zambiri kumeneku kumawomba chimphepo champhamvu kwambiri chochoka m’nyanja ya Michigan. Ndinabadwira kumeneku pa February 1, 1947, ndipo patsikulo kunali mphepo komanso chisanu chadzaoneni. Popeza bambo anga anali atangomenya nawo nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, madokotala awiri a asilikali ndiwo anali azamba a mayi anga pamene ineyo ndinkabadwa. Ndili ndi zaka teni, banja lathu linasamukira ku Los Angeles, ku California, ndipo ineyo, mkulu wanga, ndi mlongo wanga tinaphunzira pa sukulu ya Akatolika kumeneko.

Ndili mwana ndinkasewera mpira mumsewu ndi m’mapuloti omwe anali asanamangemo nyumba, koma ndinkachitanso masewera oyerekezera kuti ndine msilikali pogwiritsira ntchito mfuti zamatabwa zopanga tokha. Ndinapita ku sekondale cha m’ma 1960 ndipo m’zaka zimenezi anthu anayamba kusintha kwambiri pa kaganizidwe kawo. Nthawi imeneyi inatchuka ndi kuphedwa kwa atsogoleri osiyanasiyana komanso andale ndipo mu 1963 pulezidenti wa dziko la United States anawomberedwa. Anthu ankachita zionetsero zotsutsa boma, ankawotcha mbendera ya dziko la United States, ndiponso ankachita zionetsero zachiwawa. Ndili pasukulu, ineyo pamodzi ndi anzanga ambiri a m’kalasi mwanga tinkaopa kuti aboma atikakamiza kulowa usilikali.

Nditangomaliza sukulu ya sekondale mu 1966, ndinaitanidwa ndi boma kuti akandione ngati ndikuyenerera usilikali. Atandiyeza anapeza kuti ndili ndi thanzi labwino. Koma m’malo mondipititsa ku gulu la asilikali wamba, ndinalowa gulu la asilikali apamadzi. Ndege za helokopita zinkanditenga mtima kwambiri, motero ndinalembetsa mwakufuna kwanga kuti ndikhale m’kagulu katsopano ka asilikali apamadzi oyenda pa helokopita. Mu November 1967, nditangomaliza maphunziro oyamba ausilikali, ndinatumizidwa ku mzinda wa Saigon, womwe uli likulu la dziko la Vietnam.

Zoyamba Kukumana Nazo Kunkhondo

Posakhalitsa, ndinatumizidwa ku kabwalo kenakake ka ndege, komwe kanali ndi ndege zinayi za helokopita. Amalinyero ena 30 am’gulu lathu anagona pa bwaloli, koma enafe tinkakhala ku nyumba inayake ya nsanja ziwiri pamtunda wa makilomita 16 kuchoka pabwaloli. Tsiku loyamba, usiku ndinadzidzimuka nditamva zipolopolo zikubowola nyumbayo. Ndinagudubuzika kuchoka pa kabedi kanga n’kugona chafufumimba kwa kanthawi kochepa chabe. Nditamva kuwomba mfuti cha pamwamba panyumbayo ndinakwera kudenga, komwe msilikali wina anandipatsira mfuti. Tinamenya nkhondo usiku wonse, popanda nsapato komanso titangovala zovala zam’kati basi.

Chakudya, madzi ndiponso zipolopolo zathu zambiri zinatha titamenya nkhondo molimba kwa masiku atatu kwinaku adani atatizinga ndiponso tili kutali kwambiri ndi asilikali anzathu. Msilikali wotitsogolera analamula kuti: “Dzuwa likangotuluka tithawe mwamsanga kupita ku kabwalo kandege kaja.” Tinayenera kudutsa pa katauni kena kamene kanali kuyaka moto wokhawokha. Tikudutsa m’kataunika tinkamva kulira kwa mfuti zosiyanasiyana. Mitembo inangoti mbwee.

Komabe tinafika pa kabwalo ka ndege kaja, ndipo ngakhale pamenepa zinthu sizinali bwino ayi. Tinakumba maenje kuzungulira bwalo lonselo n’kumenya nkhondo molimba kuti tithamangitse adaniwo. Nthawi zingapo asilikali a Vietcong analowerera n’kufika pa bwalopo, n’kupha asilikali athu ambiri, kuphatikizapo msilikali wathu wamkulu. Ndinakhala m’dzenje kwa milungu ingapo popanda kusintha zovala kapena kusamba. Kenaka kunabwera helokopita imene inatisamutsira ku malo ena a asilikali.

Nditamenya nkhondo kwa masiku oyambirirawa, ndinatsimikiza mtima kukhala msilikali woomba mfuti pa khomo la helokopita. Anandiphunzitsa kwa masiku angapo ndipo ndinalowa m’gulu la asilikali oyenda pandege. Nthawi zambiri tinkangokhalira kuwomberana ndi adani; nthawi zina ndinkapita ku malo omenyera nkhondo katatu kapena kanayi patsiku.

Mmene Nkhondoyo Inandikhudzira

Ndinakhumudwa kwambiri kuona anthu ambirimbiri akuphedwa. Panthawi yomweyi ndinkaganizanso za zionetsero zotsutsa nkhondoyi zomwe anthu ankachita kwathu ku United States. Ndiye ndinkaganiza kuti, koma ifetu tikumenyera ufulu! Tikuika moyo wathu pachiswe kuti ena akhale ndi moyo wabwino. Komabe chilungamo cha nkhondoyi sindinkachiona ayi. Ndani amene akanapindula ndi nkhondoyi? Kapena anthu a ku Vietnam? Anthuwa anali kale pa nkhondo kwa zaka zambiri ifeyo tisanafike kudzamenyana nawo. Nkhondo yathuyi inangowonjezera anthu akufa ndi ovutika m’dzikoli.

Ndinali ndikadali wamng’ono ndipo sindinkamvetsa mikangano yandale imene inachititsa nkhondo imeneyi. Komanso ndinalibe nthawi yoganizira nkhaniyi mofatsa. Ndinkangoganizira za malo amene nditumizidwe kukamenya nkhondo chifukwa imeneyo ndiyo ntchito imene ndinaphunzitsidwa. Asilikali anzathu omwe anali amalinyero ankanena kuti, “Tinaphunzitsidwa kumenya nkhondo, osati kuganiza ayi.” Komabe ineyo ndinadzilonjeza ndekha kuti ndikapulumuka, ndikafufuza mozama kuti ndimvetse chifukwa chimene tinkamenyera nkhondoyi.

Nkhondo ya ku Vietnam inandiyambitsa mankhwala osokoneza bongo, ndipo izi zinandisokoneza kwambiri. Ndili mnyamata wamng’ono, ndinkasuta fodya, Loweruka ndi Lamlungu ndinkamwa mowa, ndipo ndinkapita kumapwando. Koma ndinali ndisanakhudzepo mankhwala osokoneza bongo. Ku Vietnam zinthu zinasintha. Anzanga ena ankandiuza kuti: “Mike, tangochitako pang’ono chabe! Ukudzivutitsiranji munthu woti ungathe kufa ngakhale mawamawali?” Motero, nthawi zina ndinkavomera.

Koma pokamenya nkhondo supita utasokonezeka bongo ayi ndipo ineyo ndinalumbira kuti sindidzayerekeza n’komwe kutero. Koma nditabwerera kumudzi chibaba cha zinthu zotere sichinandithere, motero sindinazileke.

Kubwerako Kunkhondo

Nditabwerera kunyumba ku California kuchoka ku Vietnam mu October 1970, ndinali nditayamba kuona moyo m’njira yosiyana kwambiri. Ndinkaona kuti ngakhale kuti ndinalowa usilikali n’cholinga chothandiza kubweretsa ufulu, anandilima pamsana. Motero kunkhondoko ndinabwerako ndili ndi mkwiyo ndiponso ukali wadzaoneni. Ndinapulukira komanso zomenyera nkhondo dziko lathu ndinalibe nazo ntchito.

Masiku ambiri ndinkangokhalira kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo kwinaku ndikukonza njinga yanga yamoto m’galaja ku nyumba ya makolo anga. Vuto langa linkangowonjezeka chifukwa chodandaula ndiponso kuganizira zimene ndinakumana nazo ku Vietnam. Ndinayamba kuvutika chikumbumtima ndipo ndinayamba kufunitsitsa kwambiri kudziwa chifukwa chimene nkhondo ya ku Vietnam ija inachitikira.

Boma linkathandiza anthu amene anachoka kunkhondo pa maphunziro awo, motero ndinayamba kuphunzira pa koleji inayake ya boma ndipo kenaka ndinapita ku yunivesite ya California State University ku Los Angeles. Kumeneko ndinayamba kugwirizana ndi anthu ena amene anachitapo zionetsero zotsutsa nkhondo ya ku Vietnam ija, komanso ena amene anamenya nawo nkhondoyo. Tinkakambirana kwa nthawi yaitali za nkhondoyo ndiponso za mmene zinthu zikuyendera padziko. Palibe aliyense wa ife amene ankamvetsa bwinobwino zimene zikuchitika. Tonse tinasokonezeka maganizo.

Kuyesetsa Kuthandiza Ena Ndiponso Kupeza Thandizo

Ambirife tinali ndi nkhawa ndiponso mavuto a m’maganizo. Mtima wanga unafuna kuthandizapo. Motero kusukulu ndinasankha maphunziro a matenda a m’maganizo. Popeza ndinapha anthu ambirimbiri kunkhondo, ndinaganiza zochita ntchito yoti indiziziritse mtima pa zimene ndinachitazi. Motero, ndinayamba kugwira ntchito m’zipatala za anthu osokonezeka maganizo.

Pa yunivesite yathu, anthu ambiri ankagwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, ndipo ndinaona kuti ichi n’chifukwa chake ambiri anali ndi mavuto ochuluka. Ndinafuna kupitiriza maphunziro anga ndi kumathandiza odwala amene anali kuchipatala chifukwa cha mavuto a m’maganizo. Motero ndinasiyiratu mankhwalawa n’kuyamba kulimbikira kwambiri maphunziro ndi ntchito yanga. Komano ndinaona kuti anthu amene ndinali kuwathandizawo mavuto awo a m’maganizo sankatheratu ayi.

Motero ndinafika potopa ndi moyo wa nthawi inowu ndiponso moyo womangokhalira kuvutitsidwa ndi chikumbumtima, moti ndinayamba kufunafuna thandizo kuti ndisiye kuvutika chonchi. Ndinayamba kupemphera ndiponso kupita kutchalitchi. Koma ku misa ya tchalitchi cha Katolika sindinkaphunzirako chilichonse chogwira mtima. Motero ndinayamba kupita kutchalitchi usiku. Ndinkalowa m’tchalitchimo, n’kuyatsa kandulo, n’kumapemphera moyang’ana mafano am’tchalitchimo. Anali mafano a Yesu ali pamtanda ndiponso a Mariya mtima wake utalasidwa ndi mpeni, ndipo munali mafano ena a anthu amene amatchedwa oyera mtima.

Ndinayamba kuganiza kuti: ‘Kutchalitchi kuno ndi malo osasangalatsa ngakhale pang’ono! Zoona mzimu wa Mulungu ungapezeke malo ngati ano?’ Nzeru zinandithera ndipo ndinalefuka kwambiri. Kuona mavuto kunali kutandikwana. Motero tsiku lina usiku ndinachoka m’tchalitchi n’kukapempherera kwina. Ndinayang’ana nyenyezi kumwamba ndipo n’kutheka kuti aka kanali koyamba m’moyo mwanga kuyesa kupemphera ndi mtima wonse kwa Mlengi wanga.

Kuphunzira Choonadi cha M’Baibulo

Nthawi ina pa Loweruka ndi Lamlungu ndinapita kwa mnzanga wina wakalekale dzina lake Gary pofuna kupumako pang’ono ntchito yanga yotopetsa yachipatala. Tsiku lina tinakhala pa balaza n’kumaonera nkhani pa TV. Nkhani zake zinali zoti pulezidenti Nixon akufuna kum’chotsa pampando. Motero tinayamba kukambirana nkhani ya mmene anthu osiyanasiyana amachitira zakatangale, ndipo ndinalongosola kuti ndimaona kuti anandidyera masuku pamutu ku nkhondo ya ku Vietnam ija.

Mkazi wa mnzangayo dzina lake Alva, anatimva tikukambirana zimenezi ndipo anatuluka m’khitchini. Iye ananena kuti zinthu zangati zimene timakambiranazo zikuchitika chifukwa choti zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. Ndiye ineyo ndinafunsa kuti: “Mavuto okhudza pulezidenti akugwirizana bwanji ndi ulosi wa m’Baibulo?” Alva anandilongosolera kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu motsogoleredwa ndi Kristu Yesu udzachotsa maboma aziphuphu onsewa ndi kuti anthu adzakhala kosatha mumtendere padziko lapansi lomwe adzalisandutse paradaiso. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3, 4) Alva anatchulapo za Pemphero la Ambuye, lomwe tikamanena timapempha kuti Ufumu wa Mulungu udze ndi kuti kufuna kwa Mulungu kuchitike padziko monga kumwamba.—Mateyu 6:9, 10.

Ndinaona kuti tikufunikiradi kutsogoleredwa ndi Mulungu kuti tikhale ndi boma labwino ndiponso mtendere weniweni padziko pano. (Mlaliki 8:9; Yeremiya 10:23) Pankhani yoti anthu angathe kukhala ndi moyo kosatha, ndinakumbukira zimene ndinaphunzira zoti maatomu amene amapanga thupi lathuli sachedwa kutha n’kupangika ena atsopano. Ngakhale kuti Alva ananena zinthu zina zondivuta kukhulupirira, anandisiyira mfundo zambiri zofunika kuziganizira. Popeza kuti ndinazunza kwambiri anthu ndinkafuna kuchita zinazake zothandiza anthu pa mavuto awo kuti zikhale ngati zafafaniza zoipa zimene ndinachitazo. Alva anandilangiza kuti ndipite ku Nyumba ya Ufumu, kuti ndikadziwe zambiri.

Mumpingo umene ndinapitako munali Bill Akina, yemwe anali mtumiki wa nthawi zonse. Komanso chifukwa choti pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse iyeyu anali m’gulu la asilikali a nkhondo yapamadzi, zinali zosavuta kwa ine kumvana naye. Koma chachikulu chinali choti iyeyu Baibulo ankalidziwa bwino, ndipo mothandizana ndi mkazi wake, anayankha mafunso anga ambiri ndi Baibulo. Maphunziro anga ndi Bill atapita patali, ndinaona kuti ngakhale kuti cholinga changa chinali chabwino pofuna kuthandiza anthu kuchipatala, thandizo langa linali losakhalitsa ayi. Koma ndinaona kuti kuthandiza anthu kudziwa zenizeni za m’Baibulo kungawapatse moyo wosatha ngati atakhulupirira n’kutsatira zimene aphunzirazo.—Yohane 17:3.

Bill anaphunzira nane Baibulo pogwiritsira ntchito buku lothandiza pophunzira Baibulo lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Mu July 1974 ndinabatizidwa posonyeza kuti ndadzipereka kwa Mulungu. Patatha miyezi sikisi ndinakhala mpainiya, kapena kuti wa Mboni za Yehova wolalikira uthenga wabwino nthawi zonse. Apa n’kuti nditasiya kuphunzira pa yunivesite paja ndiponso kugwira ntchito pachipatala chija. Pofuna kuti ndizipeza ndalama zondithandiza pa utumiki wanga, ndinapeza ntchito yokolopa m’banki usiku. (1 Atesalonika 4:11) Anzanga ndiponso achibale ankaganiza kuti mutu wanga sukuyenda bwino.

Nditachita upainiya ku California mwina kwa chaka chimodzi, ndinayamba kuganizira za zimene ndingachite kuti andigwiritsire ntchito kwambiri potumikira Yehova. Ndinaganiza zokhala ndi cholinga chokachita ntchito yaumishonale kunja. Nditachita upainiya kwa zaka zingapo, ndinaitanidwa kuti ndikachite nawo Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo, imene panthawiyo inali ku Brooklyn, ku New York. Ineyo ndinali m’kalasi ya nambala 66 ya sukuluyi ndipo mwambo wokondwerera kuti tamaliza maphunziro unachitika pa March 11, 1979, mumzinda wa Long Island City, ku New York.

Kuchita Utumiki Wosiyanasiyana

Ndinatumizidwa ku Guatemala, ku Central America, kumene ndinatumikira monga mmishonale pafupifupi chaka chathunthu. Kenaka anandiitana kuti ndikagwire ntchito pa fakitale yaing’ono ya Mboni za Yehova yosindikiza mabuku mumzinda wa Guatemala City womwe uli likulu la dzikoli. Mu 1981 ndinakwatira mpainiya wina wa kumeneko dzina lake Lupita, ndipo anamuitana kudzakhala nane limodzi pa ofesi ya nthambi. Kenaka, mu 1996 tinaleka kusindikiza mabuku ku Guatemala titayamba kulandira mabuku athu onse kuchokera ku nthambi ya ku Mexico.

Mwana wathu, Stephanie anabadwa mu 1984, koma ineyo ndinapitiriza kutumikira pa ofesi yanthambi ngakhale pamene tinakhala ndi mwana wachiwiri dzina lake Mitchell mu 1987. Sizophweka kukhala kunyumba yakutali ndi ofesi ya nthambi n’kumachita kuyendera kwa mtunda wautali pafupifupi makilomita 10 tsiku lililonse. Koma ndimaona kuti ndimwayi waukulu kutumikira m’njira imeneyi, ndipo banja langa landithandiza kwambiri kutero.

Mkazi wanga Lupita ndi mwana wanga Stephanie tsopano ndi apainiya, ndipo Mitchell ndi mtumiki wobatizidwa. Amaliza chaka chinocho kosi imene akuchita, ndipo cholinga chake n’choti achite utumiki wa nthawi zonse. Ndikudziwa kuti mwayi wapadera wotumikira m’njira zimenezi sitinaupeze chifukwa cha luso lathu koma chifukwa cha chisomo cha Yehova. Iye ndi Mulungu wachikondi, ndipo angathe kugwiritsira ntchito munthu aliyense amene ali ndi mzimu wofuna kutumikira ndiponso amene amamumvera.

Nthawi zina anthu amatifunsa kuti banja lathu limatha bwanji kuchita zinthu zambiri chonchi muutumiki komanso panthawi yomweyo n’kumatha kudzisamalira. N’chifukwa choti timagwira ntchito panthawi imene tili patchuthi. Koma chachikulu n’chakuti, timayesetsa nthawi zonse kukhala a ‘diso lakumodzi’ pa zinthu zakuthupi, kudalira Yehova kuti atithandize, kumukhulupirira ndiponso kulola kuti iye azititsogolera nthawi zonse.—Mateyu 6:25-34; Miyambo 3:5.

Kukhala ndi mfuti kunkandipangitsa kumva kuti ndili ndi mphamvu, motero masiku ano ndimaona kuti ndikufunika kumenyera nkhondo kuti ndizichita zinthu modzichepetsa. Dziko la Satanali linandiphunzitsa chidani, kupha, kukayikira ena, kuchita zamtopola, ndiponso kukonda kusavomereza zolakwa zanga. Koma Yehova wandichitira chifundo ndi kundisonyeza kukoma mtima kwachikondi, motero ndimayamikira kwambiri. Tsopano ndine wotsimikiza mtima kwambiri kusaphunzira nkhondo ndipo ndine wotsimikiza kukhala wachikondi ndiponso wachifundo kwa munthu aliyense.—Mateyu 5:43-45; Yesaya 2:4.

Ndavutika kwambiri kuti ndisinthe khalidwe langa. Komabe panopo ndaphunzira kukhala moyo wamtendere. Chinanso Mulungu wandithandiza kuthana ndi maloto oipa a kunkhondo. Ndimayembekeza ndi mtima wonse nthawi imene nkhondo zidzathe. (Salmo 46:9) Panopo, ndikuyamikira kwambiri kukhala ndi mwayi wochita nawo ntchito yopulumutsa anthu powathandiza kudziwa za Wopatsa Moyo wamkulu, Yehova Mulungu.

[Zithunzi patsamba 12]

Ndinali msilikali woomba mfuti pakhomo pa ndege ya helokopita

[Chithunzi patsamba 14]

Ndili ndi Bill Akina ndi mkazi wake, Eloise, mu 1978

[Chithunzi patsamba 15]

Ndikugwira ntchito mu fakitale yosindikiza mabuku pa ofesi ya nthambi ya ku Guatemala, mu 1982

[Chithunzi patsamba 15]

Ndikulalikira ndi mkazi wanga

[Chithunzi patsamba 15]

Panopo ndili ndi Lupita, Mitchell, ndiponso Stephanie