Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tikakumane Pachitsime”

“Tikakumane Pachitsime”

“Tikakumane Pachitsime”

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU MOLDOVA

MKWATIBWIYO akungoyang’ana mtima uli m’mwamba pamene madzi akutungidwa m’chitsime n’kuthiridwa pamsewu. Kenako akusekerera chimwemwe chitadzaza tsaya pamene mkwati akumunyamula n’kudumpha naye pamsewu ponyowapo. Anzawo ndi abale awo abwera kudzaonerera ndi kudzalulutira pamene iwo akuchita ukwati motsatira mwambo wakale kwambiri umenewu. Mwambo wapaukwati wachilendowu ukusonyeza bwino kuti ku Moldova, chitsime chimagwira ntchito zambiri kuposa kungotungapo madzi akumwa.

Dziko la Moldova lili kum’mwera chakum’mawa kwa Ulaya, ndipo lazunguliridwa ndi dziko la Ukraine kumpoto, kum’mawa, ndi kum’mwera kwake. Kumadzulo kwake kuli dziko la Romania. Dzikoli ndi lalikulu masikweya kilomita 34,000.

Ngakhale kuti m’dziko la Moldova muli mitsinje pafupifupi 3,100, chifukwa cha chilala nthawi zambiri mitsinjeyi sikhala ndi madzi okwanira oti anthu 4,300,000 a m’dzikoli athe kugwiritsa ntchito. Pofuna kuwonjezera pa madzi a m’mitsinje ndi m’nyanja, madzi ena m’dzikoli amachokera m’zitsime. M’chigawo cha m’dzikoli cha m’chigwa cha Prut, akuti mwina muli zitsime pakati pa 100,000 ndi 200,000.

Zitsime za ku Moldova zimenezi zimakhala ndi zivundikiro zokongoletsedwa bwino, komanso popeza zinakumbidwa m’mphepete mwa misewu ndi tinjira, anthu ambiri apaulendo amaima pa zitsimezi kukakonkha ludzu lawo. M’midzi yambiri m’dzikoli, chitsime cha m’mudzi chimakhalanso malo amene anthu amakakumana ndi anzawo n’kumakambirana zochitika za tsiku limenelo.

Amalemekeza Madzi Pachikhalidwe Chawo

Ku Moldova, anthu amasonyeza kuti amalemekeza madzi a m’zitsime m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, zimbudzi amazikumbira kutali ndi chitsime cha banja, ndipo pofuna kusaipitsa madzi a m’chitsimecho, amaletsa kuthiramo madzi amene atsala m’chidebe chotungira. Ngati munthu watunga madzi ambiri kuposa amene amafuna, otsalawo amawataya pansi kapena amawathira m’chidebe china chimene chimakhala pafupi ndi chitsimecho. Kuwonjezera apo, amaona kuti ndi khalidwe loipa kulavula pansi pafupi ndi chitsime. Ndipotu pa mwambo wawo, amaletsa ngakhale kukangana pafupi ndi chitsime!

Zitsime zimachititsa kuti anthu a ku Moldova azikhala ogwirizana. Ntchito yokumba chitsime chatsopano amaiona kuti ndi ntchito yoti anthu agwirire limodzi ndipo amaiona kuti ndi yofunika mofanana ndi ntchito yomanga nyumba yatsopano. Zimenezi zimaonekera m’mwambi umene ali nawo woti, Munthu amene walephera kumanga nyumba, kulera mwana wamwamuna, kukumba chitsime, ndi kudzala mtengo, ndiye kuti wangowononga moyo wake pachabe. Akatha kukumba chitsime, anthu onse amene anagwira nawo ntchitoyo amawaitana ku phwando lalikulu.

Kuwonongeka kwa Madzi

Zitsime zambiri ku Moldova madzi ake amachokera pansi pakuya mamita 5 mpaka 12 kuchokera pamtunda. Madzi ena amapezeka pansi pakuya mamita 150 mpaka 250 kuchokera pamtunda. Ngakhale kuti anthu amayesetsa pachikhalidwe chawo kutsatira njira zotetezera madziwa, madzi ambiri a pansi ku Moldova anawonongeka chifukwa cha mankhwala amene anachokera ku mafakitale ndi ku feteleza kalekale. Chikalata chimene bungwe la United Nations linatulutsa mu 1996 chotchedwa Republic of Moldova Human Development Report chinafotokoza kuti mankhwala ochokera ku feteleza komanso tizilombo toyambitsa matenda zinali zitawononga “zitsime zopitirira theka la zitsime zonse za ku Moldova.” Komabe, m’zaka zaposachedwapa madzi a m’zitsime ayamba kukhala abwinoko chifukwa cha kuchepa kwa mafakitale ndi kuchepa kwa mankhwala ndi mafuta amene akulowa pansi kukawononga madzi a pansi panthaka.

Ngati mutadzapita ku Moldova, simudzachita kufunika kuthira madzi pamsewu kuti mupeze munthu wocheza naye. N’zotheka kuti winawake azikakuuzani nkhani zomwe zachitika tsikulo uku mukumwa madzi ozizira bwino. Chachikulu n’choti mudzakumane ndi winawake wa m’dzikoli wodziwa kuchereza alendo woti adzakuuzeni kuti mukakumane pachitsime.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 30, 31]

LUSO LAKALEKALE

Oleg ndi munthu wa ku Moldova amene amagwira ntchito yokhoma zidebe, ndipo wakhala akupanga zivundikiro za zitsime zokongoletsedwa bwino chimalizireni sukulu. Iye anati: “Kwa ine, ntchito yokhoma zidebe ndi yoyamwira. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, agogo anga anaphunzira luso lokhoma zidebe kwa Myuda wina wodziwa ntchito imeneyi amene ankakhala kudera kumene kunali Ayuda ambiri kunja kwa mudzi wawo wa Lipcani. Ayuda ambiri ataphedwa pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, anthu ochepa odziwa ntchito imeneyi amene anatsala sanali Ayuda. Panthawi imeneyi m’pamene bambo anga anaphunzira luso limeneli, ndipo iwowo ndi amene anandiphunzitsa ineyo.”

Akamajambula maluwa amene amakongoletsera zivundikiro za zitsime, Oleg amagwiritsa ntchito zida zosavuta kupanga ndiponso zidindo zochepa chabe. Kwinako amangotsatira luso la manja ake ndi mmene anthu akhala akujambulira kudera limeneli kuyambira kalekale. Anthu a kudera kwawo amayamikira kwambiri ntchito imene Oleg amagwira. Iye anati: “Nthawi zambiri makasitomala anga amanenerera mitengo ya zinthu zambiri zimene ndimapanga, koma ndikawapangira chivundikiro cha chitsime, nthawi zambiri sanyinyirika kupereka ndalama zimene ndawauza kuti apereke.”

[Mapu pamasamba 30, 31]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

UKRAINE

MOLDOVA

ROMANIA

Nyanja Yakuda