Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chakudya Chikatha

Chakudya Chikatha

Chakudya Chikatha

M’MADERA ena a dziko lapansi, anthu okhala m’mizinda amangoganiza kuti akapita kukagula chakudya ku msika, akapeza chakudya chokwanira ndiponso chotsika mtengo. Chakudyacho chikakhalapo, anthu ogulawo saganizirako n’komwe zoti kodi chakudyacho chikuchokera kuti ndiponso chayenda bwanji kuti chidzafike kumeneko. Komabe chakudya chikayamba kusowa, anthu amayamba kuganizira za ntchito yomwe imakhalapo kuti chakudya chipezeke kumsika. Ngati chakudya chayamba kusowa pa chifukwa chinachake, nthawi zina pamakhala mavuto aakulu.

Taganizirani zomwe zinachitika m’dziko linalake kumpoto kwa Africa lomwe lili pa mavuto a zachuma. Boma litangosiya kuthandiza alimi, nthawi yomweyo mtengo wa buledi unakwera kuwirikiza kawiri. Poipidwa ndi zimenezi, anthu anakwiya n’kukhamukira m’misewu ndipo anaphwanya mawindo a masitolo ndiponso mabanki ndi mapositi ofesi. Zipolowe zinafalikira dziko lonselo ndipo boma linakhwimitsa chitetezo. Akuti anthu 120 anafa ndipo ambiri anavulala pamene apolisi okhazikitsa bata anawombera anthu okwiyawo.

Ngakhale m’mayiko amene chuma chikuyenda bwino chakudya chikhoza kusowa. Chitsanzo cha zimenezi ndi zomwe zinachitika ku Britain mu September, chaka cha 2000. Anthu amene ankachita zionetsero poipidwa ndi kukwera mtengo kwa mafuta anatseka njira zochokera ku mafakitale oyenga mafuta, pofuna kuti magalimoto onyamula mafuta asathe kutuluka. Patangotha masiku ochepa, mafuta anatha m’malo ogulitsira, magalimoto anasowa mafuta, ndipo panalibe woti anganyamule chakudya. M’dziko lonselo, chakudya chinatheratu m’masitolo amene amangodalira kuti katundu wawo akamatha wina akhala akufika.

Pali mavuto osiyanasiyana okhudzana ndi kanyamulidwe ka chakudya m’mayiko osauka. Chikalata chotchedwa Feeding the Cities, chofalitsidwa ndi bungwe la United Nations loona za zakudya lotchedwa Food and Agriculture Organization (FAO) chinati, pa zifukwa zosiyanasiyana, kuphatikizapo chilala, mavuto a zachuma, zipolowe, ndi nkhondo, “ntchito yonyamula zakudya imakhala yosalongosoka kapenanso sitheka kumene. Zimenezi zikachitika, ngakhale kuti zingakhudze dera lochepa ndiponso zingachitike nthawi yochepa chabe, anthu osauka ndi amene amavutika nazo kwambiri.”

Anthu ochita kafukufuku akukhulupirira kuti kuwonjezeka kwa anthu okhala m’tawuni kubweretsa “mavuto aakulu” kwa anthu amene amalima chakudya ndi amene amachipititsa m’tawuni. Akuti mwina pofika chaka cha 2007, anthu opitirira theka la anthu onse padziko lapansi azidzakhala m’mizinda. Malinga ndi bungwe la FAO, “kulima ndi kupititsa chakudya chabwino ndiponso chotsika mtengo kwa [anthu a m’tawuni] kudzakhala kovuta kwambiri, mwinanso kosatheka kumene.”

Kupititsa chakudya m’misika kuti anthu azitha kugula ndi nkhani yofunika kwambiri. Choncho, kodi njira zopezera chakudya n’zodalirika motani? N’chifukwa chiyani akatswiri akuda nkhawa kuti mwina posachedwapa zakudya zizivuta kwambiri kupeza? Ndipo kodi idzafika nthawi imene sipadzakhalanso munthu amene azidzada nkhawa kuti chakudya achipeza kuti?

[Chithunzi patsamba 19]

Kuphwanya sitolo chakudya chitasowa

[Mawu a Chithunzi]

BETAH/SIPA