Kodi Kusowa Pokhala Kungathe Bwanji?
Kodi Kusowa Pokhala Kungathe Bwanji?
“MUNTHU mukam’patsa nsomba, ndiye kuti mwamudyetsa kwa tsiku limenelo. Koma mukamuphunzitsa kuwedza yekha nsombazo, ndiye kuti mwamudyetsa kwa moyo wake wonse.” Mwambi umenewu umaphera mphongo mfundo yoti kuthandiza munthu pa vuto lokhalo lomwe ali nalo sikopindulitsa kwenikweni. Koma ndi bwino kuthandiza anthu kudziwa mmene angathetsere mavutowo ndi kudzithandiza okha. Anthu ambiri amafunika kuphunzira kudzisamalira kapenanso kusintha moyo wawo.
Mboni za Yehova sizikayika ngakhale pang’ono kuti njira yabwino kwambiri yothandizira anthu osowa malo okhala ndiyo kuphunzitsa anthu kukhala moyo wabwino kwambiri, kapena kuti kuwaphunzitsa kutsatira malangizo abwino kwambiri amene anaperekedwa ndi Mlengi wa anthu. Ndithu, palibe winanso amene angapereke malangizo oposa amenewa. Malangizo a Mlengi
wathuyu akuthandiza anthu kupewa mavuto ambiri amene amachititsa anthu kusowa pokhala. Akuthandizanso anthu oona mtima omwe ali pa vutoli, kuti alithetse. N’zoona kuti kuwerenga Baibulo pakokha sikungathetse mavuto athu onse. Komabe, Baibulo lingathandize anthu kusiya makhalidwe owonongetsa ndalama, kuyamba kudzipatsa ulemu, ndi kumakhala moyo wolemekezeka.Anthu ambiri anayamba kusowa malo okhala chifukwa cha kumwa mowa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, moyo wauchigawenga, mavuto a zachuma, kapena kutha kwa banja. Baibulo limapereka malangizo othandiza pa nkhani zonsezi. Anthu mamiliyoni ambiri athandizidwapo kale potsatira malangizo amenewa. Motero asintha moyo wawo, n’kusinthiratu umunthu wawo wonse, kuti ukhale wabwino kuposa kale. Inde, kungotsatira chabe malangizo a m’Malemba sikungathetse mavuto onse obwera ndi vuto la kusowa pokhala. Anthu amafuna kuthandizidwa m’njira zina zamsangamsanga akakhala pa mavuto monga masoka achilengedwe, matenda, umphawi, uchidakwa ndi zizolowezi zina zotere, ndiponso mavuto ena. Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amayesetsa zedi kuthandiza ovutikawa, iwo amadziwa kuti ndi Mlengi wathu yekha amene angathetseretu mavuto amenewa kwamuyaya. Koma kodi adzaterodi?
Kodi Cholinga cha Mulungu Chinali Chotani?
Pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti kusowa pokhala kudzatha. Kodi n’zotani? Taganizira mfundo iyi: Yehova Mulungu anapatsa mwamuna ndi mkazi woyamba malo abwino okhala. Mulungu anawaika anthuwa m’paradaiso, ndipo mmenemo munali zofuna zawo zonse. Akanamvera malangizo a Mlengi wawo, akanafutukula Paradaisoyo kuti afike padziko lonse. Ana awo akanadzakhala ndi zinthu zambiri komanso nyumba zabwino. Bwenzi anthu onse akudalirana ndi kukondana. Cholinga cha Mulungu chinali chimenechi ndipotu iye sanasinthe maganizo ake pankhaniyi.—Salmo 37:9-11, 29.
Komanso, zilizonse zimene Mulungu akufuna kuchita adzazikwaniritsa ndithu. (Yesaya 55:10, 11) Baibulo limalosera kuti kukubwera nthawi imene munthu aliyense adzakhale ndi nyumba yakeyake ndi katundu wochuluka. N’zoona kuti dzikoli liyenera kudzasintha kuti zimenezi zitheke ndipo Mulungu ndiye adzalisinthe polowerera pa zochita za anthu. Izi n’zimene Yesu ankatanthauza pamene anauza ophunzira ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.
Mu ulamuliro wachilungamo wa Ufumu wa Mulungu, anthu okhulupirika adzaona kukwaniritsidwa kwa ulosi wolimbikitsa wakuti: “Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo . . . Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya . . . osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja awo.” (Yesaya 65:21, 22) Mwachidule, tingoti sipadzakhalanso munthu wosowa pokhala.
A Mboni za Yehova akuyesetsa kuthandiza anthu mwauzimu masiku ano. Cholinga chawo n’choti achitire ena zabwino mogwirizana ndi mawu a Yesu. (Mateyu 22:36-39) Mtima woganizira enawu umawachititsanso kuthandiza anthu amene akusowa pokhala chifukwa cha masoka achilengedwe. *
A Mboni amadziwa kuti n’zosatheka kuthandiza munthu aliyense. Jacek, wa ku Poland uja, akukhala pa malo a anthu osowa pokhala ndipo pankhaniyi iye anati: “Ena mwa anthu osowa pokhalawa amavutitsa anzawo kapena amagwiritsira ntchito mankhwala osokoneza
bongo. Ena amadana ndi nkhani zachipembedzo, chifukwa choganiza kuti Mulungu sawaganizira. Koma pali ena amene amamvetsera akamauzidwa Mawu a Mulungu.” Chitsanzo chake ndi Jacek yemweyo. Iye wayamba kuphunzira kuti adziwe zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni.Munthu winanso wosowa malo okhala amene wamvetsera Mawu a Mulungu ndi Roman, amene akudwala matenda a Edzi ndipo ankakhala mumsewu mpaka posachedwapa. Iye anati: “N’tafika pa malo a bungwe losamalira anthu ovutika, sindinadziwe kuti Mboni za Yehova zinkakumana chapafupi pompo. Posakhalitsa a Mboni anayamba kucheza nane mumsewu ndipo anandilongosolera kuti Mulungu sanyalanyaza anthu osowa pokhala akamamufuulira pofuna thandizo. Iwo anandiitaniranso ku misonkhano yawo.”—Salmo 72:12, 13.
Kodi zimene anamvazo zinam’khudza bwanji? “Ndinaphunzira kuti ndingathe kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi ndi kuti ndine wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu. Pakuti ndinapeza anzanga ondikonda, ndinasiya kuganizira kwambiri za vuto langalo n’kuyamba kusintha umunthu wanga. Chifukwa chokonda Mulungu, ndinasiya kusuta fodya ndipo ndinapemphera n’kumulonjeza Mulungu kuti ndiyamba kuchita zinthu zolungama.”
Roman anapita patsogolo mwauzimu ndipo posakhalitsa anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. A Mboni anzake komanso aboma anamuthandiza kupeza nyumba yabwino. Panopo Roman akunena mosangalala kuti: “Mumtima mwanga muli chimwemwe chosaneneka. Ndayandikira kwa Mulungu wachikondi, amene wachititsa kuti moyo wanga ukhalenso n’cholinga. Wandipatsa banja labwino la abale ndi alongo ndiponso wandipatsa nyumba.”
Tsogolo la Anthu Osowa Pokhala
Mboni za Yehova zimayesetsa kuchitira chifundo anansi awo onse, kuphatikizapo anthu osowa pokhala. Izo zimafuna kuuza anthu choonadi cha m’Baibulo chokhudza tsogolo labwino, ndipo ngakhale panopo choonadi chimenechi chingathe kusintha moyo wa anthu.—Yohane 8:32.
Baibulo limanena kuti: “Chokhotakhota sichingawongokenso.” (Mlaliki 1:15) Inde, ngakhale kuti anthu odzipereka kugwira ntchito zinazake ndiponso aboma amakhala ndi zolinga zabwino, m’povuta kuthetsa mavuto monga kusowa pokhala ndiponso umphawi, omwe azika mizu zedi pakati pa anthu. Komabe, Baibulo limatitsimikizira kuti posachedwapa, mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, anthu onse omvera adzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Zitsanzo zake mungazipeze mu Galamukani ya January 8, 1993, tsamba 13 mpaka 20, ndi ya August 8, 2003, tsamba 10 mpaka 15.
[Chithunzi patsamba 8]
Mayi wothawa nkhondo wa ku Somalia atatenga tikiti yolandirira chakudya
[Mawu a Chithunzi]
© Trygve Bolstad/Panos Pictures
[Chithunzi patsamba 9]
Chinthu chimene osowa pokhala amafuna kwambiri n’chiyembekezo choti zabwino zili m’tsogolo
[Chithunzi patsamba 10]
Mu Ufumu wa Mulungu simudzakhala munthu wosowa pokhala