Kodi Mulungu Amakondera Mitundu ina ya Anthu?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Mulungu Amakondera Mitundu ina ya Anthu?
ANTHU ambiri amaganiza kuti Mulungu amakondera mtundu wawo. Koma kodi akafunsidwa amanena zifukwa zotani? Ena amatchula zinthu zonyaditsa zimene mtundu wawo wachitapo, monga kuwina nkhondo kapena kuyendetsa bwino chuma. Mwina angatchuleponso zinthu monga kupatsa chakudya kwa osowa, kuteteza amphawi, kapena kupititsa patsogolo zachilungamo. Ena amaona kuti Mulungu amakonda dziko lawo chifukwa choti n’lokongola.
M’mayiko onse anthu amanyadira mtundu wawo. Koma kodi Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amakonderadi mtundu winawake kuposa wina?
Khalidwe Lofunika la Mulungu
Yankho la funso limeneli n’losavuta ngati titamvetsa khalidwe lofunika la Mulungu Wamphamvuyonse, limene Baibulo limagogomezera kwambiri. Mulungu alibe tsankhu. Mwachitsanzo, lemba la Machitidwe 10:34 limanena momveka bwino kuti: “Mulungu alibe tsankhu.” Baibulo limanenanso kuti Yehova Mulungu ndi “wosasamalira nkhope za anthu,” kapena kuti sayang’ana nkhope ndipo limanenanso kuti “palibe chosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu.” (Deuteronomo 10:17; 2 Mbiri 19:7) Mulungu amadana ndi tsankhu; moti mpaka salisiyanitsa ndi kuchita zosalungama.
Koma mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi Mulungu sanakondere mtundu wa Israyeli poyerekezera ndi mitundu ina? Kodi zimenezi sizinkasonyeza tsankhu?’ N’zoona kuti m’nthawi za Baibulo Mulungu ankaona mtundu wa Israyeli ngati wapadera ndipo ankakhala ku mbali yawo pa nthawi zina zimene mtunduwo unkachita nkhondo ndi mitundu ina. Komanso Baibulo limanena kuti Mulungu “aonetsa mawu ake kwa Yakobo; Malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israyeli. Sanatero nawo anthu a mtundu wina.” (Salmo 147:19, 20) Kodi zimene Mulungu anachita nawo mtundu wa Israyeli zimasonyeza kuti iye ndi watsankhu? Ayi ndithu. Tiyeni tionepo zifukwa zitatu zotsimikizira zimenezi.
Choyamba n’chakuti Mulungu anasankha mtundu wa Israyeliwo n’cholinga choti mitundu yonse ipindule. Iye anachita pangano ndi tate wa mtunduwo, Abrahamu, ponena kuti: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:17, 18) Inde, cholinga cha Mulungu pochita zinthu ndi mtundu wa Israyeli chinali choti utulutse “mbewu” imene idzabweretse madalitso ambiri, osati kwa anthu amtundu umodzi wokha koma kwa “mitundu yonse ya dziko lapansi.”
Chifukwa chachiwiri n’chakuti madalitso a Mulungu sankapita kwa anthu amtundu wa Israyeli wokha ayi. Mopanda tsankhu iye anatheketsa kuti anthu a mitundu ina azimulambira limodzi ndi anthu ake osankhidwa. (2 Mbiri 6:32, 33) Anthu ambiri anavomereza zimenezi ndipo anadalitsidwa. Rute, yemwe anali Mkazi wachimoabu ndi chitsanzo chimodzi cha anthu otere.—Rute 1:3, 16.
Chifukwa chachitatu n’chakuti ubwenzi wapadera umene Mulungu anali nawo ndi mtundu wa Israyeli unali wa kanthawi chabe. M’chaka cha 29 C.E., mtundu wa Israyeli unatulutsa “mbewu” imene inalonjezedwa, yomwe ndi Mesiya, Yesu Kristu. (Agalatiya 3:16) Koma anthu amtundu wa Yesuwo anam’kana Yesu kuti si Mesiya. Ndipo iye anawauza kuti: “Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” (Mateyu 23:38) Kuchoka panthawiyi mpaka pano, pochita zinthu ndi anthu, Mulungu salowererapo pa zochitika za mayiko osiyanasiyana ndiponso nkhondo zawo. M’malo mwake, iye mopanda tsankhu, wakhala akupereka madalitso kwa anthu onse. Tiyeni tionepo zitsanzo zina.
Mphatso za Mulungu kwa Anthu Onse
Nsembe ya dipo ya Yesu Kristu ndi mphatso yaikulu kwambiri imene Mulungu anapereka kwa anthu. (Aroma 6:23) Mphatso imeneyi yatipatsa njira yomasuka ku uchimo ndi imfa kuti tonsefe tikhale ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Inaperekedwa kwa “anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse.” (Chivumbulutso 5:9) Inde, Mulungu amafuna kuti “yense wakukhulupirira [Yesu] asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umabweretsa madalitso ambiri kwa anthu amene amaumvera. (Chivumbulutso 14:6, 7) Umapereka chiyembekezo ndiponso nzeru zothandiza munthu kukhala wosangalala ngakhale panopo. Mopanda tsankhu, Yehova anakonza zoti ‘uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwe padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Machitidwe 16:10.) Uthenga wabwino umenewo uli m’Baibulo, buku lomwe linamasuliridwa lonse kapena mbali zake zina m’zinenero 2,300. Monga Tate wachikondi, Yehova watheketsa kuti pafupifupi munthu aliyense padziko lapansi athe kumva “mawu a moyo wosatha.”—Yohane 6:68; Yoswa 1:8.
Mphatso imeneyi pamodzinso ndi mphatso zina zochokera kwa Mulungu n’zoti aliyense angathe kulandira, zilibe kanthu kuti ndi wa mtundu wanji, fuko lanji, ndiponso chinenero chanji. Inde, kukondedwa ndi Mulungu sikudalira malo amene tinabadwira kapena fuko lathu ayi.
Kodi Mulungu Amakonda Anthu Otani?
Nangano tiyenera kutani kuti Mulungu azitikonda? Mtumwi Petro anayankha motere: “M’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) N’zoonekeratu kuti kungochita chidwi ndi Mulungu sikokwanira ayi. Tiyenera kuyamba kum’konda Mulungu mochoka pansi pamtima, n’kumaopa kumukhumudwitsa. Tiyeneranso ‘kuchita chilungamo,’ kapena kuti kuyesetsa kuchita zoyenera pamaso pa Mulungu.
Mwachitsanzo, m’mayiko ambiri muli sukulu zimene aliyense angathe kulowa, koma anthu amene amapindula ndi sukuluzi ndi okhawo amene amakalowa m’kalasi n’kuchitadi khama. N’chimodzimodzinso ndi kukondedwa ndi Mulungu. Aliyense angathe kukondedwa ndi Mulungu, koma m’pofunika khama. Khama lotereli lingaphatikizepo zinthu monga kuwerenga Baibulo nthawi zonse, kukhulupirira nsembe ya dipo ya Kristu, ndi kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu. ‘Tikamufunadi’ Yehova, iye angayambe kutikonda.—Salmo 105:3, 4; Miyambo 2:2-9.
[Chithunzi patsamba 15]
Mulungu watheketsa kuti anthu a mitundu yonse amve “mawu a moyo wosatha”