Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Njala Idzatha Padziko Pano?

Kodi Njala Idzatha Padziko Pano?

Kodi Njala Idzatha Padziko Pano?

TANGOGANIZIRANI mmene bambo wokonda ana ake amamvera akamaona anawo akuzunzika chifukwa cha kuperewera kwa zakudya m’thupi. Zimamupweteka kwambiri mu mtima. Ngati munthu amamva choncho, taganizirani mmene Atate wathu wakumwamba wachikondi amamvera. Iye akudziwa bwino mmene anthu mamiliyoni ambiri akuzunzikira chifukwa cha vuto limeneli.

Ngakhale kuti anthu ayesetsa kupezera chakudya anthu anzawo, kumayambiriro kwa zaka za m’ma 2000 zino njala ikumka iwonjezeka. Komabe, Atate wathu wakumwamba, Yehova, angathe kuchitapo kanthu kuti athetseretu njala kwamuyaya, ndipo adzaterodi. Tikudziwa bwanji zimenezi?

Baibulo limafotokoza kuti Mulungu ataika Adamu ndi Hava m’munda wa Edene, anawapatsa zonse zomwe ankafunikira kuti akhale otetezeka, okhutira, ndiponso kuti akhale ndi zakudya zokwanira. Mulungu anawauza kuti: “Ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbewu lili pa dziko lapansi.” Cholinga cha Yehova chinali choti ana a Adamu ndi Hava ‘adzaze dziko lapansi’ ndi kuti anthu onse akhale ndi zakudya za mwana alirenji.—Genesis 1:28, 29.

Ngakhale kuti mwamuna ndi mkazi woyambawo anapandukira Mlengi wawo moti anasiya kuwadalitsa, cholinga choyambirira cha Mulungu polenga anthu sichinasinthe. Baibulo limati Yehova “ndiye wakupatsa anjala chakudya,” ndipo lili ndi maulosi ambirimbiri osonyeza kuti adzathetseratu mavuto onse amene amachititsa kuti chakudya chizisowa.—Salmo 146:7.

Ophunzira a Yesu atamufunsa Yesu kuti awapatse chizindikiro, kapena umboni, wosonyeza nthawi yomwe adzakhazikitse Ufumu wake n’kulowererapo pa zochitika za padziko lapansi, Yesu anatchula zinthu zimene zidzachitike iye asanachite zimenezi. Chimodzi mwa zinthu zimenezo ndi “njala.” Kufufuza bwinobwino mawu a Yesu kumatilimbitsa mtima kuti mavuto a anthu atha posachedwapa. *Mateyu, chaputala 24.

Ponena za Paradaiso amene Mulungu adzakhazikitse, lemba la Salmo 72:16 limati: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu [kapena kuti, mbewu] dzochuluka pamwamba pa mapiri.” Kalelo ku Israyeli, mbewu zinkamera makamaka m’zidikha. Koma panthawi ya madalitso ochuluka imene ikufotokozedwa mu ulosi umenewu, mbewu zodzalidwa ngakhale m’malo ouma opandiratu chonde, amene nthawi zambiri sabala kanthu kalikonse, zidzabala zinthu zochuluka kwambiri. Katswiri wina wa Baibulo anati: “Mu ulamuliro wa Mesiya, zidzakhala ngati kuti mbewu zili waa paliponse, ngakhale pamwamba pa mapiri, kapena ngati kuti mapiri alimidwa mpaka pamwamba penipeni, motero dziko lonselo langoti waa ndi mbewu zooneka bwino.”

Tsogolo limene Baibulo likulonjeza n’losiyanadi kwambiri ndi mmene moyo wa anthu ambiri ulili masiku ano. Zoonadi, panthawi ya m’tsogolo imene Mulungu akulonjeza, “dziko lapansi [lidzapereka] zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.”—Salmo 67:6.

Ngati mukufuna kudziwa zomwe inuyo ndi okondedwa anu muyenera kuchita kuti mudzalandire nawo madalitso amenewa ndi enanso amene akufotokozedwa m’maulosi osangalatsa a m’Baibulo, musazengereze, funsani a Mboni za Yehova kwanuko kapena lemberani ku adiresi yoyenera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.

[Mawu a m’munsi]

^ ndime 6 Kuti muone momwe ulosi wa Yesu wakwaniritsidwira, onani mutu 11 m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi chachikulu patsamba 26]