Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusowa Pokhala Ndi Vuto la Padziko Lonse

Kusowa Pokhala Ndi Vuto la Padziko Lonse

Kusowa Pokhala Ndi Vuto la Padziko Lonse

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU POLAND

“ZIDAKWA zonunkha litsiro, zopanda katundu aliyense, zopanda dzina, tingoti zopanda chilichonse!” Awa ndi mawu okokomeza kwambiri. Komatu umu ndi mmene anthu ambiri amaonera anthu osowa pokhala, malingana ndi zimene ananena anthu odzipereka pantchito yothandiza anthu otere ku Czestochowa, ku Poland.

Zaka zingapo zapitazo, magazini ya The Economist inati ku Mongolia, ana ambiri a mumzinda wa Ulaanbaatar ankakhala pansi pa nthaka m’zimapaipi zonunkha mmene mumadutsa zonyansa. Magaziniyo inati anthu ambiri a ku Mongolia anakhudzidwa kwambiri atamva za anawa, koma ambiri ankangoti chinachititsa vutoli “ndicho ulesi wa makolo amene analephera kusamalira anawo.”

M’mayiko ena, ana okhala m’misewu amaphedwa ndi magulu achiwembu omwe amati kupha ana otere n’kuyeretsa mzinda. Bungwe la United Nations linati ichi n’chifukwa choti “ku Latin America anthu ambiri a zamalamulo, apolisi, ofalitsa nkhani, a zamalonda, ndiponso anthu ena osiyanasiyana amakhulupirira kuti ana okhala m’misewu amasokoneza khalidwe la anthu.” Bungweli linatinso: “Tsiku lililonse ku Rio de Janeiro, timamva zoti pafupifupi ana atatu amaphedwa.”

Anthu opanda pokhala “timawaopa . . . , komatu iwowa ndi anthu ngati ife tomwe, ndipo nawonso amamva njala. Pali anthu ambiri otere ndipo ndi anthu ovutikadi zenizeni.” Inatero nkhani ina ya pa Intaneti yolembedwa ndi anthu odzipereka pantchito yothandiza osowa pokhala ku Czestochowa. Nkhaniyo inatinso: “Zingakhale bwino ngati . . . patapezeka anthu oti athandize ovutikawa.” Kodi vuto la anthuwa n’chiyani makamaka, ndipo kodi n’lalikulu motani?

[Chithunzi pamasamba 2, 3]

Ana osowa pokhala amene amakhala pansi pa chidzenje ichi

[Mawu a Chithunzi]

Jacob Ehrbahn/Morgenavisen Jyllands-Posten