Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sayansi ndi Baibulo Zinandithandiza Kudziwa Cholinga cha Moyo

Sayansi ndi Baibulo Zinandithandiza Kudziwa Cholinga cha Moyo

Sayansi ndi Baibulo Zinandithandiza Kudziwa Cholinga cha Moyo

YOSIMBIDWA NDI BERND OELSCHLÄGEL

Ndinatha zaka 20 ndikufufuza cholinga cha moyo. Zinthu ziwiri zinandithandiza kuchipeza. Zinthu zake ndi sayansi ndi Baibulo. Maphunziro anga a sayansi ananditsimikizira kuti moyo uyenera kukhala n’cholinga. Koma Baibulo linandisonyeza cholinga chimenecho n’kundithandiza kuchimvetsa.

MWINA munamvapo anthu ena akunena kuti sayansi imatsutsana ndi Baibulo. Ine ndaphunzira zinthu ziwiri zonsezi, ndipo sindikuvomerezana nawo. Mwina mukufuna kudziwa chifukwa chake.

Ndinabadwa mu 1962 mu mzinda wa Stuttgart, kum’mwera kwa dziko la Germany. Bambo anga ankagwira ntchito yopanga makina, ndipo iwo ndi mayi anga anali olimbikira kwambiri ku tchalitchi. Mchemwali wanga wamkulu Karin, ndinasiyana naye zaka zinayi. Chinthu chimodzi chosangalatsa chomwe chinandichitikira ndili mwana ndi pamene bambo anga anandipatsa zipangizo zimene ana amaphunzirira sayansi. Ndinasangalala kwambiri kuchita zinthu zosiyanasiyana zasayansi. Ndinkakonda kuphunzira zinthu zatsopano.

Kenaka ndinasiya kuseweretsa zipangizo za sayansi zija n’kuyamba kugwiritsa ntchito kompyuta. Ngakhale ndili mnyamata wamng’ono, ndinkatha kuona kuti kompyuta yabwino kwambiri ndi ubongo. Koma ndinkadzifunsa kuti: ‘Kodi ubongo unachokera kuti? Ndani anatipatsa ubongowu? Ndipo kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’

Kuphunzira ku Yunivesite

Ndinasiya sukulu ndili ndi zaka 16 n’kuyamba kuphunzira ntchito kumalo otsukira zithunzi. Popeza ndinkasangalala kwambiri kuphunzira zinthu, cholinga changa chinali choti ndidzaphunzire sayansi ya kapangidwe ka zinthu ku yunivesite. Koma panapita nthawi zimenezo zisanatheke. Zinanditengera zaka zisanu kuti ndikwanitse chabe zofunikira kuti nditengedwe ku yunivesite. Ndinayamba maphunziro anga a ku yunivesite ku Stuttgart mu 1983, ndipo ndinakapitiriza ku Munich. Kenaka ndinatenga digiri ya udokotala wa sayansi ya kapangidwe ka zinthu pa yunivesite ya Augsburg mu 1993.

Masiku anga oyambirira ku yunivesite anali ovuta. M’chipinda chophunzirira munkakhala modzaza tho ndi ophunzira pafupifupi 250, ndipo ambiri a iwo anasiya maphunziro awo patangotha miyezi yochepa. Ine ndinayesetsa kuti ndisasiye, ndipo ndinkafunitsitsa kukwanitsa cholinga changa. Popeza ndinkagonera ku yunivesite komweko, ndinkakhalira limodzi ndi anthu ambiri omwe ankaoneka kuti ankangofuna kusangalala basi. Kucheza ndi anthu oterowo kunandibweretsera mavuto. Ndinayamba kumapita ku mapwando a anthu otayirira ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Kufufuza Kwanga Kunandifikitsa ku India

Maphunziro anga a sayansi ya kapangidwe ka zinthu anandithandiza kumvetsetsa bwino malamulo amene zinthu zimayendera m’chilengedwe. Ndinkaganiza kuti sayansi idzatha kundisonyeza kuti cholinga cha moyo n’chiyani. Komabe, pofufuza cholinga cha moyo sindinadalire sayansi yokha. Mu 1991, ndinapita ku India ndi anthu ena kukaphunzira kusinkhasinkha kwa zipembedzo za amwenye. Zinali zochititsa chidwi kwambiri kuona dzikolo ndi anthu ake. Koma ndinaipidwa kwambiri kuona kusiyana kwakukulu komwe kunalipo pakati pa olemera ndi osauka.

Mwachitsanzo, kufupi ndi mzinda wa Pune tinakumana ndi mphunzitsi wina wachipembedzo amene ankanena kuti ngati munthu ataphunzira kusinkhasinkha m’njira yoyenerera, akhoza kulemera. M’mawa uliwonse tonse tinkasinkhasinkhira limodzi. Mphunzitsiyo ankagulitsanso mankhwala pamtengo wokwera kwambiri. Zinali zachidziwikire kuti ankapeza ndalama zambiri poona moyo umene ankakhala. Tinaonanso ansembe amene ankaoneka kuti anali paumphawi, mosiyana ndi mphunzitsiyo. Ndinadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani iwowa sanalemere nako kusinkhasinkhako?’ Ulendo wanga wa ku India unangondibweretseranso mafunso ena ambiri.

Chimodzi mwa zinthu zimene ndinagula ku India linali belu lothandiza posinkhasinkha. Anandiuza kuti belulo ndikalimenya moyenerera liziimba kanyimbo kamene kangandithandize kusinkhasinkha moyenerera. Nditabwerera ku Germany, ndinagula chipepala chomwe chinalembedwa ndi munthu wina amene ankanena kuti angathe kudziwa tsogolo langa. Koma kusinkhasinkha sikunandisonyeze chilichonse chatsopano chokhudza moyo. Ndinazindikiranso kuti chipepala ndinagula chija chilibe phindu lililonse. Choncho mafunso anga okhudza cholinga cha moyo anapitirirabe.

Ndinapeza Mayankho M’Baibulo

Moyo wanga unasintha mwadzidzidzi mu 1993. Ndinali kumaliza maphunziro ndi kafukufuku wanga ndipo ndinali m’kati molemba lipoti lopezera digiri yapamwamba ya mbali inayake ya sayansi ya kapangidwe ka zinthu. Kuti ndithe kugwira nthawi imene ndinapatsidwa, ndinkachita zimenezi usana ndi usiku, ndipo ndinaimika kaye zina zonse. Kenaka mwadzidzidzi tsiku lina masana ndinamva kugogoda pakhomo. Ndinatsegula n’kupezapo azimayi awiri.

Azimayiwo anandifunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti chaka cha 1914 chinali chaka chapadera kwambiri malinga ndi zimene Baibulo limanena?” Funsolo linandiimitsa mutu. Ndinali ndisanamvepo zimenezo, ndiponso ndinalibe nthawi yofufuzira yankho lake. Komabe, linandichititsa chidwi. Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi anthu amenewa angadziwe bwanji kuti kalekale Baibulo linaneneratu kuti chaka cha 1914 n’chapadera?’

“Kodi mungafune kudziwa zambiri?” anapitiriza choncho. Ndinaganiza kuti, ‘Ndikudziwa kuti ndikamvetsera zomwe anene, ndiona kuti akudzitsutsa.’ M’malo moona kuti akudzitsutsa, ndinapeza umboni wogwira mtima wosonyeza kuti Baibulo n’lodalirika. Ndinaphunzira kuti ulosi wa m’Baibulo umafotokoza momveka bwino kuti Ufumu wa Mesiya wa Mulungu, womwe ndi boma lakumwamba lomwe m’tsogolo muno lizidzalamulira padziko lonse lapansi, unakhazikitsidwa mu 1914. *

Azimayiwo anali a Mboni za Yehova, ndipo anandipatsa buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. * Ndinamaliza kuliwerenga patatha masiku ochepa chabe, ndipo ndinapeza kuti zonse zomwe linkanena zinali zomveka. A Mboniwo anandisonyeza kuchokera m’Baibulo kuti n’cholinga cha Yehova kuti anthu onse adzakhale ndi moyo kosatha m’paradaiso pa dziko lapansi. Malinga ndi ulosi wa m’Baibulo, lonjezo limeneli likwaniritsidwa posachedwa. Chimenechi n’chiyembekezodi chabwino kwambiri cha m’tsogolo. Chiyembekezo chimenechi chinandikhudza mtima kwambiri mpaka ndinagwetsa misozi. Kodi n’kutheka kuti zimenezi n’zimene ndinakhala ndikufufuza kwa zaka 20?

Mwamsanga ndinazindikira cholinga changa m’moyo. Cholinga chake chinali choti ndimudziwe Yehova Mulungu ndi kumutumikira ndi mtima wonse. Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo ndinkaona kuti zomwe ndinali kuphunzira zinali zoonadi. Ndinkafunitsitsa kwambiri kuphunzira zinthu zauzimu. M’miyezi itatu yokha, ndinawerenga theka la Baibulo uku ndikumaliza kulemba lipoti langa lopezera digiri yapamwamba ija.

Ndinapeza Zambiri, Osati Mayankho Okha

Mu May 1993, ndinapita ku msonkhano wa Mboni za Yehova koyamba, ku Nyumba ya Ufumu ya kwathu ku Augsburg. Zinthu zomwe ankaphunzitsa kumeneko zinkamveka zoona. Kuwonjezera apo, ndinaona kuti ndinali womasuka pakati pa anthu a Mboni. Anandipatsa moni mwansangala n’kundichititsa kumva kuti ndalandiridwadi, ngakhale kuti ndinali mlendo. Mzimayi wina wachikulire anakhala pafupi nane ndiponso anandipezera buku la nyimbo. Pa milungu ingapo yotsatira, mwamuna wina wa Mboni ndi mwana wake wamwamuna wamng’ono ankanditenga pagalimoto yawo popita ku Nyumba ya Ufumu. Anzanga atsopanowa posakhalitsa anayamba kumandiitana ku nyumba zawo. Patapita nthawi ndinayamba kulakalaka kuuza ena zinthu zimene ndinali kuphunzira zokhudza cholinga cha moyo.

Ndinali nditayamba kale kusintha moyo wanga potsatira zinthu zomwe ndinaphunzira m’Baibulo. Mwachitsanzo, sindinkafunanso kusunga zinthu zokhudzana ndi mizimu. Choncho ndinataya chipepala ndinagula chija ndi belu lothandiza kusinkhasinkha lija, ndi zinthu zina zachipembedzo zomwe ndinabweretsa kuchokera ku India. Phunziro langa la Baibulo linapita patsogolo, ndipo ndinadzipereka kwa Yehova Mulungu. Ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova mu June 1994, ku Munich. Potero, ndinasonyeza ndi mtima wonse kuti ndikuvomereza kuti ndapeza cholinga cha moyo.

Mu September 1995, ndinakhala mpainiya wokhazikika, kapena kuti mtumiki wa nthawi zonse wa Mboni za Yehova. Motero nthawi zambiri ndinkakhala ndikulankhula ndi anthu za zolinga za Mulungu. Kuti ndithe kuchita zimenezi, ndinadalira mphamvu imene Yehova amapereka. Nthawi zambiri ndinkafika kunyumba madzulo n’tatha maola angapo ndikuchita utumiki, ndipo ndinkakhala wachimwemwe ndiponso wokhutira m’njira imene ndinali ndisanakhalepo n’sanadziwe Yehova. Mu January 1997, ndinaitanidwa kuti ndikapitirize utumiki wanga wa nthawi zonse ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Germany ku Selters, yomwe imatchedwa Beteli. Kumeneku n’kumene ndikukhala tsopano. Makolo anga abwerapo nthawi zingapo kudzandiona, ndipo ngakhale kuti ali ndi zikhulupiriro zosiyana ndi zanga, anayamba kulemekeza Beteli ndipo ndi osangalala kuti ndili kunoko.

Sayansi ndi Baibulo

Anthu ena angadabwe kuti zingatheke bwanji munthu amene watha zaka zambiri akuphunzira sayansi kukhulupirira zimene Baibulo limanena. Zoona zake n’zoti, sindiona kutsutsana kulikonse pakati pa sayansi ndi Baibulo. Monga katswiri wa sayansi ya kapangidwe ka zinthu, ndaphunzira malamulo amene zinthu zamoyo zimayendera, ndipo malamulo amenewa amasonyeza kuti anakhazikitsidwa ndi winawake wanzeru zoposa za anthu.

Mwachitsanzo, pa sayansi ya kapangidwe ka zinthu ndi sayansi ya zinthu zamoyo pali mfundo zambirimbiri. Ndipo ngakhale kuti mfundo zimenezi zikhoza kukhala zosavuta kuzimvetsa, nthawi zina masamu ofotokozera mfundozi amavuta kwambiri kuwamvetsa. Mfundozi amaziyambitsa ndi asayansi anzeru kwambiri ndipo amapatsidwa mphoto inayake yapamwamba kwambiri chifukwa cha ntchito yawo. Ndiyeno tangoganizirani kuti amene anakonza ndi kupanga chilengedwe, chimene asayansi amavutika kuchimvetsachi, ndi wanzeru zambiri bwanji?

Kunena kuti moyo unangoyambika mwangozi, ngati mmene amanenera asayansi ena, n’kuganiza moperewera. Mwachitsanzo: Taikani mipira khumi mondondozana pa bwalo losewerera mpira, ndipo mpira uliwonse utalikirane mita imodzi ndi unzake ndipo mipirayo ikhale mumzere wowongoka. Ndiyeno menyani mpira woyamba kuti ugunde mpira wotsatizana nawo, n’cholinga choti mipira yonseyo igundane motsatizanatsatizana mpaka kufika pa mpira womalizira. Kuwonjezera apo, yesani kudziwa malo amene mpira uliwonse uime pomaliza. Zimenezi n’zovuta kwambiri kuzichita moti anthu ambiri angaone kuti n’zosatheka.

Ngati zimenezi zili zovuta choncho, kodi munthu anganene bwanji kuti maselo a m’thupi la munthu anachita kusintha kuchokera ku zinthu zopanda moyo mwangozi basi? Kuti zimenezo zichitike, pangafunike kuchitika zinthu zovuta kwambiri poyerekezera ndi kugundanitsa mipira kuja. Motero n’zomveka kuti winawake wa nzeru zozama kwambiri kuposa za anthu ndiye analenga anthu ndi zamoyo zonse padziko lapansi. Kodi winawake ameneyu, amene ali Mlengi, angachite zimenezi popanda cholinga chilichonse? Ayi. Ayenera kuti anali n’cholinga, ndipo cholinga chimenecho chinafotokozedwa momveka bwino m’Baibulo.

Monga momwe mwaonera, sayansi ndi Baibulo zinandithandiza kupeza mayankho a mafunso amene ndinakhala nawo kwa nthawi yaitali okhudza moyo. Tangoyerekezerani mpumulo ndi chisangalalo chimene mungakhale nacho mutapeza chinthu chimene mwakhala mukuchifunafuna kwa zaka 20. Cholinga changa n’choti ndithandize anthu ambiri kupeza chinthu chomwe ineyo ndinavutikira kupeza. Sikuti ndinangopeza mayankho a mafunso amene ndinali nawo, koma ndinadziwanso njira yoyenera yolambirira Mulungu woona yekha, Yehova, chomwe chili chinthu chofunika koposa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Kuti mumve zambiri, onani mutu 10 wakuti “Ufumu wa Mulungu Ulamulira” m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, tsamba 90 mpaka 97.

^ ndime 18 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, koma tsopano anasiya kulisindikiza.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

Monga katswiri wa sayansi ya kapangidwe ka zinthu, ndaphunzira malamulo amene zinthu zamoyo zimayendera, ndipo malamulo amenewa amasonyeza kuti anakhazikitsidwa ndi winawake wanzeru zoposa za anthu

[Chithunzi patsamba 28]

Ndili ndi zaka 12

[Chithunzi patsamba 29]

Pofunafuna cholinga cha moyo, ndinayamba kuphunzira kusinkhasinkha kwa zipembedzo za amwenye

[Chithunzi patsamba 31]

Chifukwa cholalikira anthu ena, ndili ndi chimwemwe chenicheni ndiponso ndine wokhutira

[Mawu a Chithunzi]

Cover of book: J. Hester and P. Scowen (AZ State Univ.), NASA