Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Basi Adutsa!

Basi Adutsa!

Basi Adutsa!

INALI nyengo ya phukuto, mdima utatsala pang’ono kugwa, ndipo kunja kunali kukuzizirira. Posapita nthawi, bata lomwe linalipo linatha ndi kulira kwa atsekwe. Mwadzidzidzi, ndinawaona akundidutsa pamutu. Analipo pafupifupi 20, atafola ngati chilembo chachikulu cha V ndipo anayamba kuuluka mochititsa kaso kwambiri, uku akukupiza mapiko mwamphamvu. Mochititsa chidwi kwambiri, tsekwe wina anapendekekera kumanzere n’kupita kumbuyo kwa atsekwe anzake. Ndinachita chidwi kwambiri ndi zomwe ndinaonazo. N’chifukwa chiyani atsekwe akamauluka amafola ngati chilembo cha V. Ndipo akupita kuti?

Atsekwe ndi mbalame za kumadzi, ndipo sasiyana kwenikweni ndi abakha ndiponso zinsansa. Padziko lonse pali mitundu pafupifupi 40 ya atsekwe, ndipo amapezeka kawirikawiri ku Asia, Ulaya, ndi ku North America. Mwa mitundu yodziwika kwambiri ya atsekwe pali atsekwe a ku Canada, amene amakhala ndi khosi lalitali lakuda ndi banga loyera chakumutu. Atsekwe aamuna amtundu wina wa ku Canada komweko, akakula kuti afikapo amatha kulemera mwina makilogalamu 8 ndiponso akatambasula mapiko awo amatha kutalika mamita awiri. M’chilimwe, atsekwe amtunduwu amakhala kumpoto kwenikweni kwa Alaska komanso kumpoto kwa dziko la Canada, ndipo kenako amasamukira kum’mwera kwa dziko la Mexico m’nyengo yozizira.

Atsekwe amafunika kudziwa bwino nthawi yosamukayi. Ngati atafulumira kufika kumpoto, madzi amakhala adakali oundana ndipo chakudya chimakhala chochepa kwambiri. Motero atsekwe a ku Canada akamasamukira kumpoto amakonda kuyendera limodzi ndi kusintha kwa nyengo. Akafika komwe akupita, atsekwewa amagawana awiriawiri n’kupeza malo oswanirana.

Kuuluka atafola ngati chilembo cha V kumathandiza atsekwe kuti onse azionana ndiponso kuti azitsatira mwamsanga tsekwe wapatsogolo akasintha kolowera, akasintha liwiro komanso akakwera m’mwamba kapena kutsika m’munsi. Komanso akatswiri ena amakhulupirira kuti mphepo imene amakupiza atsekwe omwe ali patsogolo imathandiza kuti atsekwe kumbuyo aziuluka mosavutikira. Mulimonse mmene zililimo, zikuoneka kuti nthawi zambiri atsekwe akamasamuka amakhala kagulu ka mabanja angapo, ndipo atsekwe akuluakulu amasinthanasinthana kutsogolera gululo.

Kawirikawiri, atsekwe a ku Canada amamanga chisa malo amodzimodzi chaka ndi chaka. Nthawi zambiri amamanga chisa chawocho ndi timitengo, udzu ndiponso ndere. Atsekwe amakhala ndi mwamuna kapena mkazi mmodzi moyo wawo wonse. Mwamuna kapena mkazi akafa, tsekwe wotsalayo amatha kuyamba kukhala ndi mwamuna kapena mkazi wina. Komabe, nthawi zambiri amakhala yekha.

Tsekwe amatha kuikira mazira anayi mpaka asanu ndi atatu, ndipo amawaumbatira kwa masiku pafupifupi 28. Makolowo amateteza kwambiri anapiye awo. China chikafuna kuwagwira kapena kugwira anapiyewo, makolowo amakalipa kwambiri. Amatha kumenya mdaniyo zolimba ndi mapiko.

Anapiye a tsekwe amayamba kulankhula adakali m’dzira. Nthawi zina amalira mokweza (posonyeza kukondwa) ndipo nthawi zina amalira momvetsa chisoni kwambiri. Atsekwe akuluakulu akamalankhulana ndi anapiye awo kapena akamalankhulana okhaokha, nawonso amalira mosiyanasiyana. Ndipo, ofufuza anapeza kuti atsekwe a ku Canada ali ndi kaliridwe kosiyanasiyana kokwana 13.

Kunena zoona, atsekwe amapereka umboni wakuti ndi ‘anzeru.’ (Miyambo 30:24) Ndipotu, Yehova Mulungu ndiye ayenera kutamandidwa chifukwa ndiye analenga zonse, kuphatikizapo mbalame za mumlengalenga.—Salmo 104:24.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 17]

Kodi Mukudziwa?

● Anapiye a tsekwe akangoti aswa, amachoka pachisacho ndi makolo awo, osadzabwereraponso. Nthawi zambiri mabanja amayendera limodzi.

● Atsekwe a mizera iwiri m’mutu akuti akamasamuka amadutsa pamwamba pa phiri la Everest, lomwe ndi lalitali pafupifupi mamita 8,900.

● Atsekwe ena amatha kuuluka makilomita mpaka 1,600 osapumulira.

● Akamauluka pa liwiro lofanana ndi la tsekwe amene akuuluka yekhayekha, atsekwe amene akuuluka atafola ngati chilembo cha V sakupiza kwambiri mapiko, ndipo zimenezi zimawathandiza kuti mtima usamathamange kwambiri.

[Mawu a Chithunzi]

Top left: U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./Duane C. Anderson

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

Flying geese: © Tom Brakefield/CORBIS