Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikhulupiriro Chandithandiza Kupirira Matenda Oopsa

Chikhulupiriro Chandithandiza Kupirira Matenda Oopsa

Chikhulupiriro Chandithandiza Kupirira Matenda Oopsa

YOSIMBIDWA NDI JASON STUART

“Pepani a Stuart. Muli ndi matenda owononga minyewa a ALS, omwe amatchedwanso kuti matenda a Lou Gehrig.” * Ndiyeno adokotala anandiuza zomwe zidzandichitikire chifukwa cha matendawa: Posachedwa sindidzatha kuyenda kapena kulankhula ndipo mapeto ake ndidzafa nawo matendawa. Ndiyeno ndinawafunsa kuti: “Kodi ndatsala ndi nthawi yotalika bwanji?” Iwo anayankha kuti: “Mutha kukhala zaka zitatu mwinanso kufika zisanu.” Ndinali ndi zaka 20 chabe. Koma ngakhale anandiuza uthenga womvetsa chisoniwu, ndinaona kuti ndinali wodalitsidwa m’njira zambiri. Tandilolani ndifotokoze.

NDINABADWA pa March 2, 1978, mu mzinda wa Redwood, ku California, m’dziko la United States. Ndinali wachitatu m’banja la ana anayi la a Jim ndi Kathy Stuart. Makolo anga anali kukonda kwambiri Mulungu, ndipo anaphunzitsa ineyo ndi abale anga, Matthew, Jenifer, ndi Johnathan kukonda kwambiri zinthu zauzimu.

Ndikukumbukira kuti kuyambira ndili mwana, kuchita nawo utumiki wa khomo ndi khomo, kuphunzira Baibulo, ndi kupezeka pamisonkhano zinali zinthu zimene banja lathu linkachita nthawi zonse. Kuleredwa m’banja lauzimu kumeneku kunandithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Yehova Mulungu. Sindinkadziwa n’komwe kuti chikhulupiriro changa chidzayesedwa.

Zomwe Ndinkafuna Ndili Mwana Zinakwaniritsidwa

Mu 1985 bambo anga anatenga banja lathu kupita ku New York kuti tikaone Beteli ku Brooklyn, lomwe ndi likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova. Ngakhale kuti ndinali wa zaka zisanu ndi ziwiri zokha, ndinaona kuti Beteli anali malo apadera. Aliyense ankaoneka kuti akusangalala ndi ntchito yake. Ndinaganiza kuti, ‘Ndikadzakula, ndidzapita ku Beteli kuti ndikathandize kupanga Mabaibulo a Yehova.’

Pa October 18, 1992, ndinasonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi. Patatha zaka zochepa, ndili ndi zaka 17, bambo anga ananditenga kuti ndikaonenso Beteli. Popeza ndinali wamkulu, ndinatha kumvetsa bwino kwambiri kufunika kwa ntchito yochitidwa pa Beteli. Ndinafika kunyumba nditatsimikiza kuposa kale kukwaniritsa cholinga changa chopita ku Beteli.

Mu September 1996, ndinakhala mpainiya wokhazikika, kapena kuti mlaliki wanthawi zonse. Kuti ndisadodometsedwe pa cholinga changa chotumikira pa Beteli, ndinadzitangwanitsa kwambiri ndi zinthu zauzimu. Ndinawonjezera kuwerenga kwanga Baibulo tsiku ndi tsiku ndiponso phunziro laumwini. Usiku ndinkamvetsera nkhani za Baibulo pa tepi. Zina mwa nkhani zimenezi zinali kunena zomwe zinachitikira Akristu amene anamwalira ali ndi chikhulupiriro cholimba cha Paradaiso ndiponso kuuka kwa akufa m’tsogolo. (Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4) Posapita nthawi ndinaloweza nkhani zonsezo pamtima. Panthawi imeneyo sindinadziwe mmene nkhani zolimbikitsa zimenezi zidzakhalire zofunika kwambiri posachedwapa.

Pa July 11, 1998, ndinalandira kalata kuchokera ku Brooklyn, yondiitana kupita ku Beteli. Pomatha mwezi umodzi kuchokera pa tsiku limeneli ndinafika ku Beteli. Ndinapatsidwa ntchito ya ku chipinda chomata ndi kusoka mabuku. Mabuku amenewa amatumizidwa ku mipingo yambiri. Choncho, zomwe ndinkafuna ndili mwana zinakwaniritsidwa. Ndinali pa Beteli ‘kupanga Mabaibulo a Yehova’!

Kuyambika kwa Matenda

Koma mwezi umodzi kapena kuposapo ndisanapite ku Beteli, ndinaona kuti sindinali kutha kuwongola kwambiri chala changa chakumanja cha mkombaphala. Chapanthawi yomweyo ndinaona kuti ntchito yanga yoyeretsa maiwe osambiramo inali kunditopetsa msanga kwambiri. Ndinaganiza kuti ndi ulesi chabe, chifukwa ndinali n’tagwirapo ntchito zina zofuna mphamvu kwambiri kuposa ntchito imeneyi popanda vuto lililonse.

M’milungu yochepa yomwe ndinali pa Beteli, matendawo anakula. Ndinkalephera kuyenda mwamsanga ngati anyamata anzanga akamakwera ndi kutsika masitepe. Pantchito yanga yopanga mabuku ndinkafunika kunyamula mipukutu ya zigawo za mabuku. Ndinkatopa mwamsanga, komanso dzanja langa lakumanja linayamba kupindika. Ndiponso, chala changa chamanthu chinayamba kukhwinyata, ndipo posapita nthawi ndinali kulephereratu kuchigwedeza.

Pakati pa mwezi wa October, patangopita miyezi iwiri ndili pa Beteli, adokotala anandiuza kuti ndili ndi matenda a ALS. Pamene ndinali kuchoka mu ofesi ya adokotala, nthawi yomweyo ndinakumbukira nkhani za m’Baibulo zomwe ndinaloweza pamtima zija. Mzimu wa Yehova uyenera kuti unali nane chifukwa kumwalira sikunandichititse mantha. Ndinangopita panja kukayembekezera galimoto yopita ku Beteli. Ndinapemphera kwa Yehova kuti alimbitse mtima makolo ndi azibale anga ndikawauza uthengawu.

Monga momwe ndanenera koyambirira kuja, ndinaona kuti ndinali wodalitsidwa. Cholinga chomwe ndinakhala nacho kuyambira ndili mwana, chofuna kupita ku Beteli, chinakwaniritsidwa. Usiku umenewo ndinawoloka mlatho wa Brooklyn, ndipo ndinathokoza Yehova chifukwa chondilola kukwaniritsa cholinga changa. Ndinam’pemphanso ndi mtima wonse kuti andithandize kupirira matenda osautsawa.

Anzanga ambiri anandiimbira foni n’cholinga chofuna kundithandiza ndi kundilimbikitsa. Ndinayesetsa kukhala wosangalala ndi kupewa kudzimvera chisoni. Koma pamene ndinali kulankhula ndi mayi anga pa foni, pafupifupi mlungu umodzi atandipeza ndi matendawa, iwo anati ndi bwino kuti ndinali kulimba mtima koma sikulakwa kulira. Atangonena mawu amenewa ndinayamba kusisima. Mwadzidzidzi ndinazindikira kuti zonse zomwe ndinakhala ndikuzifuna zija zithera pomwepa.

Mayi ndi bambo ankafuna kwambiri kuti ndipite kunyumba, chotero m’mawa wina kumapeto kwa mwezi wa October anagogoda pakhomo langa mwadzidzidzi. Masiku angapo otsatira, ndinawasonyeza malo osiyanasiyana a pa Beteli. Ndinawasonyezanso kwa anzanga ndiponso kwa achikulire ena omwe akhala pa Beteli nthawi yaitali. Masiku amene ndinali ndi makolo angawa pa Beteli anali ena mwa masiku amene ndinasangalala kwambiri pa moyo wanga wonse.

Kuyamikira Madalitso Omwe Ndapeza

Kuyambira nthawi imeneyo, Yehova wapitirizabe kundidalitsa m’njira zambiri. Mu September 1999, ndinakamba nkhani ya onse koyamba. Ndinatha kukamba nkhani zina zingapo m’mipingo yosiyanasiyana. Koma posapita nthawi zomwe ndinkalankhula sizinali kumveka moti ndinasiya kukamba nkhani za onse.

Dalitso linanso lomwe ndapeza ndilo chikondi cholimba ndiponso thandizo la banja langa komanso banja langa lauzimu la abale ndi alongo. Pamene miyendo yanga inali kufooka, anzanga ankandigwira manja kuti ndithe kuyenda mu utumiki. Ena ankabwera kunyumba kwathu kudzathandiza kundisamalira.

Dalitso linanso lalikulu ndi mkazi wanga Amanda. Ndinayamba kucheza naye n’tachoka ku Beteli, ndipo ndinakopeka naye chifukwa anali wokhwima mwauzimu. Ndinamuuza zonse zokhudza matenda anga a ALS ndi zomwe adokotala ananena kuti zidzandichitikira chifukwa cha matendawa. Tisanayambe chibwenzi, tinkakhala limodzi mu utumiki nthawi zambiri. Tinakwatirana pa August 5, 2000.

Amanda anafotokoza kuti: “Ndinakonda Jason chifukwa choti amakonda Mulungu ndiponso ndi wachangu pa zinthu zauzimu. Anthu sanali kuvutika kum’konda, achikulire ndi ana omwe. Ine ndine wofatsa ndiponso sindikonda zolankhulalankhula koma iye ankakonda zolankhulalankhula ndiponso kucheza ndi anthu. Tonse timakonda nthabwala, chotero tikakhala limodzi tinkangokhalira kuseka. Ndinkamasuka naye kwambiri, ngati kuti tinadziwana kalekale. Jason anandifotokozera zonse zokhudza matenda ake ndiponso zomwe zidzachitike m’tsogolo. Koma ndinaganiza kuti ndi bwino kuti tisangalale mmene tingathere. Ndipo moyo ndi wosatsimikizika m’dongosolo lino la zinthu. Zinthu zogwa mwadzidzidzi zimagwera aliyense, ngakhale munthu wa thanzi labwino.”—Mlaliki 9:11.

Kupeza Njira Zolankhulira

Pamene anthu anayamba kuvutika kumva zonena zanga, Amanda ankamasulira zolankhula zanga. N’tasiyiratu kulankhula, tinapeza njira yapadera yolankhulirana. Amanda amatchula zilembo za afabeti, ndipo akanena chilembo chomwe ndikufuna, ndimaphethira. Iye amakumbukirabe chilembocho, kenako n’kutchula china. Mwa njira imeneyi ndimatha kunena zilembo zonse za ziganizo. Ine ndi Amanda taidziwa bwino kwambiri njira yolankhulirana imeneyi.

Tsopano, chifukwa cha luso lamakono, ndili ndi kompyuta yoika pamiyendo imene imandithandiza kulankhula ndi anthu. Ndimalemba pa kompyuta zimene ndikufuna kunena, ndiyeno mawu a m’kompyuta amatchula zonse zimene ndalemba. Popeza sinditha kugwiritsa ntchito manja anga, pali kachipangizo kamene amakayang’anitsa patsaya langa ndipo kamadziwa ndikagwedeza tsayalo. Pakona ya kompyuta pamaoneka kabokosi kali ndi zilembo za afabeti. Ndikamagwedeza tsaya ndimatha kusankha chilembo chimene ndikufuna ndipo mwa kutero ndimatha kulemba mawu.

Ndi kompyuta imeneyi ndimatha kulemba kalata kwa anthu amene achita chidwi ndi Baibulo. Anthu amenewa ndi omwe mkazi wanga amapeza mu utumiki. Pogwiritsa ntchito mawu a m’kompyutayi ndimatha kunena zinthu zomwe ndakonzekereratu kukalalikira ku khomo ndi khomo ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Ndatha kupitiriza kuchita upainiya wokhazikika mwa kugwiritsa ntchito njira zimenezi. Chaposachedwapa, ndinayambiranso kukamba nkhani ndiponso kuchita mbali zina zophunzitsa mumpingo umene ndili mtumiki wothandiza.

Kukhalabe Wanthabwala

Takumana ndi mayesero aakulu osiyanasiyana. Miyendo yanga itayamba kufooka, ndinkagwa nthawi zambiri. Panthawi zoposa ziwiri, ndinagwa chagada ndipo ndinatemeka m’mutu. Minofu yanga inkakungika ndipo zikatero ndinkangogwa ngati mtengo. Anthu omwe ali pafupi nane ankachita mantha ndipo ankabwera kudzandithandiza. Nthawi zambiri ndinkanena nthabwala kuti mitima yawo ikhale m’malo. Nthawi zonse ndinkayesetsa kukhala wanthabwala. Panalibenso china choti ndikanachita. Ndikanatha kukwiya chifukwa choona mmene moyo wanga ulili wovuta, komano zimenezo zikanandithandiza bwanji?

Usiku wina ndili kocheza ndi Amanda limodzi ndi anzathu awiri, ndinagwa chagada mwadzidzidzi ndipo ndinapweteka m’mutu. Ndimakumbukira kuti anthu atatuwo anada nkhawa kwambiri ndipo anawerama n’kumandiyang’ana, ndipo wina anandifunsa ngati sindinavulale.

“Inde sindinavulale, koma ndikuona nyenyezi,” ndinayankha motero.

“Kodi ukunena zoona?” mnzangayo anafunsa motero.

Ndinayankha kuti: “N’zoonadi, taonani,” ndikuloza nyenyezi zenizeni kumwamba. “N’zokongola.” Tonse tinaseka.

Kupirira Mavuto Tsiku ndi Tsiku

Pamene minofu yanga inapitiriza kukhwinyata ndinayamba kukumana ndi mavuto ambiri. Mwamsanga zinthu monga kudya, kusamba, kupita kukadzithandiza, kapena kumanga mabatani a zovala, zinakhala ntchito zotopetsa ndiponso zokhumudwitsa za tsiku ndi tsiku. Tsopano thanzi langa lafika poipa kwambiri moti sinditha kuyenda, kulankhula, kudya, kapena kupuma popanda wina kundithandiza. Anandiika paipi pa mimba imene amaikamo chakudya chamadzimadzi. Ndili ndi makina ondithandiza kupuma omwe anawalumikiza ku paipi yomwe ili pakhosi panga, kuti ndizitha kupuma.

Ngakhale kuti ndinkafuna kwambiri kuti ndizidzichitira ndekha zinthu mmene ndikanathera, nthawi zonse Amanda anali wokonzeka kundithandiza. Pamene ndakhala wodalira kwambiri ena, Amanda sanandichititsepo kudziona monga munthu woperewera. Nthawi zonse amandipatsa ulemu. Ntchito imene akuchita panopo yondisamalira ndi yaikulu kwambiri, koma ndikudziwa kuti yakhala yovuta.

Pofotokoza mmene amamvera, Amanda anati: “Jason wakhala akufooka pang’onopang’ono, chotero ndaphunzira mmene ndingamusamalire pamene zinthu zakhala zikusintha. Popeza akugwiritsa ntchito makina omuthandiza kupuma, amafunika kumusamalira usana ndi usiku. M’mapapo mwake mumachita makhololo ndi malovu ambiri, ndipo amafunika kuwachotsa ndi chopopera. Chifukwa cha zimenezi n’kovuta kuti awiri tonsefe tigone bwino usiku. Ndimakhala wosungulumwa ndiponso wokhumudwa nthawi zina. Ngakhale kuti nthawi zonse timakhala pamodzi, n’zovuta kuti tilankhulane. Jason anali munthu wokonda kulankhula, koma tsopano maso ake okha ndi amene amaonetsa kuti akusangalala. Iye amakondabe nthabwala, ndipo amaganiza bwinobwino. Koma ndimafuna n’tamva mawu ake. Ndimafunanso atandikumbatira ndi kundigwira dzanja ngati momwe ankachitira kale.

“Anthu nthawi zina amandifunsa kuti ndimatha bwanji kupirira. Vuto limeneli landiphunzitsa kuti ndifunikira kudalira kwambiri Yehova. Ndikayamba kudzidalira ndekha, ndimaganiza kwambiri za vuto langali moti ndimamva ngati sindingathe n’kupuma komwe. Pemphero limandithandiza, chifukwa choti Yehova yekha ndi amene amandimvetsa bwino ndiponso ndi amene amamvetsa bwino zimene ndikukumana nazo. Makolo a Jason akhala akundithandiza kwambiri. Nthawi zonse ndikafuna kupumako kapena kupita mu utumiki wa kumunda iwo amandithandiza. Ndimayamikira kwambiri thandizo limene abale ndi alongo mumpingo wathu atipatsa. Chinanso chimene chimandithandiza ndi kukumbukira kuti mavuto alionse m’dongosolo lino ndi akanthawi ndiponso ndi opepuka. (2 Akorinto 4:17) Ndimayesetsa kuganizira kwambiri dziko latsopano limene likubwera, mmene Yehova adzakonza zinthu zonse. Pamene mavuto onsewa adzatha Jason n’kukhala wathanzi labwino, mosakayikira ndidzasangalala kwambiri n’kuliranso panthawi imodzimodziyo.”

Kulimbana ndi Maganizo Ofoola

Monga mwamuna, nthawi zina zimandikhumudwitsa kwambiri kukhala pa njinga ya olumala, osatha kuchita chilichonse. Ndikukumbukira zomwe zinachitika nthawi ina banja lathu lonse litapita kukacheza kunyumba kwa achemwali anga madzulo. Ndinali ndisanadye chakudya chotero ndinkamva njala. Aliyense anali kusangalala kuwotcha nyama ndi chimanga. Pamene ndinali kuonerera ena akudya ndi kusewera ndi makanda, ndinavutika maganizo kwambiri. Ndinayamba kuganiza kuti: ‘Chimenechitu sichilungamo! N’chifukwa chiyani sindikuchita nawo zinthu zonsezi?’ Sindinafune kusokoneza aliyense pamachezawo, chotero ndinapempha Yehova kuti andithandize kuti ndisalire.

Ndinakumbukira kuti mwa kukhala wokhulupirika, ndingapatse Yehova mwayi woyankha Satana amene akumutonza. (Miyambo 27:11) Zimenezi zinandipatsa nyonga, chifukwa ndinazindikira kuti pali zinthu zofunika kwambiri kuposa kudya chimanga ndi kusewera ndi makanda.

Ndikudziwa bwino kwambiri mmene zilili zosavuta kwa munthu wodwala monga momwe ndilili inemu kukhala wongoganizira mavuto ake. Koma ndaona kuti n’zothandiza kukhala ‘wochuluka mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akorinto 15:58) Mwa kukhala wotanganidwa ndi utumiki, sindimakhala ndi nthawi yoganizira mavuto anga. Kuchita ntchito yothandiza ena kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yehova kwandithandiza kwambiri kukhala wachimwemwe.

Pali chinthu chinanso chomwe chandithandiza kulimbana ndi kuvutika maganizo. Ndimakumbukira zokumana nazo za anthu okhulupirika amene anali ku ndende, ena ali mu zipinda zaokha, chifukwa choti anakana kusiya kulalikira Ufumu wa Mulungu. Ndimayerekeza chipinda changa kukhala ndende yanga ndi kuti ndili m’ndendeyi chifukwa cha chikhulupiriro changa. Ndimaganizira za zinthu zabwino zimene ndili nazo poyerekezera ndi ena mwa abale amenewo. Ndimatha kuwerenga mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Ndimatha kuchita nawo misonkhano yachikristu, kaya mwa kupita ku Nyumba ya Ufumu kapena kumvetsera pafoni. Ndili ndi ufulu wochita utumiki wanga. Ndili ndi mkazi wanga wokondedwa amene ndimacheza naye. Kusinkhasinkha motero kumandithandiza kuzindikira mmene ndilili wodalitsidwa.

Ndimakumbukira kwambiri mawu a mtumwi Paulo akuti: “Sitifoka: koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m’kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.” Ndithudi umunthu wanga wakunja ukuvunda. Koma ndine wotsimikiza kuti ndisafooke. Chimene chimandithandiza ndi kuika maso anga achikhulupiriro pa “zinthu zosaoneka,” kuphatikizapo madalitso adziko latsopano likubwerali. Ndikudziwa kuti m’dziko limenelo Yehova adzandisintha kuti ndikhalenso ndi thanzi labwino.—2 Akorinto 4:16, 18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Kuti mumvetse mmene matendawa amakhalira, werengani bokosi lakuti “Mfundo Zokhudza Matenda a ALS,” patsamba 27.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

Mfundo Zokhudza Matenda a ALS

Kodi ALS n’chiyani? ALS (amyotrophic lateral sclerosis) ndi matenda amene amakula mwamsanga ndipo amawononga minyewa ya m’fupa lamsana ndi ya mbali ina ya ubongo. Minyewa imeneyi ntchito yake ndi kunyamula mauthenga kuchokera ku ubongo kupita nawo ku minofu m’thupi. ALS imapangitsa minyewa imeneyi kufota kapena kufa ndipo kenako ziwalo zimafa pang’onopang’ono. *

N’chifukwa chiyani matenda a ALS amatchedwanso matenda a Lou Gehrig? Gehrig anali katswiri wotchuka wa ku United States wa masewera a mpira, amene anapezeka ndi matenda a ALS mu 1939 ndipo anamwalira mu 1941 ali ndi zaka 38. M’mayiko ena matenda amenewa amatchedwa matenda owononga minyewa, koma matenda oterewa alipo amitundumitundu, kuphatikizapo matenda a ALS. Matenda a ALS nthawi zina amatchedwanso matenda a Charcot kutengera dzina la Jean-Martin Charcot, katswiri wa minyewa wa ku France amene anali woyamba kufotokoza za matendawa mu 1869.

Kodi chimayambitsa ALS n’chiyani? Chimene chimayambitsa matendawa sichikudziwika. Malinga ndi zomwe ofufuza apeza, zimene zingayambitse matendawa ndi mavailasi, kuperewera kwa zakudya zomanga thupi, nthenda ya kumtundu (makamaka ALS yotengera kumtundu), zitsulo zina zake, poizoni amene amawononga minyewa (makamaka ALS ya ku Guam), kusokonezeka kwa mphamvu yoteteza thupi ku matenda, ndi kusokonezeka kwa timadzi tinatake ta m’thupi.

Kodi chimachitika n’chiyani matendawa akamakula? Minofu ya thupi lonse imafooka ndi kukhwinyata. Pamene matenda apitirira minofu imene imathandiza popuma imafooka. Ndipo m’kupita kwa nthawi wodwalayo amadalira makina othandiza kupuma. Chifukwa choti matendawa amakhudza minyewa yokha, sawononga kuganiza kwa wodwalayo, umunthu wake, nzeru zake, kapena kakumbukiridwe kake ka zinthu. Samulepheretsanso kuona, kununkhiza, kulawa, kumva, ndi kuzindikira kuti chinthu china chamukhudza. Nthawi zambiri munthu amamwalira pakatha zaka mwina zitatu mpaka zisanu chiyambire matendawa. Koma odwala okwana pafupifupi 10 pa 100 alionse amatha kukhala zaka khumi kapena kuposapo.

Kodi wodwala amalandira chithandizo chotani? Palibe mankhwala amene amachiza ALS. Adokotola angapereke chabe mankhwala ochepetsa ululu. Malinga ndi mmene matendawo alili, wodwala angapindule ndi maphunziro omuthandiza kugwiritsiranso ntchito ziwalo zake, kudzichitira yekha zinthu, kulankhula, ndi kugwiritsa ntchito zipangizo zina zomuthandiza.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 48 Pali mitundu itatu ya matenda a ALS imene ikudziwika. Mitundu yake ndi: Osatengera kumtundu (omwe ali ofala kwambiri), otengera kumtundu (pafupifupi anthu 5 mpaka 10 pa anthu 100 alionse odwala matenda amenewa amakhala oti anatengera kumtundu). Ndipo pali a ku Guam (anthu ambiri amene adwalapo nthendayi ndi a ku Guam ndi zilumba zina za m’nyanja ya Pacific).

[Mawu a Chithunzi]

Lou Gehrig: Photo by Hulton Archive/Getty Images

[Chithunzi patsamba 25]

Kuona Beteli mu 1985

[Chithunzi pamasamba 26, 27]

Ine ndi Amanda patsiku la ukwati wathu

[Chithunzi patsamba 28]

Kompyuta yapadera yoika pamiyendo imandithandiza kulankhula

[Chithunzi pamasamba 28, 29]

Ndimasangalala kukamba nkhani mumpingo wathu