Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dzikoli Likulowera Kuti?

Kodi Dzikoli Likulowera Kuti?

Kodi Dzikoli Likulowera Kuti?

KODI zinthu zidzakhala bwanji zaka 10, 20, kapena 30 zikubwerazi? Ndi uchigawenga umene wafala masiku anowu, zingakhale zochititsa mantha kuganizira mmene zinthu zidzakhalire m’tsogolo. Luso la zopangapanga likupita patsogolo kwambiri. Mayiko ambiri akukhala modalirana chifukwa choyendetsera limodzi ntchito zosiyanasiyana. Kodi m’tsogolomu atsogoleri a padziko lonse adzagwirizana n’kukonza zinthu kukhala bwino? Anthu ena amakhulupirira zimenezi. Iwo amayembekezera kuti pofika chaka cha 2015, atsogoleri a mayiko adzathetsa njala ndi umphawi, zomwe ndi zofala, adzachepetsa kufala kwa Edzi, ndiponso adzachepetsa ndi theka chiwerengero cha anthu amene alibe madzi abwino akumwa komanso sakhala malo aukhondo.—Onani bokosi lakuti “Zimene Anthu Akulakalaka Zikusiyana ndi Zimene Zikuchitikadi.”

Komabe, nthawi zambiri zimaoneka kuti zimene anthu amayembekezera sizichitika. Mwachitsanzo, zaka makumi angapo zapitazo katswiri wina anafotokoza kuti podzafika chaka cha 1984, alimi azidzatha kulima ndi mathirakitala pansi pa nyanja za mchere; wina anati podzafika chaka cha 1995, galimoto zizidzakhala ndi kompyuta zothandiza kupewa ngozi; ndipo wina ananena kuti podzafika chaka cha 2000, padzakhala anthu pafupifupi 50,000 okhala mumlengalenga ndi kumagwira ntchito zawo komweko. N’zosachita kufunsa kuti panopo anthu amene ananena zimenezi amalakalaka akadapanda kunena. Mtolankhani wina analemba kuti: “Palibenso china chilichonse kuposa kupita kwa nthawi chomwe chimachititsa anthu anzeru kwambiri kuti aoneke opusa kwambiri.”

Buku Lokhala Ngati Mapu Otitsogolera

Anthu ali ndi maganizo ambiri onena za m’tsogolo, koma nthawi zina maganizo awowo amangokhala zolakalaka chabe, osati zinthu zoti zingachitike. Kodi n’kuti komwe tingapeze mfundo zodalirika zonena za m’tsogolo?

Taganizirani fanizo ili. Yerekezerani kuti muli m’basi ndipo mukudutsa m’dziko lachilendo. Ndiyeno mukuyamba kuda nkhawa chifukwa choti deralo simukulidziwa. Mukuganizaganiza kuti, ‘Kodi panopo ndili kuti makamaka? Kodi basiyi ikuloweradi kolondola? Patsala mtunda wotani kuti ndifike komwe ndikupita?’ Mutaona pa mapu olondola n’kusuzumira pa windo lanu ndi kuona zikwangwani za mumsewu, mungathe kupeza mayankho a mafunso anuwo.

Umu ndi mmene zinthu zilili kwa anthu ambiri amene amada nkhawa akaganizira za m’tsogolo. Amadzifunsa kuti, ‘Kodi tikulowera kuti? Kodi tidzapezadi mtendere wa padziko lonse? Ngati ndi choncho, kodi zimenezi zidzachitika liti?’ Baibulo lili ngati nyali yomwe ingatithandize kuyankha mafunso amenewa. Tikaliwerenga mosamala, ndi kuona bwinobwino zomwe zikuchitika padziko pano, kukhala ngati tasuzumira pawindo, tingadziwe zambiri zokhudza pomwe tili ndi kumene tikulowera. Komabe, choyamba tikufunika kuona mmene mavuto athuwa anayambira.

Chiyambi Chomvetsa Chisoni

Baibulo limatiuza kuti Mulungu atalenga mwamuna ndi mkazi woyamba, iwo anali angwiro ndipo anawaika m’paradaiso. Adamu ndi Hava anapangidwa kuti akhale kwamuyaya, osati zaka 70 kapena 80 zokha ayi. Mulungu anawauza kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” Cholinga cha Mulungu chinali choti Adamu, Hava, ndiponso mbadwa zawo adzakulitse Paradaiso mpaka kufika padziko lonse lapansi.—Genesis 1:28; 2:8, 15, 22.

Adamu ndi Hava anapandukira Mulungu. Motero anathamangitsidwa m’Paradaiso. Kuwonjezera apo, matupi ndiponso ubongo wawo zinayamba kufooka pang’ono ndi pang’ono. Tsiku lililonse likamatha, imfa yawo inali kuyandikira pang’ono ndi pang’ono. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mwa kupandukira Mlengi wawo, iwo anachimwa, ndipo “mphoto yake ya uchimo ndi imfa.”—Aroma 6:23.

Mapeto ake, Adamu ndi Hava anamwalira, koma panthawi yomwe amamwalirayi anali atabereka ana angapo aamuna ndi aakazi. Kodi zikanatheka kuti ana amenewa akwaniritse cholinga chomwe Mulungu anali nacho poyambirira? Ayi, chifukwa chakuti iwo anatengera kupanda ungwiro kuchokera kwa makolo awo. Ndipotu, mbadwa zonse za Adamu zimapatsirana uchimo ndi imfa. Nafenso tinatengera uchimo ndi imfa. Baibulo limati: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”—Aroma 3:23; 5:12.

Kudziwa Pamene Tili

Kupanduka kwa Adamu ndi Hava kunali chiyambi cha ulendo wautali ndi wovuta wa anthu ndipo ulendowu ukupitirirabe mpaka masiku athu ano. Zili ngati mmene ananenera mwamuna wina amene analemba nawo Baibulo kuti, anthu ‘anagonjetsedwa kuutsiru.’ (Aroma 8:20) Mawu amenewa akufotokozadi bwino kwambiri mavuto amene anthufe tikukumana nawo. Zina mwa mbadwa za Adamu ndi amuna ndi akazi omwe ndi akatswiri pa zamankhwala ndiponso pa luso la zopangapanga. Koma palibe ngakhale mmodzi wa mbadwa zimenezi amene wakwanitsa kubweretsa mtendere ndiponso umoyo wabwino padziko lonse monga momwe Mulungu ankafunira.

Aliyense wa ife wakhudzidwa ndi kupanduka kwa Adamu ndi Hava. Mwachitsanzo, ndani amene sanavutikepo ndi kusoweka kwa chilungamo, sanavutikepo ndi mantha chifukwa cha umbanda, ngakhalenso matenda aakulu? Ndaninso amene sanavutikepo ndi chisoni chimene tonsefe timakhala nacho munthu amene timam’konda akamwalira? Zimaoneka kuti mtendere umene timakhala nawo pamoyo wathu sukhalitsa, umasokonezedwa ndi mavuto. Ngakhale kuti nthawi zina timasangalala, moyo wathu umangofanana ndi mmene Yobu anaufotokozera pamene anati: “Munthu . . . ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.”—Yobu 14:1.

Tikaganizira komwe tachokera ndiponso mavuto omwe tikukumana nawo panopa, n’zotheka kusaona cholimbikitsa chilichonse m’tsogolomu. Koma Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu sadzalola kuti zinthu zipitirize monga momwe zililimu mpaka muyaya. Cholinga chomwe anali nacho poyambirira pamene ankalenga munthu chidzachitika. (Yesaya 55:10, 11) Kodi tingatsimikize bwanji kuti zimenezi zichitika posachedwa?

Malinga ndi zimene Baibulo limanena, panopo tili m’nthawi yowawitsa yotchedwa “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1) Mawu akuti “masiku otsiriza” sakunena za mapeto a dziko lapansili ndiponso zamoyo zonse zomwe zilipo ayi. Koma, akutanthauza “mathedwe a nthawi ya pansi pano,” zomwe zikutanthauza mapeto a dongosolo losautsali. (Mateyu 24:3) Baibulo limafotokoza zochitika ndiponso makhalidwe a anthu omwe adzafale m’masiku otsiriza amenewa. Taonani zina mwa zimenezi m’bokosi la patsamba 8, ndipo kenako ganizirani zomwe zikuchitika padziko lapansi pano. Mapu athu, lomwe ndi Baibulo, akutithandiza kudziwa pamene tili tsopano, kuti ndi pafupi kwambiri ndi mapeto a dongosolo lino la zinthu. Komano, kodi chidzatsatirepo n’chiyani?

Zimene Zili M’tsogolo

Adamu ndi Hava atangopanduka, Mulungu anayamba kufotokoza cholinga chake chokhazikitsa Ufumu “woti sudzawonongeka ku nthawi zonse.” (Danieli 2:44) Ufumu umenewo, womwe anthu ambiri anaphunzitsidwa kuupempherera m’pemphero lomwe limadziwika ndi dzina loti Pemphero la Ambuye, udzabweretsa madalitso ochuluka kwa anthu.—Mateyu 6:9, 10.

Ufumu wa Mulungu sichinthu chinachake chokhala mumtima mwa munthu ayi. Ndi boma lenileni lakumwamba lomwe lidzachite zambiri padziko lapansi pano. Tangoonani zimene Mulungu akulonjeza kudzawachitira anthu kudzera mu Ufumu wakewu. Baibulo limati choyamba Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ (Chivumbulutso 11:18) Kodi anthu omwe amam’mvera adzawachitira chiyani? Mawu Ake olembedwa amati, “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.” (Chivumbulutso 21:4) Kodi ndi munthu uti amene angachite zinthu ngati zimenezi? Ndi Mulungu yekha amene angatichitire zinthu zomwe anafuna kuwachitira anthu poyambirira.

Kodi mungatani kuti mudzapindule ndi madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse? Lemba la Yohane 17:3 limati: ‘Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.’ Panopa Mboni za Yehova zili m’kati mogwira ntchito yophunzitsa yomwe ikuthandiza anthu kuchita zimenezi. Izo zikugwira ntchitoyi m’mayiko oposa 230, ndipo mabuku awo amafalitsidwa m’zinenero zoposa 400. Ngati mukufuna kudziwa zambiri, onanani ndi Mboni za Yehova kwanuko kapena lemberani kalata ku adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Tsono tamverani, inu amene mumati, ‘Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka tikuchita malonda ndikupanga ndalama.’ Mudziwa bwanji? Inu simudziwa ngakhale chimene chiti chichitike mawa.”—Yakobo 4:13, 14, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Baibulo limafotokoza mbiri yathu kuyambira pa mwamuna ndi mkazi woyambirira. Motero limatiuza komwe tinachokera. Limatisonyezanso kumene tikulowera. Koma kuti timvetse zimene Baibulo limatiuza, timafunika kuliphunzira bwinobwino, ngati mmene tingachitire ndi mapu

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Mawu akuti “uchimo” angathe kutanthauza kuchita cholakwa kapena kukhala ndi mtima wokonda kuchita zoipa. Tinabadwa ochimwa, ndipo izi zimakhudza mmene timachitira zinthu. “Kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.”—Mlaliki 7:20

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Mutati muumbe njerwa ndi chikombole chopindika, njerwa zonse zingakhale zopindika. Popeza ndife mbadwa za Adamu, tingati ndife njerwa zake, ndipo ndife opindika chifukwa cha kupanda ungwiro. Kupindika kumeneko n’komwe Adamu, “chikombole chathu,” anali nako

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Baibulo limati: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Izi zikusonyeza chifukwa chimene zochita za anthu zofuna kubweretsa mtendere padziko lonse zalepherekera. Munthu sanalengedwe kuti ‘azilongosola mapazi ake’ popanda kuthandizidwa ndi Mulungu

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Wamasalmo wotchulidwa m’Baibulo anauza Mulungu kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Monga nyali, Baibulo limatithandiza kukhala ndi nzeru tikafuna kusankha zochita. Popeza ndi ‘nyali ya ku mapazi athu,’ limatiunikira njira kuti tizizindikira zomwe zidzachitikire anthu m’tsogolomu

[Bokosi patsamba 7]

ZIMENE ANTHU AKULAKALAKA ZIKUSIYANA NDI ZIMENE ZIKUCHITIKADI

Mu September 2000, mayiko onse a m’bungwe la United Nations anagwirizana zinthu zingapo zoti adzakhale atachita pofika chaka cha 2015. Zina mwa zimene anagwirizanazo ndi izi:

Kuchepetsa ndi theka chiwerengero cha anthu omwe amagwiritsa ntchito ndalama zosakwana dola imodzi patsiku komanso kuchepetsa chiwerengero cha anthu ovutika ndi njala.

Kuonetsetsa kuti ana onse akumaliza maphunziro a m’sukulu za pulayimale.

Kuthetsa kusiyana komwe kulipo pakati pa amayi ndi abambo pamaphunziro alionse.

Kuchepetsa kwambiri imfa za ana osakwanitsa zaka zisanu.

Kuchepetsa kwambiri imfa za amayi apakati.

Kuthetsa kufala kwa matenda a Edzi ndi kachilombo koyambitsa matendawa kuphatikizapo matenda ena onse akuluakulu, monga malungo, ndiponso kuyamba kuchepetsa chiwerengero cha anthu omwe ali ndi matendawa.

Kuchepetsa ndi theka chiwerengero cha anthu amene alibe madzi abwino akumwa.

Kodi zinthu zimenezi zingachitikedi? M’chaka cha 2004, akatswiri a zaumoyo padziko lonse ataonanso bwinobwino mmene zinthu zilili, anati pa zimene anthu akulakalaka pakufunikanso kuganizira kuti zomwe zikuchitika panopa sizikupereka chiyembekezo chilichonse. Mawu oyamba m’buku lakuti State of the World 2005 amati: “M’madera ambiri, umphawi ukupitiriza kubwezeretsa m’mbuyo chitukuko. Matenda monga Edzi ndiponso kachilombo komwe kamayambitsa matendawa zikufalikira, ndipo n’zotheka kuti m’mayiko ambiri matenda oterewa adzasakaza miyoyo yambiri. M’zaka zisanu zapitazi, ana pafupifupi 20 miliyoni anamwalira ndi matenda oti akanatha kupewedwa omwe anawatenga ku madzi, ndipo tsiku ndi tsiku anthu mamiliyoni ambiri akupitirizabe kuvutika ndi umphawi ndiponso uve womwe umayendera limodzi ndi kusowa madzi abwino akumwa ndiponso malo okhala aukhondo.”

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 8, 9]

ZIZINDIKIRO ZINA ZA “MASIKU OTSIRIZA”

Nkhondo zoti sizinachitikepo.—Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:4.

Njala.—Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:5, 6, 8.

Miliri.—Luka 21:11; Chivumbulutso 6:8.

Kuwonjezeka kwa kusaweruzika.—Mateyu 24:12.

Kuwononga dziko.—Chivumbulutso 11:18.

Zivomezi zikuluzikulu.—Luka 21:11.

Nthawi zowawitsa.—2 Timoteo 3:1.

Kukonda kwambiri ndalama.—2 Timoteo 3:2.

Kusamvera makolo.—2 Timoteo 3:2.

Kupanda chikondi chachibadwidwe.—2 Timoteo 3:3.

Kukonda zokondweretsa munthu, osati Mulungu.—2 Timoteo 3:4.

Kusadziletsa.—2 Timoteo 3:3.

Kusakonda chabwino.—2 Timoteo 3:3.

Kunyalanyaza zoopsa zomwe zikubwera m’tsogolo.—Mateyu 24:39.

Onyoza omwe amakana umboni wa masiku otsiriza.—2 Petro 3:3, 4.

Kulalikira Ufumu wa Mulungu padziko lonse.—Mateyu 24:14.

[Mawu a Chithunzi]

© G.M.B. Akash/Panos Pictures

© Paul Lowe/Panos Pictures

[Chithunzi patsamba 9]

Anthu amadziwa kuti Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu