Kodi Tili ndi Tsogolo Labwino?
Kodi Tili ndi Tsogolo Labwino?
Anthu amafunitsitsa atadziwa za m’tsogolo. Ndani wa ife sangafune kudziwa zomwe tidzachite mwezi wamawa, chaka chamawa, ngakhalenso zaka khumi zikubwerazi? Tikayang’ana m’tsogolo kwambiri, kodi dzikoli lidzakhala lotani zaka 10, 20, kapena 30 zikubwerazi?
KODI mukaganizira za m’tsogolo mumakhala n’chiyembekezo chilichonse? Anthu mamiliyoni ambiri ali nacho, ndipo anthu amenewa tingawagawe m’magulu awiri. Pali anthu amene amati ali ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti m’tsogolo muno zinthu zidzakhala bwino ndipo pali ena amene amakhulupirira kuti zinthu zidzakhala bwino chabe chifukwa choopa kuganizira zinthu zoopsa za m’tsogolo.
N’zoona kuti pali anthu ena amene amati akaganizira za m’tsogolo saonamo chabwino chilichonse. Ena mwa iwo ndi anthu amene amakonda kunena kuti dziko lonse lapansi lidzawonongedwa. Iwo amati ngati padzakhale anthu opulumuka adzakhala ochepa kwambiri.
Kodi inuyo mumaganiza kuti m’tsogolo muli zotani? Kodi mumaona kuti dzikoli lidzawonongedwa popanda wopulumuka aliyense kapena mumaona tsogolo labata ndi mtendere? Ngati mumayembekezera tsogolo la bata ndi mtendere, kodi chiyembekezo chanucho chili ndi maziko otani? Kodi maziko amenewo ndi enieni kapena ndi zongolakalaka chabe?
Mosiyana ndi zimene amanena anthu amene amati dziko lonseli lidzawonongedwa, ofalitsa magazini ya Galamukani! sakhulupirira kuti anthu adzatheratu padziko lapansi pano. Baibulo limapereka zifukwa zotsimikizika zokhulupirira kuti m’tsogolomu muli zinthu zosangalatsa kwambiri.
[Mawu a Chithunzi patsamba 5]
U.S. Department of Energy photograph