Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Mapiri Ndi Ofunika Pamoyo wa Padziko Lapansi (April 8, 2005) Kuona malo a Grand Tetons kunali chimodzi mwa zinthu zochititsa nthumanzi kwambiri pa moyo wanga. Koma nditawerenga momwe mapiri alili ofunika ndinachita chidwi kwambiri. Tsopano ndikudziwa bwino kwambiri kufunika kwa mapiri padziko lapansi pano ndiponso ndikuyamikira kwambiri Mlengi wodabwitsa amene anawapanga.

J. G., United States

Ndikaona kukongola kwa chilengedwe cha Yehova, ndimasowa mawu ofotokozera mmene ndimamvera. Ngakhale kuti anthu awononga chilengedwe, tingathebe kuyamikira ndi kusangalala ndi mapiri. Ndimasangalala kuuza ena zimene zidzachitike m’tsogolomu posachedwapa, monga momwe lemba la Salmo 72:16 limalonjezera.

R. C., United States

Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Ndizigwira Ntchito ya Manja Chifukwa Chiyani? (April 8, 2005) Ndimagwira ntchito pa kampani yopaka penti ya bambo anga. Koma munthu wina anandiuza kuti pantchito imeneyi munthu safunikira kuganiza. Komabe, nkhaniyi inanena kuti Yesu ndi Paulo anali kugwira ntchito za manja. Tsopano ndalimbikitsidwa kuti ndizigwira ntchito yanga ndili wosangalala kwambiri. Ndikufuna kuidziwa bwino kwambiri ntchitoyi kuti ndidzagwiritse ntchito luso limeneli pomanga Nyumba za Misonkhano ndi Nyumba za Ufumu.

M. Y., Japan

Nkhani imeneyi inandilimbikitsa kwambiri. Inandikumbutsanso kuti cholinga chathu chachikulu pamoyo ndicho kutumikira Yehova Mulungu ndipo ntchito imene ndisankhe ikhale yogwirizana ndi cholinga chimenechi. Nkhani yabwino kwambiri imeneyi inandithandiza kusintha kuti munthu asamachite kundiuza kuti ndigwire ntchito zimene zikufunika kugwiridwa pakhomo pathu. Chofunika kwambiri n’chakuti, nkhaniyi yandithandiza kudziwa mmene Yehova amaonera ntchito za manja.

Y. K., Russia

Zamoyo Zinapangidwa ndi Tinthu Todabwitsa Tangati Matcheni (January 22, 2005) Ndili ndi zaka 15. Ku sukulu mu kalasi la sayansi ya zamoyo, tikuphunzira mmene zamoyo zimapezera chakudya. Nditapita ndi magaziniyi kusukulu, aphunzitsi athu anagwiritsa ntchito nkhaniyi potiphunzitsa. Anatisonyeza zithunzi zomwe zili m’nkhaniyi. Titamaliza kuphunzira, onse m’kalasimo anafuna magaziniyi. Nkhaniyi inasonyeza bwino kuti Yehova ali ndi nzeru zochuluka kwambiri. Mosakayikira afunikira kum’tamanda. Ndikuyembekezera mwachidwi nthawi imene zamoyo zonse zidzatamande Yehova.

Y. B., Russia

“Ndikanakonda Anthu Akanadziwa Zimenezi!” (January 8, 2005) Ndili ndi zaka 17, ndipo nthawi zambiri ndaganizirapo zodzasamukira kudera kumene kukufunika olengeza Ufumu oti akathandize. Chitsanzo cha David chandilimbikitsa kuti nditsimikize zodzasamukira ku dera loterolo ndikangomaliza sukulu. Pitirizani kufalitsa zitsanzo zolimbikitsa zotero. Achinyamata a msinkhu wanga amafunika kuwalimbikitsa kawirikawiri kuti apite patsogolo pantchito yolalikira.

K. O., Poland

Ndili ndi zaka 20, ndipo ndinalira pamene ndinkawerenga nkhaniyi. Ndinati, ‘Ngati ndingamwalire ndili wachinyamata, sindikufuna kuti ndidzanong’oneze bondo chifukwa choti sindinatumikire Yehova ndi mphamvu zanga zonse.’ Cholinga changa n’choti posachedwapa ndikhale mlaliki wanthawi zonse. Ndiika nkhani imeneyi m’felemu n’kuipachika pakhoma kuti ndisadzaiwale mmene inandikhudzira panthawi imene ndinkaiwerenga. Zikomo kwambiri chifukwa chofalitsa zokumana nazo zosangalatsa zotere.

N. N., Japan