Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kwa Owerenga

Kwa Owerenga

Kwa Owerenga

KUYAMBIRA ndi magazini ino, zinthu zina ndi zina mu Galamukani! zisintha. Komabe, zambiri sizisintha.

Cholinga chomwe magazini ya Galamukani! yakhala nacho kwa zaka zambiri sichinasinthe. Monga momwe likufotokozera tsamba 4, “magaziniyi imafalitsidwa n’cholinga chophunzitsa banja lonse.” Magaziniyi imaonetsetsa zochitika padziko lonse, imakhala ndi nkhani za anthu a zikhalidwe zosiyanasiyana, imalongosola zinthu zodabwitsa za chilengedwe, imakamba nkhani zaumoyo, kapena kufotokoza nkhani za sayansi kwa anthu omwe sanaphunzire sayansi. Galamukani! ipitiriza kuwadziwitsa anthu amene amaiwerenga zinthu zosiyanasiyana, ndi kuwathandiza kukhala tcheru kuzochitika padzikoli.

M’magazini ya Chingelezi ya August 22, 1946, Galamukani! inalonjeza kuti: “Cholinga chachikulu cha magaziniyi ndicho kutsatira kwambiri choonadi.” Mogwirizana ndi lonjezo limenelo, Galamukani! yakhala ikuyesetsa nthawi zonse kufalitsa nkhani zoona. Kuti izi zitheke, nkhani zake zimafufuzidwa mokwanira bwino ndipo amatsimikizira kuti n’zolondola. Koma magaziniyi ‘yatsatira kwambiri choonadi’ m’njira ina yofunika kwambiri.

Magazini ya Galamukani! yakhala ikulimbikitsa oiwerenga kuti aziona za m’Baibulo. Komabe, kuyambira ndi magazini ino, Galamukani! izikhala ndi nkhani zambiri zofotokoza za m’Baibulo kusiyana ndi momwe inali kuchitira m’mbuyomu. (Yohane 17:17) Galamukani! ipitirizanso kukhala ndi nkhani zosonyeza mmene malangizo abwino a m’Baibulo angatithandizire kukhala moyo wabwino ndi watanthauzo masiku ano. Mwachitsanzo, nkhani zakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” ndiponso “Zimene Baibulo Limanena” zimakhala ndi malangizo ambiri a m’Baibulo, ndipo zipitiriza kutuluka nthawi zonse m’magaziniyi. Kuwonjezera pamenepa, Galamukani! ipitiriza kulongosolera anthu omwe amaiwerenga lonjezo la m’Baibulo la dziko latsopano lamtendere lomwe posachedwapa lidzalowe m’malo mwa dongosolo losamvera malamulo limene lilipoli.—Chivumbulutso 21:3, 4.

Kodi n’chiyaninso chimene chasintha? Kuyambira ndi magazini ino, Galamukani! izisindikizidwa kamodzi pamwezi m’zinenero zambiri mwa zinenero zake 82 (poyamba inkatuluka kawiri pamwezi m’zinenero zambiri). * Chigawo chakuti “Zochitika Padzikoli,” chomwe chakhala chikusindikizidwa nthawi yaitali m’zinenero zambiri, chizituluka m’magazini iliyonse patsamba limodzi. Pakhalanso tsamba lina lakuti “Kuchokera kwa Owerenga” lomwe lizituluka nthawi zambiri. Komanso, patsamba 31, tiyamba kuikapo mbali yosangalatsa kwambiri yomwe izituluka m’magazini iliyonse, yakuti “Kodi Mungayankhe Bwanji?” Kodi tsamba limeneli lizikhala ndi zotani, ndipo kodi mungaligwiritse ntchito motani?

Taonani kwa nthawi yochepa chabe zimene zili patsamba 31 la magazini ino. Ana azisangalala ndi zigawo zina za tsambali; zina n’zofuna anthu omwe aphunzira Baibulo mozama. Chigawo chakuti “Zinachitika Liti?” chikuthandizani kukhala ndi chithunzithunzi cha nthawi yomwe anthu otchulidwa m’Baibulo anakhala moyo ndiponso nthawi imene zinthu zikuluzikulu zinachitika. Ngakhale kuti mayankho a chigawo chakuti “Za M’magazini Ino” azipezeka m’masamba osiyanasiyana m’magaziniyo, mayankho a mafunso enawo azisindikizidwa mozondotsa patsamba la m’magazini yomweyo, ndipo tizitchula tsamba lake. Bwanji osayamba mwafufuza kaye musanaone mayankho akewo ndipo kenako n’kufotokozera anzanu zimene mwaphunzira? Mungathenso kumakambirana pabanja panu kapena ndi ophunzira Baibulo anzanu, zinthu za patsamba limeneli lakuti, “Kodi Mungayankhe Bwanji?”

Zaka pafupifupi 60 zapitazo, Galamukani! inalonjeza kuti: “Pankhani zomwe zizikhalamo, magaziniyi iziyesetsa kukhala ndi nkhani za padziko lonse, osati za m’dziko limodzi lokha. Anthu oona mtima a m’mayiko onse azisangalala nayo. . . . Anthu ambiri, ana ndi akuluakulu omwe, . . . azithandizidwa, kuphunzitsidwa ndiponso kusangalala ndi nkhani zake.” Owerenga magaziniyi padziko lonse akuvomereza kuti Galamukani! yasunga lonjezo limeneli. Tikukutsimikizirani kuti ipitiriza kutero.

Ofalitsa

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 M’zinenero zina Galamukani! ikusindikizidwa kamodzi pa miyezi itatu, ndipo n’kutheka kuti mbali zimene zafotokozedwa m’nkhani ino sizizituluka m’zinenero zonse zoterozo.

[Zithunzi patsamba 3]

Mu 1919 inatchedwa “The Golden Age,” kenako inasintha dzina mu 1937 n’kukhala “Consolation,” ndipo mu 1946 inayamba kutchedwa “Galamukani!”

[Zithunzi patsamba 4]

Kwa nthawi yaitali, “Galamukani!” yakhala ikulimbikitsa oiwerenga kuti aziona za m’Baibulo

[Mawu a Chithunzi]

Guns: U.S. National Archives photo; starving child: WHO photo by W. Cutting