Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Maselo Ofiira a M’magazi Ndi Odabwitsa Kwambiri

Maselo Ofiira a M’magazi Ndi Odabwitsa Kwambiri

Maselo Ofiira a M’magazi Ndi Odabwitsa Kwambiri

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

Magazi ali ndi maselo ambiri ofiira. Dontho limodzi la magazi lili ndi mamiliyoni ambiri a maselo amenewa. Kuwaona kudzera m’chipangizo choonera tinthu tating’ono, amaoneka ngati mandasi olowa pakati. Selo lililonse lili ndi mamiliyoni ambiri a tinthu ting’onoting’ono tofiira tonyamula mpweya totchedwa himogulobini. M’kati mwa himogulobini aliyense muli kanthu kozungulira kopangidwa ndi tinthu tina tating’ono tosaoneka ndi maso totchedwa maatomu. Himogulobini aliyense amakhala ndi maatomu a hayidirojeni, kaboni, nayitirojeni, okosijeni, ndi sulfure okwana 10,000. Amakhalanso ndi maatomu anayi olemera a ayironi amene amathandiza magazi kuti azitha kunyamula mpweya wa okosijeni. Himogulobini amathandiza kuti mpweya woipa uchoke m’thupi upite ku mapapo kenako tiupumire kunja.

Mbali inanso yofunika kwambiri ya maselo ofiira a m’magazi ndi khungu lake. Khungu lodabwitsa limeneli limathandiza maselo kutamuka kukhala opyapyala kuti azitha kudutsa m’mitsempha yaing’ono kwambiri n’kufika ku mbali zonse za thupi.

Maselo ofiira a m’magazi amapangidwa m’kati mwa mafupa. Selo latsopano likalowa m’magazi, likhoza kuzungulira kudutsa mu mtima ndi m’thupi monse nthawi zoposa 100,000. Maselo ofiira amenewa alibe mutu umene maselo ena amakhala nawo. Zimenezi zimathandiza kuti maselowa akhale ndi malo ambiri onyamulira mpweya wabwino ndipo amakhala opepuka moti mtima umatha kupopa maselo amenewa ambiri kuti afike m’thupi lonse. Koma chifukwa choti alibe mutu, saatha kudzikonzanso. Chotero, masiku pafupifupi 120 akadutsa, maselo ofiirawa amakalamba ndipo saatha kutamuka. Maselo oyera aakulu amadya maselo otha ntchitowa ndipo amalavula maatomu a ayironi. Maatomu a ayironi amenewa amalowa m’madzi a m’magazi n’kubwerera ku mafupa kukagwiritsidwanso ntchito popanga maselo ofiira atsopano. Pa sekondi iliyonse, mafupa amapanga maselo ofiira atsopano okwana 2 miliyoni mpaka 3 miliyoni n’kuwalowetsa m’magazi.

Maselo ofiira ambirimbiri amenewa atasiya kugwira ntchito mwadzidzidzi, mungamwalire m’mphindi zochepa. Tiyenera kuyamikira kwambiri Yehova Mulungu chifukwa cha mbali yodabwitsayi ya chilengedwe chake, imene imatithandiza kukhala ndi moyo ndiponso kusangalala nawo. Mosakayikira mukugwirizana ndi wamasalmo amene ananena kuti: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.”—Salmo 139:1, 14.

[Chithunzi patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Selo lofiira la m’magazi

Khungu

Himogulobini (azikulitsa)

Okosijeni