Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwana Akamwalira

Mwana Akamwalira

Mwana Akamwalira

▪ Imfa ya mwana imakhala yopweteka kwambiri kwa otsala, makamaka makolo. Mayi wina amene mwana wake wa zaka 16 anapsa pangozi yoopsa n’kumwalira, anati: “Mulungu satilola kutenga malo a ana athu akamamwalira kapena kufera nawo limodzi.”

Koma mayiyu sanataye mtima, ndipo anafotokoza kuti: “Mulungu watiuza zoona zake za imfa, ndipo zimenezi zathandiza ineyo ndi mwamuna wanga kuti tisamakhumudwe kapena kulephera kuganiza bwino.” Mayiyu anavomereza kuti “si Mulungu wathu amene wachitira mwana wathu zimenezi, ndipo Iye analonjeza kuukitsa akufa m’paradaiso padziko lapansi. M’maganizo athu timatha kuona mwana wathu ali moyo, wathanzi ndiponso wosangalala. Timamuona ali ndi anzake ndiponso banja lathu.”

Ngakhale anthu amene amadalira kwambiri lonjezo la Mulungu la kuukitsa akufa amafunika kuwalimbikitsa. Mayiyu analimbikitsidwa ndi anzake ambiri, ndipo amawathokoza zedi. Iye anati: “Mfundo zambiri za m’Malemba zimene anatiuza ndiponso zinthu zambiri zotikomera mtima zimene anatichitira zinachokera m’kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Tinalimbikitsa onse amene tinali nawo pafupi kukawerenga kuti atimvetse bwino ndiponso amvetse bwino chisoni chimene tipitirizabe kukhala nacho.”

Mwinamwake, inuyo kapena munthu wina amene mukum’dziwa angalimbikitsidwe atawerenga kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Ngati mukufuna kuitanitsa kabukuka lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.