N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?
Zimene Achinyamata Amadzifunsa
N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?
“Ndinadzicheka kwambiri m’mikono moti anafunikira kundisoka kuchipatala. Panthawiyo, ndinauza adokotala kuti ndadzicheka ndi babu la magetsi. Zimenezi zinali zoona, kungoti sindinawauze kuti ndinachita kudzicheka dala.” Anatero Sasha, wa zaka 23.
“Makolo anga aona malo omwe ndadzicheka, koma angoona malo omwe sindinadzicheke kwambiri, omwe mukuoneka ngati ndakalika. . . . Nthawi zina amaona pena pomwe ndadzicheka poti sanaonepo, choncho ndimangowanamiza zinazake. . . . Sindikufuna kuti adziwe.” Anatero Ariel, wa zaka 13.
“Ndakhala ndikudzivulaza kuyambira ndili ndi zaka 11. Ndinkadziwa zoti Mulungu amaona kuti thupi la munthu n’lofunika kulisamalira, koma kudziwa zimenezi sikunadisiyitse kudzivulaza.”Anatero Jennifer, wa zaka 20.
MWINA mukudziwapo munthu wangati Sasha, Ariel, kapena Jennifer. * Mwina ndi mnzanu wa ku sukulu. Mwina ndi mchemwali wanu kapena mchimwene wanu. Mwinanso mungakhale inu nomwe. Ku United States kokha, akuti anthu okwana mamiliyoni angapo, omwe ambiri a iwo ndi achinyamata, amadzivulaza dala m’njira zosiyanasiyana, monga kudzicheka, kudziwotcha, kudzizunzunda, kapena kudzikala pakhungu. *
Kudzivulaza dala? M’mbuyomu, anthu ambiri akanati anthu amene amachita zimenezi amatero chifukwa chotsatira fashoni inayake yachilendo kapena chifukwa choti ali m’kagulu ka chipembedzo kenakake kodabwitsa. Komabe, m’zaka zaposachedwapa, anthu adziwa zinthu zambiri zokhudza kudzivulaza, komwe kumaphatikizapo kudzicheka kapena kudzipundula. Zikuonekanso kuti anthu amene akuulula kuti ali ndi vutoli awonjezekanso. Michael Hollander, mkulu wa chipatala chinachake chothandiza anthu omwe ali ndi vutoli ku United States, anati: “Dokotala aliyense akunena kuti vutoli likukula.”
Kudzivulaza nthawi zambiri sikupha munthu, koma n’koopsa. Mwachitsanzo, taganizirani za mtsikana winawake dzina lake Beth. Iye anati: “Ndikamadzivulaza, ndimagwiritsa ntchito
lezala. Andigonekapo m’chipatala kawiri. Ulendo winawake n’tadzicheka ndinafunika kupita kuchipatala n’kukafikira ku malo othandizira anthu ovulala kwambiri.” Mofanana ndi anthu ambiri amene ali ndi vuto limeneli, Beth akudzivulazabe mpaka panopa atakula. Iye anati: “Ndinayamba ndili ndi zaka 15, ndipo panopa ndili ndi zaka 30.”Kodi inuyo kapena munthu wina amene mukumudziwa ali ndi vuto lodzivulaza? Ngati ndi choncho, musataye mtima. Thandizo lilipo. M’magazini yotsatira ya Galamukani! tidzafotokoza momwe anthu amene amadzivulaza angathandizidwire. * Koma choyamba, ndi bwino kufotokoza kuti ndi anthu otani amene amakhala ndi vuto limeneli, ndipo n’chifukwa chiyani amachita zimenezi.
Anthu Odzivulaza Amakhala Osiyanasiyana
N’zovuta kuwaika m’gulu limodzi anthu amene amadzivulaza. Ena amachokera ku mabanja osowa mtendere, pamene ena amachokera ku mabanja achimwemwe. Ena amakhala oti amalephera ku sukulu, pamene ambiri amakhala oti amakhoza bwino. Nthawi zambiri anthu odzivulaza sasonyeza chizindikiro chilichonse choti ali ndi vuto, chifukwa munthu amene ali ndi mavuto sikuti nthawi zonse amachita kuonetsera kwa ena. Baibulo limati: “Ngakhale m’kuseka mtima uwawa.”—Miyambo 14:13.
Ndiponso, kudzivulaza kwake kumasiyanasiyana. Mwachitsanzo, atachita kafukufuku winawake anapeza kuti anthu ena amadzicheka kamodzi pachaka, pamene ena amadzicheka pafupifupi kawiri tsiku lililonse. N’zochititsa chidwi kuti amuna ambiri ayamba kudzicheka kuposa mmene anthu ankaganizira kale. Komabe, vutoli limapezeka makamaka pakati pa atsikana amene sanakwanitse zaka 20.
Ngakhale kuti anthu ake amakhala osiyanasiyana chonchi, ena amakhala ofanana m’njira zinazake. Buku linalake la achinyamata linati: “Achinyamata amene amadzivulaza, nthawi zambiri amaona kuti palibe chomwe angachite kuti asinthe zinthu pamoyo wawo, amavutika kuuza ena zakukhosi kwawo, amakhala osungulumwa kapena amaona kuti anthu ena amawasala. Achinyamata amenewa amachita mantha, ndipo amadzikayikira.”
N’zoona kuti anthu ena anganene kuti zimenezi zimachitikira pafupifupi wachinyamata aliyense amene akulimbana ndi zopinga zimene munthu amakumana nazo akamakula. Komabe, kwa anthu amene amadzivulaza, mavuto ake amakhala aakulu kwambiri. Chifukwa choti amalephera kuulula zimene zikuwavuta kwa munthu amene amamukhulupirira, angaone ngati mavuto amene akukumana nawo kusukulu, kuntchito, kapena kunyumba awakulira kwambiri. Amaona kuti mavutowa sadzatha ndiponso alibe woti angamuuze. Choncho amasowa chochita. Kenaka amatulukira chinthu chinachake: Akadzivulaza, amaona kuti apezako kampumulo ku zinthu zimene zikuwavutitsa m’maganizo, ndipo amaona kuti akupezako bwino kwa kanthawi.
N’chifukwa chiyani amafuna kudzimvetsa ululu m’thupi kuti achepetse ululu wa m’maganizo? Kuti tichitire chitsanzo, taganizirani zimene zimachitika adokotala akatsala pang’ono kukubayani jakisoni. Akamayamba kukubayani, kodi munayamba mwadzitsinako, kapena kukanikiza khungu lanu ndi chikhadabo, kuti musamve kupweteka kwa jakisoniyo? Munthu wodzivulaza amachita zofanana ndi zimenezi, ngakhale kuti iye amapyola pamenepa. Amaona kuti kudzicheka kumamuthandiza kuiwalako mavuto ake ndipo kumamubweretserako mpumulo ku ululu wake wa m’maganizo. Ndipo ululu wa m’maganizowo umakhala waukulu kwambiri moti amaona kuti kuli bwino azimva kupweteka m’thupi kusiyana ndi kumva kupweteka m’maganizo. Mwina n’chifukwa chake
munthu wina amene amadzivulaza anafotokoza kuti kudzicheka ndiko ‘mankhwala a mantha ake.’“Njira Yochepetsera Kuvutika Maganizo”
Anthu amene sakulidziwa bwino vuto limeneli angaganize kuti munthu akamadzivulaza ndiye kuti akufuna kudzipha. Koma nthawi zambiri zinthu sizikhala choncho. Sabrina Solin Weill, mkonzi wamkulu wa magazini inayake ya achinyamata, analemba kuti: “Nthawi zambiri anthu amenewa amakhala akufuna kuchotsa ululu wokhawo basi, osati miyoyo yawo.” Choncho buku lina linati kudzivulaza ndi “‘njira yosungira moyo’ osati yodziphera.” Bukulo linanenanso kuti kudzivulaza ndi “njira yochepetsera kuvutika maganizo.” Kodi amavutika maganizo chifukwa chiyani?
Atachita kafukufuku apeza kuti anthu ambiri amene amadzivulaza anavutikapo mwanjira inayake m’mbuyomu. Mwina anazunzidwa kapena kunyanyalidwa ali aang’ono. Ena amachita zimenezi chifukwa choti m’banja mwawo munali mavuto kapena kholo lawo linali chidakwa. Enanso amachita zimenezi chifukwa choti akudwala matenda a maganizo.
Pangakhalenso mavuto ena. Mwachitsanzo, Sara akuti ankadzizunza chifukwa chofuna kuti asamalakwitse zinthu. Ngakhale kuti anachitapo zinthu zolakwa zazikulu ndipo analandira thandizo kuchokera kwa akulu mumpingo, ankadziimba mlandu kwambiri chifukwa cha zinthu zimene ankalakwitsa tsiku ndi tsiku. Sara anati: “Ndinaona kuti ndifunika ‘kusiya kudzinyengerera.’ Kwa ine, kudzivulaza kunali ngati kudzilanga. ‘Kudzilanga’ kwake kunaphatikizapo kudzizula tsitsi, kudzicheka m’mikono, kudzimenya ndi kudzizunzunda kwambiri, komanso kudzipatsa zilango monga kuika dzanja langa m’madzi otentha kwambiri, kukhala panja kukuzizira kwambiri osavala chovala champhepo chilichonse, kapena kukhala tsiku lonse osadya.”
Sara ankadzivulaza chonchi chifukwa choti ankadzida kwambiri. Iye anati: “Nthawi zina ndinkadziwa kuti Yehova anandikhululukira zolakwa zanga, koma sindinkafuna kuti andikhululukire. Ndinkafuna ndivutike chifukwa ndinkadzida kwambiri. Ngakhale ndinkadziwa kuti Yehova sangakonze malo ozunzirako anthu, ngati malo amoto amene Matchalitchi Achikristu amaphunzitsa, ndinkafuna akonze malo oterowo kuti akazunzireko ine ndekha.”
“Nthawi Zowawitsa”
Ena angadabwe kuti n’chifukwa chiyani khalidwe lodetsa nkhawa ngati limeneli ladziwika bwino m’zaka zaposachedwa zokhazi. Komabe, anthu amene amaphunzira Baibulo akudziwa kuti tikukhala mu “nthawi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1) Choncho sadabwa kuona kuti anthu, kuphatikizapo achinyamata, amachita zinthu zovuta kuzimvetsa.
Baibulo limavomereza kuti “nsautso iyarutsa [kapena kuti, “ipengetsa”] wanzeru.” (Mlaliki 7:7) Mavuto amene achinyamata amakumana nawo akamakula, amene nthawi zina amaphatikizana ndi zinthu zomvetsa chisoni zomwe zawachitikira pamoyo wawo, angawachititse kuyamba kuchita zinthu zodzipweteka, kuphatikizapo kudzivulaza. Wachinyamata amene amaona kuti anthu amamusala ndiponso kuti palibe amene angalankhule naye, akhoza kuyamba kudzivulaza kuti apezeko mpumulo. Komabe, mpumulo uliwonse umene ungaoneke ngati wabwera chifukwa chodzivulaza umakhala wosakhalitsa. Pakapita nthawi yochepa mavutowo amabweranso, ndipo zikatero amayambiranso kudzivulaza.
Nthawi zambiri anthu amene amadzivulaza amafuna kusiya koma zimawavuta kwambiri kuti achite zimenezi. Kodi anthu ena akwanitsa bwanji kusiya kudzivulaza? Tidzakambirana zimenezi mu nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” yakuti “Kodi Ndingasiye Bwanji Kudzivulaza?” mu Galamukani! ya February 2006.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Mayina ena mu nkhani ino tawasintha.
^ ndime 6 Kudzivulaza n’kosiyana ndi kuboola thupi kapena kudzidinda chidindo. Nthawi zambiri anthu amaboola thupi kapena kudzidinda chidindo chifukwa chotsatira mafashoni osati chifukwa choti ali ndi vuto la m’maganizo. Onani Galamukani! ya August 8, 2000, tsamba 16 ndi 17.
^ ndime 9 Lemba la Levitiko 19:28 limati: “Musamadzicheka matupi anu chifukwa cha akufa.” Mwambo wachikunja umenewu, umene mwina cholinga chake chinali kusangalatsa milungu imene ankakhulupirira kuti imasamalira anthu akufa, ndi wosiyana ndi chizolowezi chodzivulaza chomwe tikuchifotokoza m’nkhani ino.
ZOTI MUGANIZIRE
▪ N’chifukwa chiyani achinyamata ena amayamba kudzivulaza?
▪ Poti mwawerenga nkhaniyi tsopano, kodi njira zina zabwino zochepetsera kuvutika maganizo zomwe mungaziganizire ndi ziti?
[Mawu Otsindika patsamba 11]
“Ngakhale m’kuseka mtima uwawa.”—Miyambo 14:13
[Mawu Otsindika patsamba 11]
“Nthawi zambiri, anthu amenewa amakhala akufuna kuchotsa ululu wokhawo basi, osati miyoyo yawo”
[Mawu Otsindika patsamba 12]
Tikukhala mu “nthawi zowawitsa.”—2 Timoteo 3:1