Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kudalira Baibulo Kuti Lizititsogolera?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kudalira Baibulo Kuti Lizititsogolera?

Zimene Baibulo Limanena

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kudalira Baibulo Kuti Lizititsogolera?

“Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero.”—2 Timoteo 3:16.

MUKAFUNA malangizo pamoyo wanu, kodi mumapita kwa ndani? Masiku ano kuli malangizo ambirimbiri pafupifupi pa nkhani iliyonse. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amadalira Baibulo kuti liziwatsogolera, lomwe linalembedwa kalekale.

Komabe, anthu ena ambiri amaona kuti Baibulo n’losathandiza, makamaka masiku ano pamene anthu adziwa zambiri ndiponso kuli luso la zopangapanga lamakono. Aphunzitsi ndi asayansi ena otchuka amakhulupirira kuti Baibulo n’losathandiza masiku ano. Kodi zimenezi n’zoona? Popeza masiku ano munthu akhoza kupeza malangizo mosavuta, n’chifukwa chiyani angafune kudalira Baibulo?

Buku la Choonadi

Panthawi inayake Yesu Kristu akupuma pachitsime analankhula ndi mkazi winawake wachisamariya. Anamuuza kuti: “Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira Iye ayenera kum’lambira mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) Mawu amenewa akusonyeza kuti pali kulambira kumene Mulungu amakuvomereza. Kuti tilambire m’choonadi, kulambira kwathu kuyenera kugwirizana ndi zimene Mulungu wanena m’Baibulo zokhudza iyeyo. M’Mawu a Mulungu muli choonadi.—Yohane 17:17.

Komabe, pali zipembedzo zambiri zimene zimati zimakhulupirira Baibulo, ndipo chilichonse chimaphunzitsa zosiyana ndi chinzake. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri amasokonezeka akafuna kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni. Kodi Yesu ndi Mulungu, kapena ndi Mwana wa Mulungu? Kodi munthu akafa amakhala ndi moyo kwinakwake kapena ayi? Kodi helo ndi malo enieni a moto kumene anthu amakazunzidwa akafa? Kodi Satana ndi munthu weniweni? Kodi Mkristu amafunika kukhala munthu wotani? Kodi zochita ndi zoganiza zathu Mulungu ali nazo ntchito? Kodi ngati anthu amakondanadi ndiye kuti akhoza kumagonana asanakwatirane? Kodi kumwa zakumwa zoledzeretsa n’kulakwa? * Zipembedzo zosiyanasiyana zimati zimaphunzitsa zoona pa nkhani zimenezi. Koma nthawi zambiri zimene chipembedzo chimodzi chimaphunzitsa zimakhala zosemphana ndi zimene chipembedzo china chikuphunzitsa. N’zosatheka kuti zonse zikhale zoona.—Mateyu 7:21-23.

Choncho, kodi mungadziwe bwanji zoona zenizeni zokhudza Mulungu ndi kulambira kumene amasangalala nako? Tiyeni tiyerekezere kuti mwauzidwa kuti mukufunika kuchitidwa opaleshoni chifukwa muli ndi matenda enaake aakulu. Kodi mungatani? Ngati n’kotheka, mungafufuze mosamala kwambiri kuti mupeze dokotala wabwino kwambiri wodziwa kuchita opaleshoni imeneyo. Mungafufuze za maphunziro ake, kutalika kwa nthawi yomwe wagwira ntchito imeneyi, ndipo kenako mungalankhule naye. Pomaliza pake, mutakhulupirira kuti ndi wodziwadi bwino ntchito yake kuposa dokotala wina aliyense mogwirizana ndi zomwe mwafufuza, mungamulole kuti akuchiteni opaleshoni. Ena mwina angakhale ndi maganizo osiyana ndi anu pa nkhani imeneyi. Koma inuyo mungakhale ndi zifukwa zabwino zokhulupirira dokotala ameneyu.

Mwanjira yomweyo, mutafufuza mosamala ndiponso moona mtima umboni umene ulipo, mukhoza kuyamba kukhulupirira Mulungu ndi Baibulo. (Miyambo 2:1-4) Pofunafuna mayankho a mafunso okhudza kulambira kumene Mulungu amavomereza, muli ndi chosankha. Mukhoza kudalira maganizo ndi ziphunzitso zotsutsana za anthu, kapena mukhoza kuona zimene Baibulo limanena.

N’lolondola ndi Lothandiza

Mukafufuza mosamala m’Baibulo, mupeza umboni wochuluka wosonyeza kuti “lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa.” * (2 Timoteo 3:16, 17) Mwachitsanzo, m’Baibulo muli maulosi ambiri ofotokozedwa mwatsatanetsatane. Zimene zachitika m’mbiri zimasonyeza kuti maulosiwa anakwaniritsidwa. (Yesaya 13:19, 20; Danieli 8:3-8, 20-22; Mika 5:2) Ngakhale kuti Baibulo si buku la sayansi, likamanena nkhani za sayansi limanena zolondola. Limanena zinthu zokhudza chilengedwe ndi thanzi labwino zimene zinalembedwa zaka masauzande ambiri asayansi asanazitulukire.—Levitiko 11:27, 28, 32, 33; Yesaya 40:22.

Komanso, Baibulo limatithandiza kusankha zinthu mwanzeru. Lili ndi malangizo ambirimbiri othandiza okhudza zochitika m’banja, thanzi lanu, mmene mungakhalire wosangalala, malonda, ndi zinthu zina zochitika tsiku ndi tsiku. Lemba la Miyambo 2:6, 7 limati: “Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake; Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni.” Mukamadalira Baibulo kuti likutsogolereni, mungazindikire bwino zinthu, n’kumatha “kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”—Ahebri 5:14.

Mawu a Mulungu amatithandizanso kumvetsa cholinga cha moyo. (Yohane 17:3; Machitidwe 17:26, 27) Amafotokoza tanthauzo la zomwe zikuchitika padzikoli. (Mateyu 24:3, 7, 8, 14; 2 Timoteo 3:1-5) M’Baibulo Mulungu amafotokoza momwe adzachotsere kuipa padziko pano n’kuthandiza anthu kukhala ndi thanzi labwino ndiponso moyo wosatha.—Yesaya 33:24; Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3, 4.

Anthu ambiri adzionera okha kuti Baibulo ndi bukudi lodalirika la malangizo othandiza. Ofalitsa magazini ya Galamukani! akukupemphani kuti muziwerenga nkhani zakuti “Zimene Baibulo Limanena,” zomwe zimatuluka m’magazini iliyonse ya Galamukani! Mukatero, mungapeze umboni wina wosonyeza kuti Baibulo lilidi ndi malangizo abwino kwambiri kuposa malangizo ena alionse oti muzitsatira pamoyo wanu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Nkhani zakuti “Zimene Baibulo Limanena,” zomwe zimatuluka nthawi zonse mu Galamukani! zidzayankha mafunso amenewa ndi ena m’tsogolo muno.

^ ndime 12 Kuti mupeze umboni wosonyeza kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu, onani buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

Kodi Mulungu amavomereza kulambira kotani?—Yohane 4:24.

▪ Kodi muyenera kutani kuti mupindule ndi nzeru za Mulungu?—Miyambo 2:1-4.

▪ Kodi Baibulo lili ndi malangizo otani othandiza?—Ahebri 5:14.