Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ Mu 2000, akuti padziko lonse anthu 8.3 miliyoni anayamba kudwala chifuwa chachikulu cha TB, ndipo anthu pafupifupi mamiliyoni awiri odwala chifuwachi anamwalira. Pafupifupi onsewo anali a m’mayiko osauka.—MEDICAL JOURNAL OF AUSTRALIA.
▪ “Panopo, pali ana 10 miliyoni omwe ali ndi kachilombo ka HIV, ndipo pa anthu 4.9 miliyoni omwe amatenga kachilomboka chaka ndi chaka padziko lonse, oposa theka ndi a zaka zapakati pa 15 ndi 24.”—UNITED NATIONS POPULATION FUND.
▪ Makamera a mumlengalenga anajambula mbalame zina za kunyanja zokhala ngati abakha zikuuluka kuzungulira dziko lonse lapansi. Mbalame yaliwiro kwambiri inauluka kuzungulira dziko lonse masiku 46 okha.—MAGAZINI YA SCIENCE, U.S.A.
▪ “Pa ola lililonse, dziko lonse limagwiritsa ntchito ndalama zoposa madola 100 miliyoni posamalira asilikali, ndiponso pogula ndi kusamalira zida za nkhondo.”—VITAL SIGNS 2005, WORLDWATCH INSTITUTE.
Kodi Chiwawa Chochitira Atsogoleri Azipembedzo Chikuchuluka?
Mu 2005, nyuzipepala ina ya ku London ya Daily Telegraph inati: “Kukhala wansembe ndi imodzi mwa ntchito zoopsa kwambiri ku [Britain].” Kafukufuku wina amene boma kumeneko linachita mu 2001 anasonyeza kuti atsogoleri azipembedzo pafupifupi atatu pa anayi alionse amene anafunsidwa pa kafukufukuyo anali atachitiridwapo za chipongwe kapena kumenyedwa, zaka ziwiri m’mbuyo mwake. Kuyambira mu 1996, kwaphedwa atsogoleri azipembedzo okwana asanu ndi awiri. M’tawuni ina, ya Merseyside, “m’malo olambiriramo okwana 1,400, mwakhala mukuchitika ndewu, kubedwa, ndiponso kuotcherana katundu pafupifupi tsiku lililonse.”
Pali Mitundu Yambiri ya Zinyama ndi Zomera
Ngakhale kuti nkhalango zachilengedwe za m’madera otentha zikuwonongedwa, “m’katikati mwa chilumba cha Borneo muli mitundu yambiri ya zinyama ndi zomera,” inatero magazini ya The New York Times. Malinga ndi zomwe ananena a World Wildlife Fund, kuyambira mu 1994 mpaka kudzafika mu 2004, pachilumbachi, chomwe chimayang’aniridwa ndi mayiko a Brunei, Indonesia, ndi Malaysia, akatswiri a sayansi ya zamoyo anapezapo mitundu yatsopano yokwana 361 ya zomera ndi zinyama. Mwa zina anapezapo mitundu yatsopano 260 ya tizilombo, 50 ya zomera, 30 ya nsomba, 7 ya achule a m’masamba, 6 ya abuluzi, 5 ya nkhanu, 2 ya njoka, ndiponso mtundu umodzi wa achule. Komabe, nkhalango za m’katikati mwa chilumbachi zikhoza kuwonongeka ngati anthu apitiriza kudula mitengo mwachisawawa. Izi zikuchitika chifukwa choti anthu akufuna kwambiri mitengo yolimba ya m’nkhalangozi ndi mitengo yopangira mphira komanso akufuna mafuta a mitengo ya mgwalangwa.
Kukhulupirira Malodza Kukufala
A bungwe lina lochita kafukufuku la ku Germany, la Allensbach, anati: “Ngakhale m’nyengo inoyo yomwe luso la zopangapanga ndi sayansi zapita patsogolo kwambiri, anthu ambiri akukhulupirirabe malodza.” Kafukufuku wina amene anachitika nthawi yaitali anasonyeza kuti “anthu akupitiriza kukhulupirira mwayi kapena tsoka, ndipo panopa ndiye zafala kwambiri kusiyana ndi mmene zinalili zaka 25 zapitazo.” M’ma 1970 anthu 22 pa 100 alionse ndiwo ankakhulupirira kuti pali kukhudzana kulikonse pakati pa nyenyezi za mchira ndi moyo wawo. Lero, anthu 40 pa 100 alionse ndiwo amakhulupirira zimenezi. Masiku ano pa anthu achikulire atatu alionse, mmodzi yekha ndiye amakaniratu zokhulupirira malodza. Kafukufuku wina amene anachita pakati pa anthu 1,000 ophunzira m’mayunivesite ku Germany anasonyeza kuti mmodzi mwa ophunzira atatu alionse amakhulupirira zithumwa zimene amayenda nazo m’galimoto kapena ku makiyi awo.
Madzi Oundana a ku Antarctic Akusungunuka
Nyuzipepala ya Clarin, ya ku Buenos Aires, inati: “M’zaka 50 zapitazi, madzi ambiri oundana a ku Antarctic asungunuka,” ndipo izi zachitika mofulumira kwambiri kusiyana ndi mmene akatswiri ena anali kuganizirira m’mbuyomu. Pantchito yoyamba yaikulu kwambiri yoyesa madzi oundana anapeza kuti derali n’lofundirapo ndi madigiri seshasi 2.5 kusiyana ndi mmene linalili zaka 50 zapitazo. A David Vaughan a bungwe la British Antarctic Survey anati kusintha kwa nyengo ndiko kwachititsa kuti madziwa asungunuke kwambiri chonchi. Iwo anafunsa kuti: “Kodi anthu ndiwo akuchititsa vutoli?” Poyankha anati: “Sitinganene mwatchutchutchu, koma tatsala pang’ono kutulukira yankho la funso lofunika limeneli.”