Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali Mulungu Mmodzi Yekha Woona?

Kodi Pali Mulungu Mmodzi Yekha Woona?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Pali Mulungu Mmodzi Yekha Woona?

MOLEKE, Asitaroti, Baala, Dagoni, Merodake, Zeu, Herme, ndi Artemi ndi ina mwa milungu yaimuna ndi yaikazi imene inatchulidwa mayina m’Baibulo. (Levitiko 18:21; Oweruza 2:13; 16:23; Yeremiya 50:2; Machitidwe 14:12; 19:24) Komabe, Yehova yekha ndi amene amatchedwa Mulungu Wamphamvuyonse m’Malemba. M’nyimbo yokondwerera kuti apambana, Mose anatsogolera anthu ake poimba kuti: “Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova?”—Eksodo 15:11.

N’zachionekere kuti Baibulo limaika Yehova pamwamba pa milungu ina yonse. Koma kodi milungu ina yochepayi imagwira ntchito yanji? Kodi milungu imeneyi, ndiponso milungu ina yosawerengeka imene anthu akhala akulambira kuyambira kalekale, ndi milungu yeniyeni yotsikirapo mphamvu poyerekezera ndi Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova?

Milungu Ina Ndi Yopeka Chabe

Baibulo limati Yehova ndiye Mulungu woona yekha. (Salmo 83:18; Yohane 17:3) Mneneri Yesaya analemba mawu a Mulungu mwiniwakeyo pamene anati: “Ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.”—Yesaya 43:10, 11.

Milungu ina yonseyo sikuti yangokhala chabe milungu yotsikirapo poyerekezera ndi Yehova. Yambiri mwa iyo kulibeko, anthu anangopeka zoti iliko. Baibulo limati milungu imeneyi ndi “ntchito ya manja a anthu, . . . yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.” (Deuteronomo 4:28) Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti Yehova ndiye Mulungu woona yekha.

Choncho n’zosadabwitsa kuti Malemba amaletseratu kulambira mulungu wina aliyense kupatulapo Yehova. Mwachitsanzo, mu lamulo loyamba la Malamulo Khumi amene anaperekedwa kwa Mose, mtundu wakale wa Israyeli unauzidwa kuti usamalambire mulungu wina aliyense kupatula Yehova. (Eksodo 20:3) Chifukwa chiyani?

Choyamba, kupembedza mulungu amene kulibe n’komwe ndi mwano waukulu kwa Mlengi. Baibulo limati olambira milungu yonyengayi “anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo.” (Aroma 1:25) Nthawi zambiri milungu yopekayi imaimiridwa ndi mafano opangidwa ndi zinthu zopezeka m’chilengedwe, monga zitsulo kapena mitengo. Milungu yambiri imakhudzana kwambiri ndi zinthu zina za m’chilengedwe, monga mabingu, nyanja zamchere, ndi mphepo. Choncho n’zachionekere kuti kupembedza milungu iliyonse yabodza yoteroyo n’kuchitira Mulungu Wamphamvuyonse chipongwe chachikulu.

Mlengi amanyansidwa kwambiri ndi milungu yonyenga ndiponso mafano oimira milunguyo. Komabe, mawu a Mulungu osonyeza kuipidwa kwake amapita makamaka kwa anthu amene amapembedza milungu yonyengayi. Maganizo ake anafotokozedwa mwamphamvu m’mawu awa: “Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golidi, ntchito ya manja a anthu. Pakamwa ali napo koma osalankhula; maso ali nawo, koma osapenya; makutu ali nawo, koma osamva; inde, pakamwa pawo palibe mpweya. Akuwapanga adzafanana nawo; inde, onse akuwakhulupirira.”—Salmo 135:15-18.

Palinso chifukwa china chimene Baibulo limaletsera kwambiri kulambira munthu kapena chinthu china chilichonse kupatulapo Yehova Mulungu. Kuchita zimenezi n’kungowononga nthawi ndi mphamvu. Mneneri Yesaya anafotokoza bwino zimenezi pamene anati: “Ndani wapanga mulungu, kapena kusungunula fano losema losapindula kanthu?” (Yesaya 44:10) Baibulo limanenanso kuti “milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano” osapindulitsa. (Salmo 96:5) Milungu yonyenga n’njachabechabe, ndipo kulambira chinthu chachabechabe n’kopanda phindu.

Yesu, Angelo, Ndiponso Mdyerekezi

Malemba nthawi zina amatchula anthu ngati milungu. Komabe, tikafufuza mosamala timaona bwinobwino kuti mawu akuti “mulungu” mu nkhani zoterozo satanthauza kuti anthu amenewa ndi milungu yoti izilambiridwa. M’malo mwake, m’zinenero zoyambirira zomwe Baibulo linalembedwa, mawu akuti “mulungu” ankagwiritsidwanso ntchito kufotokoza munthu wamphamvu kapena wa thupi lofanana ndi Mulungu kapena amene amachita zinthu mogwirizana ndi Mulungu Wamphamvuyonse.

Mwachitsanzo mavesi ena m’Baibulo amati Yesu ndi mulungu. (Yesaya 9:6, 7; Yohane 1:1, 18) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yesu ayenera kulambiridwa? Yesu mwiniwakeyo anati: “Ambuye [Yehova] Mulungu wako uzim’gwadira, ndipo Iye yekhayekha uzim’tumikira.” (Luka 4:8) Mwachionekere, ngakhale kuti Yesu ndi wamphamvu kwambiri ndiponso ndi wangati Mulungu, Baibulo silinena kuti tizimulambira.

Komanso, palibe paliponse m’Malemba pamene anthu analimbikitsidwa kupembedza angelo. Ndipotu, pa nthawi inayake, mtumwi wokalamba Yohane anachita kakasi kwambiri ndi mngelo moti anawerama kuti alambire mngeloyo. Koma mngeloyo anayankha kuti: “Tapenya, usatero; . . . lambira Mulungu.”—Chivumbulutso 19:10.

Mtumwi Paulo anati Mdyerekezi ndiye “mulungu wa nthawi ino ya pansi pano.” (2 Akorinto 4:4) Monga “mkulu wa dziko ili lapansi,” Mdyerekezi walimbikitsa anthu kulambira milungu yonama yambirimbiri. (Yohane 12:31) Choncho, anthu akamalambira milungu yopangidwa ndi anthu, kwenikweni amakhala akulambira Satana. Koma Satana si mulungu woti tizimulambira. Iye anadziika yekha pa ulamuliro, anachita kulanda ulamuliro wa mwiniwake. M’tsogolomu, iyeyu, komanso mitundu yonse ya kulambira konyenga, idzachotsedwa. Zimenezi zikadzachitika, anthu onse, inde, chilengedwe chonse, chidzavomereza mpaka muyaya kuti Yehova ndiye Mulungu woona yekha wamoyo.—Yeremiya 10:10.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani za kulambira mafano?—Salmo 135:15-18.

▪ Kodi Yesu ndi angelo ayenera kupembedzedwa ngati milungu?—Luka 4:8.

▪ Kodi Mulungu woona yekha ndi ndani?—Yohane 17:3.

[Zithunzi pamasamba 28, 29]

Mafano kuchokera kumanzere kupita kumanja: Mariya ku Italy; mulungu wa chimanga wa a Maya ku Mexico ndi ku Central America; Asitaroti ku Kanani; fano la za matsenga ku Sierra Leone; Buda ku Japan; mulungu wa a Aztec wotchedwa Chicomecóatl ku Mexico; mulungu wangati mbalame wotchedwa Horus ku Egypt; Zeu ku Greece

[Mawu a Chithunzi]

Maize god, Horus falcon, and Zeus: Photograph taken by courtesy of the British Museum