Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ukalamba Ungakhaledi Wosangalatsa?

Kodi Ukalamba Ungakhaledi Wosangalatsa?

Kodi Ukalamba Ungakhaledi Wosangalatsa?

NTHAWI ili 6:30 m’mawa, ndipo kunja kukuzizira kwambiri ku Soweto, m’dziko la South Africa. Evelyn ayenera kudzuka pabedi tsopano. * Popeza alibe chilichonse chotenthetsa m’nyumba, kudzuka pabedi n’kopweteka kwambiri.

Pang’ono ndi pang’ono akutsitsa pansi miyendo yake yodwala nyamakazi, uku akumva ululu woopsa. Kenaka akukhala tsonga m’mphepete mwa bedilo n’kudikira kaye. Patapita kanthawi, miyendo yakeyo ikusiya kupweteka. Kenaka Evelyn akulumira mano n’kuimirira ndipo akubuula ndi ululu. Manja ali mchiuno, monga momwe ‘dzombe limakokera miyendo yake,’ Evelyn akuyenda pang’onopang’ono kupita kubafa.—Mlaliki 12:5. *

‘Koma ndiye ndayesetsatu!’ akutero Evelyn, chifukwa waonanso tsiku latsopano, komanso watha kudzuka n’kuyamba kuyenda ngakhale kuti thupi lake likupweteka.

Komabe, iye ali ndi nkhawa ina. Evelyn akuti: “Ndimaopa kuti mwina m’tsogolo muno ndidzazunguzika maganizo.” Nthawi zina amataya makiyi, koma pakadali pano amathabe kuganiza bwinobwino. Evelyn anati: “Ndimangopemphera kuti ndisadzasokonezeke maganizo ngati mmene nkhalamba zina zimachitira.”

Evelyn ali mtsikana sankaganizako n’komwe za ukalamba. Koma mwadzidzidzi, anazindikira kuti zaka zambirimbiri zadutsa, ndipo panopa thupi lake likamapweteka nthawi zonse limamukumbutsa kuti ali ndi zaka 74.

Anthu ena amene amakhala moyo wofewerapo poyerekezera ndi wa Evelyn ndiponso amene sakudwala matenda alionse aakulu komanso alibe nkhawa iliyonse, angamaonedi kuti zaka zawo zaukalamba n’zosangalatsa. Mofanana ndi kholo lakale Abrahamu, akhoza kufika ‘ukalamba wabwino, n’kukhala nkhalamba ya zaka zambiri.’ (Genesis 25:8) Ena amakhala ndi “masiku a mavuto” ndipo amangoti: “Ndilibenso zondisangalatsa.”—Mlaliki 12:1, Malembo Oyera.

Kodi inuyo ukalamba mumauona bwanji? Kodi mavuto ena amene okalamba amakumana nawo ndi otani? Kodi kuzunguzika maganizo ndi mbali ya ukalamba? Kodi munthu angatani kuti akhale ndi mtendere wa mumtima mu ukalamba wake?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina ena mu nkhani zino tawasintha.

^ ndime 3 Anthu adziwa kwa nthawi yaitali kuti ndime imeneyi m’buku lakale la m’Baibulo la Mlaliki ndi ndakatulo yofotokoza bwino mavuto amene munthu amakumana nawo akamakalamba.