Kukaona Malo Opangira Ziwalo
Kukaona Malo Opangira Ziwalo
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU NEW ZEALAND
NDINALI ndi zolinga ziwiri zimene ndinakonzera ulendo wopita ku Malo Opangira Ziwalo ku Wellington, m’dziko la New Zealand. Choyamba, mwendo wanga wochita kupanga unkafunika kuukonza mwina ndi mwina. Chachiwiri chinali kufuna kukaona malowa ndi kudziwa bwino zomwe zimachitika popanga ziwalo.
Dokotala wanga wa pamalowa anandikomera mtima n’kuvomera pempho langa loti ndione nawo malowo. Zimene ndinaona kumeneko zinandithandiza kwambiri. Ndinayamba kumvetsa luso ndiponso khama lomwe akatswiri a ntchito yopanga ndi kuikirira anthu ziwalo amafunika kukhala nalo.
Kodi Amapanga Motani Mwendo?
Ambiri mwa anthu ofuna chithandizo amene amabwera ku malowa amakhala oti akufuna kuti awapangire mwendo. Choyamba, amavundikira mbali yotsala ya mwendo wodukawo. Akatero, amagwiritsa ntchito pulasitala kupanga chinthu chofanana ndendende ndi mbali ya mwendo yomwe inatsalayo. Kenaka amagwiritsa ntchito chimene apangacho kukonzera dzenje lomwe amalumikizirako mwendo watsopano. Akatero amayamba ntchito yopanga mwendo wogwira ntchito bwinobwino woti ulowe m’malo mwa mwendo womwe unadukawo. Masiku ano amagwiritsa ntchito kompyuta poyeza saizi ya mwendo wotsalawo ndipotu imeneyi ndi njira yamakono ndiponso yofulumira kwambiri. Kenako, makina amapanga chinthu chofanana ndendende ndi mbali yotsala ya mwendo woduka uja.
Nditatha kuona njira zomwe amagwiritsa ntchito popanga miyendo pa malowa, anandionetsa zinthu zopanga kale zomwe amapangira ziwalo, zomwe anaitanitsa kunja kwa dzikoli. Chimodzi mwa zitsanzo zochititsa chidwi kwambiri ndi bondo loyendera madzi lomwe amalilowetsa ku dzenje la pulasitiki ndipo dzenjeli amatha kulisintha politenthetsa kuti likhale momwe munthuyo akufunira. Mabuku a zithunzi za zipangizo ngati zimenezi amapezeka padziko lonse m’malo osiyanasiyana.
Akamamaliza kupanga mwendo amaonetsetsa kuti dzenje loulumikizira ku mbali yotsala ya mwendo wodukawo, bondo lake, khungu lake, ndiponso phazi lake zalumikizana bwino kuti munthu azitha kuyenda nawo bwinobwino. Kenako, amakonza chipulasitiki chokutira mwendowo. Chipulasitikichi chimabisa zitsulo za mwendowo. Pomaliza amaonetsetsa kuti chipulasitikicho chikuoneka mofanana ndi mbali yotsala ya mwendo wodukawo.
Wodwala akauzolowera mwendowu, amam’patsa tsiku loti adzaonane ndi dokotala wochita maopaleshoni a mafupa amene amachita kubwera pa malo opangira ziwalowa. Mwa kutero, katswiri
wodziwa za mafupayu amatha kutsimikizira kuti mwendo watsopanowo uzigwiradi ntchito bwinobwino.Ana ndiponso Akatswiri a Masewera
Popitiriza ulendo wanga woona malowa, ndinachita chidwi ndi mtsikana wina wamng’ono. Mtsikanayu sanachite manyazi kutionetsa mbali yomwe inatsala ya chiwalo chake chomwe chinaduka ndiponso chiwalo chomwe anam’pangira. Kenako ndinamuona akudumphadumpha, akuchita kuonekeratu kuti alibe nkhawa iliyonse.
Ndinachita chidwi kwambiri ndi zimene dokotala wanga ananena zokhudza ana amene aduka chiwalo. Anandisonyeza kadzanja kakang’ono n’kundifotokozera kuti ziwalo zoterezi amaveka ana ang’onoang’ono a miyezi mwina isanu ndi umodzi. N’chifukwa chiyani amatero? Cholinga chimakhala choti anawo aphunzire kuti m’tsogolo adzathe kugwiritsa ntchito dzanja kapena mkono wochita kupanga. Anafotokoza kuti, popanda kuchita zimenezi, mwanayo akamakula amaphunzira kugwiritsa ntchito mkono umodzi ndipo m’tsogolo mwake angathe kudzavutika kuphunzira kugwiritsa ntchito mikono iwiri.
Ndinauzidwa kuti nthawi inayake chaposachedwapa, kampani ina ya ku Ulaya inatumiza ku Sydney, m’dziko la Australia zipangizo za ziwalo zochita kupanga zoti akatswiri a masewera osiyanasiyana adzagwiritse ntchito pa masewera a Olimpiki a anthu olumala. Zipangizozi ankapereka ulele kwa ochita masewerawo, ndipo akatswiri opanga ndi kuikirira ziwalo zoterezi, ena ochoka ku New Zealand, anali chire kuti athandize opikisanawo m’kati mwa masewerawo.
Pali ziwalo zina zomwe amapangira akatswiri a masewera basi. Anandionetsa chitsanzo cha zipangizo zoterezi. Anandionetsa zipangizo za phazi ndi kakolo wake lopangidwa ndi zinthu zapadera zopangitsa kuti lizichita zinthu mofanana ndendende ndi phazi lachilengedwe.
Mmene Ntchitoyi Yapitira Patsogolo Masiku Ano
Kodi m’tsogolomu zinthu zidzakhala bwanji pankhani yopanga ziwalo? Dokotala wanga anandifotokozera za mwendo wina woyendetsedwa ndi kompyuta womwe panopo uli ndi munthu mmodzi yekha m’dziko la New Zealand. Zikuoneka kuti chifukwa cha tizitsulo tina tomwe tili m’kati mwake, mwendowu umatha kudziwa ukakhudzidwa. Chifukwa cha zimenezi mwendo umenewu umayenda mwachibadwa.
M’mayiko ena, madokotala aluso kwambiri akuyesera njira ina. Njirayi ndi yomuika munthu kachitsulo kapadera ku mbali yotsala ya chiwalo chomwe adula, ndipo pa kachitsulo kameneka m’pamene amadzatha kumangirirapo chiwalo chochita kupanga. Zikatero, podzamupangira chiwalo safunikanso kupanga chipulasitala kapena dzenje lovekerako chiwalocho.
Panopa akufufuzanso njira zolumikizira tizitsulo ta m’ziwalo zochita kupanga ku minyewa yopita ku ubongo, zomwe zingathandize munthu kuyendetsa chiwalocho akangoganiza kutero. Ku United States ndi ku mayiko ena, ayesapo kupatsa anthu manja a ena, koma anthu amasiyana maganizo pankhaniyi. Munthu amene amupatsa dzanja la munthu wina amafunika kuti moyo wake wonse azimwa mankhwala oti thupi lake lisakane chiwalo cha munthu wina chomwe am’patsacho.
Pankhani yopanga mikono, panopa akugwiritsa ntchito njira inayake yomwe imathandiza kuti tizitsulo tizilandira mauthenga ochokera ku minofu ya mkono womwe unatsala. Minyewa yolandira ndi kutumiza mauthenga otere imakhala ikugwirabe ntchito m’mbali yotsala ya mkono wodukawo.
Batire limakuza mauthengawo kuti aziyendetsa tizitsulo ta m’chiwalo chochita kupangacho. Panopa atulukira luso lamakono kwambiri logwiritsa ntchito kompyuta kuti chiwalocho chizigwirizana bwino ndi munthu aliyense payekhapayekha.Podabwa ndi kupita patsogolo kotereku kwa luso lopanga ziwalo, ndinafunsa dokotala wangayo kuti angafananitse motani kagwiridwe ntchito ka ziwalo zimenezi ndi ka ziwalo zachilengedwe. Sanapite m’mbali, ananenetsa kuti mkono kapena mwendo wachilengedwe sungafanane m’pang’ono pomwe ndi wochita kupanga. Izi zinandipangitsa kuganizira mawu a wamasalmo yemwe anapemphera motere kwa Mlengi wake: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa.”—Salmo 139:14.
[Chithunzi patsamba 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Zithunzi]
Mikono yotha kulandira mauthenga ochokera ku ubongo ili ndi tizipangizo tothandiza kuti ichite zinthu mwamsanga kapena ayi komanso kuti igwire kwambiri chinthu kapena ayi
[Mawu a Chithunzi]
Hands: © Otto Bock HealthCare
[Zithunzi]
M’kati mwa bondo ili, lomwe ndi loyendera kompyuta, muli tizitsulo ta kompyuta ndi mphamvu ya maginito zomwe zimapangitsa kuti lizisinthasintha mogwirizana ndi kayendedwe ka amene wavalayo
[Mawu a Chithunzi]
Knee: Photos courtesy of Ossur
[Chithunzi]
Umu ndi mmene mumaonekera m’kati mwa phazi lochita kupanga ndipo apa tikuona chipulasitiki chakunja ndi kakolo wake
[Mawu a Chithunzi]
© Otto Bock HealthCare
[Mawu a Chithunzi]
© 1997 Visual Language
[Chithunzi patsamba 21]
Kusintha zina ndi zina pa mwendo wochita kupanga
[Chithunzi patsamba 22]
Kuikirira mwendo
[Chithunzi patsamba 23]
Kadzanja kophunzitsira ana aang’ono amene aduka dzanja
[Chithunzi patsamba 23]
Mu 2004 wopambana mpikisano wa Olimpiki wa mamita 100 wa anthu olumala anathamanga masekondi 10.97 ali ndi phazi lopanga ndi kaboni
[Mawu a Chithunzi]
Photo courtesy of Ossur/Photographer: David Biene
[Mawu a Chithunzi patsamba 21]
© Otto Bock HealthCare