Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupirira Mavuto a Ukalamba

Kupirira Mavuto a Ukalamba

Kupirira Mavuto a Ukalamba

“ZAKA zathu zonse zikwanira makumi asanu ndi awiri, ndipo ngati tili olimba, makumi asanu ndi atatu. Ndipo zambiri mwa zimenezo ndizo zakusauka ndi zopanda pake; chifukwa zimapita msanga, ndipo ife timauluka.” (Salmo 89:10, 11, Malembo Oyera [90:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu]) Ndakatulo yakale imeneyi, yomwe inalembedwa zaka 3,000 zapitazo, ikutsimikizira kuti ukalamba wakhala ukuvutitsa anthu kuyambira kalekale. Ngakhale kuti azachipatala apita patsogolo kwambiri, zinthu zina zochitika pa ukalamba zimakhalabe ‘zosautsa ndi zopanda pake.’ Kodi n’zinthu ziti zochitika pa ukalamba zimene zimakhala zotero, ndipo kodi anthu ena akulimbana bwanji ndi mavuto amenewa?

Okalamba Koma Oganizabe Bwinobwino

“Chimene ndimaopa kwambiri ndi kusokonezeka maganizo,” anadandaula motero Hans, wa zaka 79. Mofanana ndi okalamba ambiri, Hans anayamba kuda nkhawa ataona kuti akumaiwalaiwala zinthu. Iye ankaopa kuti mwina akutaya chimene wolemba ndakatulo wina wakale anachitcha “mbale yagolidi,” yomwe ndi ubongo ndi zonse zomwe umakumbukira zamtengo wapatali. (Mlaliki 12:6) Hans anafunsa kuti, “Kodi nthawi zonse munthu akamakalamba amasokonezeka maganizo?”

Ngati nanunso, mofanana ndi Hans, mwaiwalapo mayina a anthu, kapena mwadzifunsapo ngati kuiwala koteroko ndi chiyambi cha kusokonezeka maganizo, khazikani mtima pansi. Anthu a misinkhu yonse amatha kuiwala zinthu, ndipo kusintha kwa kagwiridwe ntchito ka ubongo kumene kumachitikira anthu okalamba nthawi zambiri sikukhala chifukwa cha matenda a maganizo. * Ngakhale kuti anthu akamakalamba amatha kuiwala mwa apo ndi apo, “okalamba ambiri amafika pa mapeto pa moyo wawo akuthabe kuganiza bwinobwino,” analemba choncho Dr. Michael T. Levy, tcheyamani wa sayansi ya khalidwe la anthu pa chipatala cha yunivesite ya Staten Island ku New York.

N’zoona kuti achinyamata nthawi zambiri amakumbukira zinthu msanga kusiyana ndi okalamba. Koma katswiri wina wa za ubongo dzina lake Richard Restak anati: “Popanda kuganizira za nthawiyo, anthu okalamba nthawi zambiri amakumbukira bwino zinthu mofanana ndi achinyamata.” Ndipotu, ngati aphunzitsidwa bwino, anthu okalamba amatha kupitirizabe kuphunzira, kukumbukira zinthu, ndiponso ngakhale kupita patsogolo pa zinthu zina.

Kuvutika Kukumbukira Zinthu Ndiponso Matenda Oti Angachiritsidwe

Koma bwanji ngati munthu akuvutika kwambiri kukumbukira zinthu? Ngakhale zitakhala choncho, munthuyo si kuti nthawi yomweyo aganize kuti ali ndi matenda a maganizo. Matenda ena ambirimbiri oti munthu angathe kuchira, amene anthu amadwala akakalamba akhoza kuchititsa munthu kuvutika kukumbukira zinthu ndiponso kusokonezeka maganizo mwadzidzidzi. Matenda oterowo nthawi zambiri anthu amawatcha molakwika kuti “ukalamba” kapena “kusokonezeka maganizo.” Nthawi zina ngakhale madokotala amaganiza zimenezi chifukwa cha kusamvetsa bwino zinthu. Zimenezi zimakhala zowachotsera ulemu anthu okalamba, komanso zingawalepheretse kupeza chithandizo choyenera cha mankhwala. Kodi ena mwa matenda amenewa angakhale chiyani?

Kusokonezeka maganizo mwadzidzidzi kungachitike chifukwa cha kuperewera kwa zakudya m’thupi, kuchepa madzi m’thupi, kuchepa magazi, kuvulala m’mutu, matenda a chithokomiro, kuperewera kwa mavitamini, mphamvu ya mankhwala amene munthuyo akumwa, kapena kusokonezeka chifukwa chopita ku malo achilendo. Kuvutika kukumbukira zinthu kungayambe chifukwa cha kupanikizika maganizo kwa nthawi yaitali, ndiponso matenda ena osiyanasiyana amakonda kuchititsa anthu okalamba kusokonezeka maganizo. Matenda ovutika maganizo angayambitsenso okalamba kuvutika kukumbukira zinthu ndi kusokonezeka maganizo. Choncho, Dr. Levy anati “mukaona kuti munthu akusokonezeka maganizo mwamsanga, musangonyalanyaza zimenezi kapena kuganiza kuti ndi matenda a ukalamba ndipo palibe chomwe mungachite.” Atamuyeza munthuyo bwinobwino kuchipatala, akhoza kupeza chifukwa chomwe chikumuchititsa zimenezo.

Zomwe Mungachite Ngati Mukudwala Matenda Ovutika Maganizo

Anthu sanayambe lero kuvutika maganizo. Ngakhale atumiki okhulupirika a Mulungu anavutikapo maganizo. Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, mtumwi Paulo analangiza Akristu anzake kuti: “Limbikitsani amantha mtima,” kapena kuti, ovutika maganizo. (1 Atesalonika 5:14) M’masiku athu ovuta ano, tikufunika kulimbikitsidwa kuposa n’kale lonse. Koma n’zomvetsa chisoni kuti okalamba akamadwala matenda ovutika maganizo nthawi zambiri madokotala sawatulukira matendawa kapena amawasokoneza ndi matenda ena.

Chifukwa cha maganizo olakwika amene anthu ambiri amakhala nawo oti anthu akamakalamba amakhala a ndwii ndiponso okwiyakwiya, anthu ena komanso okalamba eni akewo amaganiza kuti zimenezi ndi mbali ya ukalamba osati zizindikiro za matenda. Koma buku lotchedwa Treating the Elderly linati: “Zimenezi si zoona. Matenda ovutika maganizo pakati pa okalamba si mbali ya ukalamba.”

Kuvutika maganizo kwa nthawi yaitali, osati kungoipidwa chabe kwa kanthawi, ndi nthenda yoopsa yomwe zotsatirapo zake zikhoza kukhala zoipa kwambiri, ndipo siiyenera kunyalanyazidwa. Nthendayi ikakhalitsa, ikhoza kufika poipa kwambiri moti odwala ena amadzipha chifukwa chotaya mtima. Dr. Levy anati kwa anthu okalamba, kumvetsa chisoni kwa nthenda yovutika maganizo n’koti “nthenda yotheka kuchiritsidwa mosavuta pa matenda onse a maganizo imeneyi ndi imenenso ingawaphe mosavuta.” Matendawa akapitirira, wodwalayo angafunike kukalandira chithandizo kwa katswiri wodziwa kuchiza matenda a maganizo. *Marko 2:17.

Anthu amene akuvutika maganizo azikumbukira kuti Yehova “ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Iye “ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka.” (Salmo 34:18) Ndipotu, iye ndi amene kuposa wina aliyense “amatonthoza mtima wopsinjika.”—2 Akorinto 7:6, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

Palibe Chifukwa Chodzionera Ngati Wopanda Ntchito

Zaka zoposa 3,000 zapitazo, Mfumu Davide yokhulupirika inapemphera kuti: “Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.” (Salmo 71:9) Ngakhale m’zaka za m’ma 2000 zino, malingaliro ngati amenewa si achilendo kwa okalamba amene angamaope kuti azionedwa ngati otha ntchito. Kulephera kuchita zinthu chifukwa cha matenda kungachititse munthu kudziona ngati woperewera, ndipo kupumitsidwa ntchito kungachititse munthu kudziona ngati wachabechabe.

Komabe, ngati tilimbikira zinthu zimene tingathe kuchita, m’malo mokhumudwa poganizira za zinthu zimene sitingathenso kuchita, tikhoza kupitirizabe kudziona kuti ndife ofunika. Pa nkhani imeneyi, lipoti lina la bungwe la United Nations linalimbikitsa anthu ‘kupitirizabe kupita patsogolo kudzera m’maphunziro a kusukulu kapena a mtundu wina, kulowa nawo mabungwe ena ake kwanuko, ndi kuchita nawo zinthu zachipembedzo.’ Ernest, wa Mboni za Yehova wina yemwe anali katswiri wophika buledi ku Switzerland, ndipo anapuma pa ntchito, n’chitsanzo chabwino cha munthu amene ‘akupitiriza kupita patsogolo kudzera m’maphunziro.’ Ernest ali ndi zaka za m’ma 70 anaganiza zogula kompyuta n’kuphunzira kuigwiritsa ntchito. Kodi iye anachita zimenezi chifukwa chiyani, pamene anthu ambiri a msinkhu wake amaopa kuphunzira luso lamakono? Iye anafotokoza kuti: “Choyamba, kuti maganizo anga akhalebe ochangamuka pamene ndikukalamba. Ndipo chachiwiri, kuti ndidziwe luso lamakono limene lingandithandize pofufuza zinthu m’Baibulo ndi pa ntchito yanga mu mpingo.”

Kugwira ntchito zothandiza kungapindulitse anthu okalamba m’njira zambiri zofunika: Kumawachititsa kumva kuti ali ndi cholinga m’moyo ndiponso amakhala okhutira, komanso akhoza kumapezerapo kangachepe. Mfumu Solomo yanzeru inanena kuti ndi mphatso ya Mulungu kuti munthu ‘akondwere ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse.’—Mlaliki 3:12, 13.

Kuchita Zomwe Tingathe

Ku madera ambiri, anthu okalamba ndi amene amaphunzitsa anthu zinthu, komanso ndi amene amalangiza anthu pa nkhani zokhudza khalidwe labwino ndi nkhani zauzimu. Iwo amachitira zimenezi mibadwo yotsatizanatsatizana. Mfumu Davide inalemba kuti: “Pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m’mbuyo.”—Salmo 71:18.

Koma bwanji ngati okalamba sangathe kuchita zambiri chifukwa cha matenda kapena zochitika zina? Zimenezi zinakhumudwitsa wa Mboni za Yehova wina wa zaka 79 dzina lake Sarah, amene anauza mkulu wachikristu za mavuto akewo. Mkuluyo anamukumbutsa za mfundo ya m’Baibulo yoti “pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu.” (Yakobo 5:16, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Mkuluyo anafotokoza kuti, “pa zaka zonsezi, mwapanga ubwenzi wolimba kwambiri ndi Mulungu. Panopa mukhoza kutipindulitsa enafe ndi ubwenzi umenewo mukamatipempherera muli panokha.” Iye analimbikitsidwa kwambiri pamene mkuluyo anamuuza kuti, “a Sarah, tikufunikira kwambiri mapemphero anu.”

Monga momwe Sarah anazindikirira, pemphero ndi njira yosangalatsa ndiponso yatanthauzo yomwe anthu okalamba angadziperekere usana ndi usiku kuthandiza ena. (Akolose 4:12; 1 Timoteo 5:5) Komanso, mapemphero oterowo amathandiza okalamba okhulupirika kuyandikira kwa Yehova, “Wakumva pemphero.”—Salmo 65:2; Marko 11:24.

Okalamba ena amene sangachite zambiri koma saumira nzeru zawo ndi katundu wawo amathandiza kwambiri anthu ena ku madera kwawo. Amasonyezadi kuti ‘imvi ndiyo korona wa ulemu, ikapezedwa m’njira ya chilungamo.’—Miyambo 16:31.

Komabe tingafunse kuti: Kodi tingayembekezere zotani m’tsogolomu tikamakalamba? Kodi ndi nzerudi kuyembekezera kukhala ndi moyo wabwino zaka zikamapita?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Ochita kafukufuku ena amanena kuti “pafupifupi anthu 90 pa 100 alionse a zaka zoposa 65 sadwala matenda a maganizo.” Kuti mumve zambiri zokhudza chithandizo cha matenda a maganizo, onani nkhani zokamba za matenda a Alzheimer’s mu Galamukani! ya October 8, 1998.

^ ndime 13 Galamukani! silangiza anthu kuti atsatire njira yakutiyakuti ya chithandizo. Akristu ayenera kuonetsetsa kuti chithandizo chilichonse chimene akulandira sichikutsutsana ndi mfundo za m’Baibulo. Onani nkhani zakuti “Kumvetsetsa Matenda a Maganizo,” mu Galamukani! ya January 8, 2004.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Nthawi zambiri okalamba amaona kuti akusiyidwa m’mbuyo m’dziko lathu lamakono lochita zinthu mofulumirali

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

Mmene Mungathandizire Okalamba

Achitireni Ulemu. “Mkulu usam’dzudzule, komatu um’dandaulire ngati atate; . . . akazi aakulu ngati amayi.”—1 Timoteo 5:1, 2.

Amvetsereni Mwatcheru. ‘Khalani wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.’—Yakobo 1:19.

Achitireni Chifundo. “Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe.”—1 Petro 3:8, 9.

Muzizindikira Pamene Akufunika Kuwalimbikitsa. “Mawu oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.”—Miyambo 25:11.

Muziwaitana Mukamachita Zinthu Zosiyanasiyana. ‘Cherezani alendo.’—Aroma 12:13.

Athandizeni. “Iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pom’mana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? Tiana, tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’choonadi.”—1 Yohane 3:17, 18.

Alezereni Mtima. “Valani . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.”—Akolose 3:12.

Tikamasamalira okalamba, timasonyeza kuti tikulemekeza mfundo za Mulungu, chifukwa Mawu ake amati: ‘Uchitire ulemu munthu wokalamba.’—Levitiko 19:32.

[Chithunzi patsamba 6]

Kuyezedwa bwinobwino kuchipatala kungathandize