Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“N’kabwino Kwabasi!”

“N’kabwino Kwabasi!”

“N’kabwino Kwabasi!”

Ku Brazil, mphunzitsi wina wa jogalafe anachita chidwi kwambiri ndi zinthu zosiyanasiyana zomwe magazini a Galamukani! amaphunzitsa. Iye analemba kuti: “M’magazini amenewa ndimapezamo zinthu zambiri zogwiritsa ntchito pophunzitsa kuposa zomwe ndimapeza m’mabuku ambiri ophunzitsira ana asukulu. Ngakhale kuti ndine wa chipembedzo china, ndikugwirizana kwathunthu ndi mfundo zimene magazini a Galamukani! amalimbikitsa.”

Koma mphunzitsi ameneyu anadzazindikira kuti Galamukani! ndi magazini amodzi okha mwa mabuku ambiri amene Mboni za Yehova zimafalitsa. Iye analemba kuti: “Mwana wa wina sukulu wa sitandade sikisi anandibwereka kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma.’ Ndinachita chidwi kwambiri kuona mmene anakalembera. N’kabwino kwabasi! Ngati anthu, makamaka achinyamata, ali ndi chithunzi cha momwe zinthu zotchulidwa m’Baibulo zinachitikira ndiponso komwe zinachitikira, amatha kumvetsetsa bwino zinthu akamaphunzira Baibulo.”

Iye anapitiriza kuti: “Mabuku anu amapezeka paliponse: m’basi, pakati pa ana asukulu, ngakhalenso pamzere wa anthu ku banki. Ndine wosangalala kwambiri kuona kuti akufikira anthu osowa amene amavutika kwambiri kupeza mabuku abwino. Zikomo kwambiri chifukwa cha ntchito yabwino imene mukuchitayi.”

Kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma’ kakupezeka m’zinenero pafupifupi 80. Kali ndi mapu a kalala ambirimbiri ndi zithunzi zosonyeza madera osiyanasiyana otchulidwa m’Baibulo, makamaka za Dziko Lolonjezedwa pa nthawi zosiyanasiyana. Ngati mukufuna kuitanitsa kabuku ka masamba 36 kameneka, lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma.’

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Brochure covers: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.