Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Malinga ndi zokonda za munthu aliyense wokhoma msonkho, boma la Spain limaika padera 0.5 peresenti ya ndalama za misonkho kuti zipite ku mabungwe othandiza ovutika kapena mabungwe a Akatolika. Ngakhale kuti anthu 80 pa 100 alionse ku Spain amati ndi Akatolika, ndi anthu 20 okha pa 100 alionse amene amasankha kupereka ndalama ku tchalitchicho.—EL PAÍS, SPAIN.

“Munthu wamwamuna wa zaka 30 wosuta fodya amadula moyo wake ndi zaka faifi ndi theka, ndipo wamkazi ndi zaka sikisi ndi theka,” malinga ndi ndandanda ya moyo wa anthu yomwe linakonza bungwe lotchedwa Institute of Actuaries. Koma, kusiya kusuta fodya ali ndi zaka 30 kungamuthandize kuti asafe chifukwa cha matenda obwera chifukwa cha kusuta fodya.—THE TIMES, ENGLAND.

M’chaka cha 2004, mafuta amene amagwiritsidwa ntchito pa dziko lonse anawonjezeka ndi 3.4 peresenti kufika pa migolo 82.4 miliyoni patsiku. Mayiko a United States ndi China ndi amene anagwiritsa ntchito theka la mafuta owonjezerekawo ndipo tsopano dziko la United States limagwiritsa ntchito mafuta okwana migolo 20.5 miliyoni patsiku pamene la China limagwiritsa ntchito migolo 6.6 miliyoni patsiku.—VITAL SIGNS 2005, WORLDWATCH INSTITUTE.

“Muziwayamikira Amayi Anu”

Akatswiri oona za ntchito anati mayi yemwe sali pantchito yolembedwa wa ku Canada wa ana awiri apasukulu atati alipiridwe chifukwa cha ntchito yonse yomwe amagwira, ndalama zomwe angalandire pachaka, kuphatikizapo za ntchito yomwe wagwira nthawi yowerukira itapitirira, zingakwane madola pafupifupi 130,000. Ndalama zimenezi anazipeza ataona momwe anthu akulipiridwira masiku ano. Anawerengetsera ndalama zimene munthu angamalandire “atamagwira ntchito maola 100 pa mlungu. Maola amenewa akuchokera pa masiku sikisi pa mlungu a maola 15 tsiku lililonse ndi tsiku limodzi la maola 10,” inatero nyuzipepala ya Vancouver Sun. Zina mwa ntchito zimene mayi yemwe sali pa ntchito yolembedwa amagwira ndi ntchito ya wosamalira ana masana, mphunzitsi, dalaivala, wokonza m’nyumba, wophika, nesi, ndi wokonza zowonongeka pakhomo. Nyuzipepalayo inapereka malangizo otsatirawa: “Muziwayamikira amayi anu: N’kutheka kuti sakulipidwa ndalama zokwanira.”

Achinyamata Sakudziwa Kuti Khalidwe Labwino N’liti

Magazini ya yunivesite ya Jyväskylä ku Finland inati achinyamata ambiri ku Finland “akukhazikitsa mfundo zawozawo zoti aziyendera.” Nthawi zambiri masiku ano “anthu amasankha mfundo za chikhulupiriro chawo kuchokera ku zinthu zosiyanasiyana, ngati kuti akugula zinthu m’sitolo,” inatero magaziniyo. Zotsatira zake nthawi zina zimakhala zosokoneza. Mwachitsanzo, achinyamata amakhulupirira kuti m’pofunika kugawa chuma ndi ulemerero mwachilungamo; koma panthawi yomweyomweyo, “ayamba kukhulupirira kuti kuchita zinthu mopanda manyazi ndiponso kupikisana moipa n’kwabwino.”

Kuopsa Kwina Koikidwa Magazi

Mu nkhani imene inafalitsidwa posachedwapa, bungwe loona za mankhwala ku France la Health and Safety Agency for Medical Products linati, munthu akhoza kutenga mosavuta tinthu ta m’magazi toyambitsa nthenda inayake kusiyana ndi momwe ankaganizira m’mbuyomu. Tinthu timeneti timayambitsa nthenda yakupha imene imawononga minyewa ndi ubongo ndipo ilibe mankhwala, yofanana ndi nthenda ya misala ya ng’ombe. Ananena kuti aona kuti munthu akhoza kutenga nthenda imeneyi mosavuta kusiyana ndi mmene ankaganizira m’mbuyomu chifukwa choti ku Britain anapeza anthu awiri amene akuwaganizira kuti anatenga nthendayi ataikidwa magazi. Panopa palibe njira yopezera nthendayi zizindikiro zake zisanayambe.

Kufuna Kukhala Wochepa Thupi

Atachita kafukufuku apeza kuti “atsikana aang’ono kwambiri, ngakhale a zaka zisanu, sakusangalala ndi matupi awo ndipo amafuna atakhala ochepa thupi,” inatero nyuzipepala ya The Sydney Morning Herald. Nkhaniyo inatchula za kafukufuku amene anachita pa atsikana a ku Australia a zaka zisanu mpaka eyiti. Pafupifupi theka la atsikanawo ankafuna atakhala ocheperapo thupi, pamene ena ochuluka chimodzimodzi anati “angasinthe kadyedwe atati anenepa.” Wochita kafukufuku wina anati ngati munthu sakusangalala ndi thupi lake “akamakula angayambe kusadzidalira, kuvutika maganizo, ndi kudwala matenda ovutika kudya.”