Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Analidi Mwana wa Mulungu?

Kodi Yesu Analidi Mwana wa Mulungu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Yesu Analidi Mwana wa Mulungu?

NDI MTIMA wonse, mtumwi Petro anauza Yesu kuti: “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” (Mateyu 16:16) Awa ndi amodzi mwa malo ambiri m’Baibulo pamene Yesu amatchedwa Mwana wa Mulungu, ndipo mawu amenewa achititsa anthu opembedza kunena zinthu zambiri zosiyanasiyana.

Anthu ambiri amene amakhulupirira kuti Yesu Kristu ndi Mulungu amavutika kufotokoza chifukwa chake amatchedwanso Mwana wa Mulungu. Sizingatheke kuti akhale zonse ziwiri. Ena amati Yesu anali munthu wofunika m’mbiri ya anthu, anali munthu wanzeru, kapenanso mneneri weniweni wa Mulungu, koma sanali ndi udindo winanso woposa pamenepa. Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani kwenikweni pa nkhani imeneyi? Kodi zimene mumakhulupirira zili ndi kanthu?

Mwana Woyamba Kubadwa wa Mulungu

Baibulo limasonyeza kuti pa nthawi inayake Mulungu anali yekha. Chifukwa cha chikondi chake, anafuna kugawana ndi wina mphatso ya moyo mwakukhala tate, koma osati m’njira imene anthu amakhalira atate. M’malo mwake, Yehova anagwiritsa ntchito mphamvu yake yolenga, yomwe sitingathe kuimvetsa, kupanga munthu wauzimu wamoyo ndiponso wanzeru, “woyamba wa chilengo cha Mulungu,” amene panopa tikumudziwa kuti Yesu Kristu. (Chivumbulutso 3:14; Miyambo 8:22) Popeza Yesu analengedwa mwachindunji ndi Mulungu panthawi imene Mulungu anali yekhayekha, moyenerera amatchedwa “wobadwa yekha” ndi “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.”—Yohane 1:14; Akolose 1:15.

Choncho n’zochita kuonekeratu kuti, monga woyamba wa zolengedwa za Mulungu, Yesu sangakhale Mlengi, kapena kuti “Mulungu yekhayo.” (1 Timoteo 1:17, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Komabe, Mulungu anapatsa Mwana wake maudindo ambiri. Mwachitsanzo, kudzera mwa Yesu, Mulungu analenga “zonse,” kuphatikizapo angelo. Angelo amenewa amatchedwa “ana a Mulungu,” popeza Yehova ndi amenenso anawapatsa moyo.—Akolose 1:16; Yobu 1:6; 38:7.

Atakonza dziko lapansi kuti pakhale anthu, Mulungu, mosakayikira akulankhula ndi Mwana wake woyamba kubadwa, anati: “Tipange munthu m’chifanizo chathu.” (Genesis 1:26; Miyambo 8:22-31) Choncho, Yehova analenganso mwana wake woyamba waumunthu, Adamu, kudzera mwa cholengedwa chauzimu chimene chinadzakhala Yesu.—Luka 3:38.

Mmene Yesu Anakhalira Mwana Waumunthu wa Mulungu

Mtumwi Yohane ananena kuti pa nthawi yake ya Mulungu, Mwana wa Mulungu wauzimu “anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife.” (Yohane 1:14) Kuti Yesu asinthe chonchi, Mulungu mozizwitsa anasamutsa moyo wa Yesu kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya, yemwe anali namwali wachiyuda. Mwanjira imeneyi, Yesu anakhalabe Mwana wa Mulungu, ngakhale kuti tsopano anali munthu. Komanso, popeza Mulungu, osati munthu wina aliyense, ndi amene anapatsa Yesu moyo, Yesu anabadwa wangwiro, wopanda tchimo. Mngelo Gabrieli anauza Mariya kuti: “Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.”—Luka 1:35; Ahebri 7:26.

Umboni wotsimikizira kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu pamene anali munthu unachokera kwa Atate mwiniwakeyo. Panthawi ya ubatizo wa Yesu, Yohane Mbatizi analipo pamene kumwamba kunatseguka ndipo anamva mawu ochokera kumwamba akunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:16, 17) Choncho n’zosadabwitsa kuti Yohane anauza ophunzira ake kuti: “Ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.”—Yohane 1:34.

Panthawi ya utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu sankachita kulengeza zoti iyeyo ndi Mesiya, Mwana wa Mulungu. (Marko 8:29, 30) Nthawi zambiri iye ankafuna kuti anthu azindikire okha zimenezi pomvetsera zinthu zomwe ankaphunzitsa, poona moyo umene ankakhala, ndi poona zozizwitsa zambiri zimene anachita. Zambiri mwa zozizwitsa zimenezi anazichita pamaso pa anthu ambiri. Mwachitsanzo, iye anachiritsa “onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu.” (Mateyu 4:24, 25; 7:28, 29; 12:15) Akhungu, ogontha, olumala, ndi odwala, onse anabwera kwa Yesu ndipo iye anawachiritsa. Anaukitsanso akufa. (Mateyu 11:4-6) Pamaso pa ophunzira ake, Yesu mozizwitsa anayenda pamadzi ndipo anatontholetsa mphepo ndi mafunde patachitika namondwe woopsa. Mphamvu zazikulu zimene anasonyezazi zinachititsa ophunzirawo kunena kuti: “Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.”—Mateyu 14:24-33.

Mmene Mwana wa Mulungu Angakuthandizireni

N’chifukwa chiyani Mulungu anasamutsa Mwana wake wobadwa yekha wokondedwa kumwamba kum’pititsa padziko lapansi, pomwe anadzafa imfa yankhanza? “Kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Indedi, panalibenso njira ina imene Yesu akanatha “kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri” kupatulapo kufa. (Mateyu 20:28) Zoonadi, m’mbiri yonse ya anthu, palibe amene anakonda anthu kwambiri kuposa Yehova ndi Mwana wake woyamba kubadwa.—Aroma 8:32.

Pambuyo pa imfa yake, Yesu “anatsimikizidwa . . . kuti ndiye Mwana wa Mulungu” m’njira yapadera ndi yamphamvu kwambiri, mwa “kuuka kwa akufa” n’kukhalanso ndi moyo monga Mwana wa Mulungu wauzimu. (Aroma 1:4; 1 Petro 3:18) Kenaka, atadikirira modekha pambali pa Atate wake kwa zaka pafupifupi 1900, Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, lomwe ndi boma lakumwamba limene posachedwapa lidzalamulira padziko lonse lapansi.—Salmo 2:7, 8; Danieli 7:13, 14.

Kodi mukufuna kuyanjidwa ndi Mwana wa Mulungu wamphamvuyu? Ngati mukutero, tikukulimbikitsani kuphunzira zimene anaphunzitsa n’kuzitsatira pamoyo wanu. Yesu mwiniwakeyo anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Zoonadi, zimene munthu amakhulupirira zokhudza Mwana wa Mulungu n’zofunikadi.—Yohane 3:18; 14:6; 1 Timoteo 6:19.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi Yesu ndi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu m’lingaliro lotani?—Yohane 1:3, 14; Chivumbulutso 3:14.

▪ N’chifukwa chiyani mungakhulupirire kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu?—Mateyu 3:16, 17.

▪ Kodi mungapindule bwanji mukamakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu?—Yohane 3:16; 14:6; 17:3.

[Zithunzi pamasamba 12, 13]

Zinthu zanzeru zimene Yesu ankaphunzitsa ndiponso zozizwitsa zake zamphamvu zinasonyeza kuti sanali munthu wamba