Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Mmene Mungadzitetezere ku Khansa Yapakhungu (June 8, 2005) Mfundo zomwe zili mu nkhani zimenezi n’zabwino kwambiri. Ine ndine dokotala wamkulu pa chipatala cha matenda apakhungu. Ndingakonde kulandira magazini ena owonjezera kuti ndigawire anthu ena.

K. W., Denmark

Chifukwa cha magazini imeneyi, ndinaganiza zokayezetsa chiphuphu chomwe chinamera pamsana panga. Dokotala anandiuza kuti chikanatha kusanduka khansa yotchedwa Bowen. Ndinachitidwa opaleshoni nthawi yomweyo. Nkhani zimenezi zinandithandiza kuchitapo kanthu mwamsanga.

S. M., Japan

Bokosi lomwe lili pa tsamba 7 linandichititsa kukayezetsa kuchipatala chiphuphu chimene ndinali nacho. Atandiyeza anapeza kuti khansa yapakhungu yoopsa kwambiri inali kuyamba kumene. Monga momwe nkhaniyi inafotokozera, khansayo akanati asaipeze mwamsanga, ikanatha kundipha. Ndikuthokoza kwambiri dokotala wanga ndi nkhani za mu Galamukani! imeneyi, zimene mwina zinapulumutsa moyo wanga.

L. S., United States

Zoti Banja Likambirane (May 8, 2005 yachingelezi) Kale ndinkawerenga nkhani zokhazo zomwe zandisangalatsa, koma nditaona “Zoti Banja Likambirane,” ndinawerenga magazini yonseyo kuti ndithe kuyankha mafunsowo. Sipanapite nthawi yaitali kuti ndiyambe kumawerenga magazini yonse nthawi zonse.

Y. Z., Russia

Ndinasangalala kwambiri ndi tsamba limeneli. Linali lokondweretsa, komanso linandithandiza kuzindikira kuti ndifunika kumaika maganizo anga onse pa zimene ndikuwerenga.

D. S., Britain

Zimene Achinyamata Amadzifunsa—N’chifukwa Chiyani Ndimacheza ndi Anthu Olakwika? (August 8, 2005) Zikuoneka kuti pambuyo pa zaka teni ndikuchita ‘zochuluka mu ntchito ya Ambuye,’ sindinkadziwabe momwe ndingathetsere khalidwe loipa limeneli. (1 Akorinto 15:58) Ndinazindikira kuti ndimaganiza mwachibwana, koma sindinadziwe momwe ndingathetsere vuto limeneli. Ndimathokoza Yehova chifukwa cha nkhani ngati zimenezi, zomwe zimatithandiza kukhala bwinobwino m’dziko lamasiku anoli.

J. F., United States

Mu nkhani imeneyi, anatchulapo zoti ‘sitifunika kuwapeweratu anthu amene sadziwa zinthu zoona za m’Baibulo.’ Kodi mungafotokozepo bwino pamenepa? Bwanji ngati Mkristu akucheza kwambiri ndi munthu wosakhulupirira? Kodi zimenezi si zodetsa nkhawa?

D. P., United States

Yankho la “Galamukani!”: Nkhaniyo sinali kulimbikitsa Akristu kuti azicheza kwambiri ndi anthu osakhulupirira. Pa zochitika zilizonse, mfundo ya m’Baibulo yotsatirayi imagwira ntchito: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Koma zimenezi sizitanthauza kuti tizipeweratu anthu osakhulupirira. Monga momwe nkhaniyo inafotokozera, Baibulo limatilimbikitsa kuti “tichitire onse chokoma,” osati ofanana nawo chikhulupiriro okha. (Agalatiya 6:10) Ndipotu, utumiki wathu wachikristu umafuna kuti tizichita chidwi chenicheni ndi anthu, ndi kuwachitira zinthu mwaulemu. Yesu anapereka chitsanzo chabwino pankhani imeneyi. Iye sankacheza kwambiri ndi anthu amene sankachita chidwi ndi chifuniro cha Mulungu. (Yohane 15:14) Komabe, iye ankafikira anthu ndipo ankadziwa njira yochezera nawo. Chifukwa cha zimenezi, Yesu anakhala ndi mwayi wochitira umboni wabwino. (Mwachitsanzo, onani nkhani ya pa Luka 7:36-50.) Mofanana ndi Yesu, nafenso tikhoza kumachitira ulemu anthu osakhulupirira. Cholinga chathu n’choti tikhale “oganizira ena, ndi kuonetsa kudzichepetsa kwenikweni kwa anthu onse.”—Tito 3:2, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.