Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulandira Mafoni Angozi ku London

Kulandira Mafoni Angozi ku London

Kulandira Mafoni Angozi ku London

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU BRITAIN

“CHOLINGA chathu n’choti tizifikira anthu odwala ndi ovulala kwambiri pasanathe mphindi eyiti kulikonse komwe angakhale mu London muno, lomwe ndi dera lalikulu masikweya kilomita 1,600,” anatero Rob Ashford, mkulu woyang’anira maambulansi wa bungwe lotchedwa London Ambulance Service. “Timakwanitsa kuchita zimenezi pa ngozi zoposa 75 mwa ngozi 100 zilizonse, ngakhale kuti ngozi zimene zimachitika pachaka zikuchuluka.”

Ndinaitanidwa kukaona maofesi amene amalandirira mafoni onena za ngozi ku Waterloo mu mzinda wa London, kum’mwera kwa mtsinje wa Thames. Amenewa ndi maofesi aakulu ku Ulaya konse olandirira mafoni angozi, ndipo amalandira mafoni 3,000 patsiku. Mafoni amenewa amachokera m’dera lokhala anthu seveni miliyoni, amene amalankhula zinenero zoposa 300. Kodi anthu 300 amene amagwira ntchito pa maofesiwa amatani kuti athe kukwanitsa zimenezi?

Kuzindikira Kukula kwa Ngoziyo

Ndinaona munthu wina woyankha mafoni akulandira foni yangozi. Ku Britain, nambala imene munthu amaimba pakakhala ngozi ndi 999. Msangamsanga, woyankha foniyo anadziwa malo amene panachitikira ngoziyo ndi njira yachidule yokafikirapo. Nthawi yomweyo mapu a misewu anaoneka pa kompyuta yake. Kuti adziwe kukula kwa ngoziyo, anafunsa mafunso angapo: Ndi anthu angati amene akufunika chithandizo? Ali ndi zaka zingati, ndipo kodi ndi akazi kapena amuna? Kodi akomoka? Kodi akupuma? Kodi akumva kupweteka m’chifuwa? Kodi akutuluka magazi?

Pamene munthu woyankha foniyo akulowetsa pa kompyuta mayankho a mafunso amenewa, kompyutayo nthawi yomweyo imasonyeza kukula kwa ngoziyo. Imayatsa getsi lofiira ngati ngoziyo ndi yaikulu kwambiri ndipo anthu akhoza kufa nthawi ina iliyonse, getsi lachikasu ngati ngoziyo ndi yaikulu koma anthu saali mwakayakaya, kapena getsi lobiriwira ngati ngoziyo si yaikulu ndiponso anthu saali mwakayakaya. Woyankha foniyo kenaka amatumiza zimenezi kwa mnzake amene amatumiza thandizo kwa munthu amene wachita ngoziyo.

Thandizo la Pamalo Angoziwo

Bungweli lili ndi maambulansi 395 ndi magalimoto ena 60 amene amatha kufika mwachangu pamalo angozi. Munthu akaimba foni kuti kwinakwake kwachitika ngozi, amatumizako galimoto imene ili kufupi kwambiri ndi malowo. Amathanso kutumiza anthu opereka chithandizo choyamba oyenda panjinga zamoto, chifukwa amatha kuyenda mwamsanga ngakhale mumsewu mukhale modzaza magalimoto. Komanso pali madokotala 12 amene amatha kuwaitana nthawi ina iliyonse kukathandiza anthu opereka chithandizo choyamba aja.

Pamene ndinali ku maofesiwa, apolisi anaimba foni kuti pa msewu wina umene umayenda magalimoto ambiri pachitika ngozi yaikulu. Pamalopo panali patafika kale ambulansi, koma apolisiwo anaimbirabe foni ku likulu la maambulansili. Chifukwa chiyani? Kuti adziwitse anthu ogwira ntchito kumeneko kuti mwina pangafunike kutumiza helikopita yawo. Ndege yosavuta kuizindikira yofiira imeneyi imauluka nthawi pafupifupi 1,000 pachaka. M’ndegemu mumakhala wopereka chithandizo choyamba ndi dokotala, amene nthawi zambiri amatengera anthu ovulala kwambiri ku chipatala cha Royal London Hospital, kumene amakalandira chithandizo mwamsanga.

Mu 2004, anayeseranso njira ina yothandizira anthu. Anayamba kukhala ndi njinga zogwira ntchito ngati maambulansi ku bwalo la ndege ku Heathrow, ku London. Kumeneku kunali kuwonjezera ntchito imene ikuchitika kale ku mbali ya mzindawu yotchedwa West End. Pali gulu la madokotala angozi ndi opereka chithandizo choyamba amene amagwira ntchito ndi njingazi, ndipo potero amapeputsa ntchito ya maambulansi kuti azitha kutumizidwa ku ngozi zina. Njinga iliyonse ili ndi getsi la buluu ndi belu la ambulansi (sayilini). Ilinso ndi mabokosi amene amanyamuliramo katundu wokwana makilogalamu 35, yemwe amaphatikizapo chipangizo choyambitsanso mtima kugunda, mpweya wa okosijeni, ndi mankhwala opha ululu.

Patangotha masiku ochepa chiyambitsireni maambulansi apanjingawa, phindu lake linaoneka. Mayi wina wa zaka 35 anadwala kwambiri ku bwalo la ndege ku Heathrow pamene anali kudikirira ndege ndipo anasiya kupuma. Anthu awiri apanjinga opereka chithandizo choyamba anabwera m’timphindi tochepa atangolandira foni yangozi, anamupatsa okosijeni, ndipo nthawi yomweyo anayamba kumuthandiza kuti ayambirenso kupuma. Ambulansi inabwera kudzamutenga kupita naye ku chipatala china chapafupi. Atachira, anakakumana ndi anthu amene anamupatsa chithandizo choyamba aja ndipo anawathokoza chifukwa chopulumutsa moyo wake.

Ntchito Yawo Akuiwonjezerabe

Anthu oimba foni yangozi akakhala kuti satha kulankhula Chingelezi, amawatumiza kwa munthu amene angathe kumasulira zimene akunenazo. Nthawi zina zimavuta kudziwa chinenero cha munthu woimba foniyo, makamaka ngati akulankhula msangamsanga chifukwa cha nkhawa kapena kusokonezeka maganizo.

Pofuna kuphunzitsa anthu za chithandizo chapangozi, anakonza filimu yaifupi yokhala ndi mawu achingelezi imene ikupezeka pa DVD. Cholinga cha filimuyi n’kulimbikitsa anthu a ku London ochokera kum’mwera kwa Asia “kuti aphunzire kuthandiza munthu kuti ayambirenso kupuma,” inatero magazini yotchedwa LAS News, imene imafalitsidwa ndi bungwe la London Ambulance Service. DVD imeneyi imasonyezanso zomwe zimachitika pa maofesiwa akalandira foni yangozi.

Anthu a mafuko osiyanasiyana okhala mu mzinda wa London, umene uli likulu la dziko la England, amayamikira chithandizo chachangu chimene amalandira pangozi, kaya ngozi yake ikhale yokhudza munthu mmodzi kapena anthu ambiri ndiponso kaya ichitikire pansi pa nthaka kapena pamwamba m’nyumba yaitali kwambiri. Ponena za amuna ndi akazi amene amagwira ntchito ku London Ambulance Service, dokotala wina amene amagwira ntchito yaulere anati: “Amenewa ndi ena mwa anthu azachipatala aluso kwambiri amene ndagwirapo nawo ntchito.” Amenewa ndi mawu abwino oyamikira anthu ogwira ntchito ku bungwe limeneli, lomwe ndi bungwe lalikulu kwambiri padziko lonse lopereka chithandizo cha ambulansi chaulere.

[Bokosi patsamba 11]

Mavuto Ndiponso Zokhumudwitsa

Mafoni osayenera amene anthu amaimba pofuna kudziwa zinthu zina, ndi mafoni okhudza matenda kapena kuvulala kwakung’ono, komanso mafoni amene anthu amaimba mwadala kapena chifukwa choti analakwitsa, amavutitsa anthu othandiza pangozi. Komanso, odwala ndi anthu ena, kuphatikizapo azibale awo, atukwanapo ngakhalenso kumenya anthu azachipatala amene abwera kudzawathandiza. Anthuwa amakwiya mwina chifukwa choti asokonezeka maganizo kapena akugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapenanso akuganiza kuti anthu odzawathandizawa anachedwa. Palibe njira yosavuta yothetsera mavuto amenewa, koma kuphunzitsa anthu kwathandizako.

[Zithunzi patsamba 10]

Pa malowa amalandira mafoni angozi pafupifupi 3,000 tsiku lililonse

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

All photos: Courtesy of London Ambulance Service NHS Trust