Tsiku Lofunika Kwambiri M’mbiri Yonse ya Anthu
Tsiku Lofunika Kwambiri M’mbiri Yonse ya Anthu
Tsiku limeneli ndi tsiku limene Yesu Kristu anamwalira. N’chifukwa chiyani imfa ya Yesu inali yofunika kwambiri? Pali zifukwa zingapo.
Kukhulupirika kwa Yesu mpaka kufa kunasonyeza kuti munthu angathe kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu.
Imfa ya Kristu inapatsanso anthu ena mwayi wokalamulira naye kumwamba. Kuwonjezera apo, inatsegula njira yoti anthu ena ambiri adzasangalale ndi moyo wosatha m’paradaiso pa dziko lapansi.
Usiku woti mawa lake amwalira, Yesu anagwiritsa ntchito mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo wofiira monga zizindikiro za nsembe ya thupi lake yomwe anaipereka mwachikondi. Ndipo anauza ophunzira ake kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Kodi inuyo mudzakumbukira nawo chinthu chofunika kwambiri chimenechi?
Mboni za Yehova zikukuitanani kuti mukakhale nazo limodzi pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Chaka chino tsiku la Chikumbutso chimenechi ndi Lachitatu, April 12, dzuwa litalowa. Mukhoza kudzapita ku Nyumba ya Ufumu yomwe muli nayo pafupi. Funsani a Mboni za Yehova kwanuko kuti mudziwe nthawi ndi malo ake enieni.