Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Anthu pafupifupi 200 miliyoni, omwe ndi 5 peresenti ya anthu a zaka zapakati pa 15 ndi 64 padziko lonse lapansi, anamwa kapena kusuta mankhwala oletsedwa ndi boma chaka chathachi.—2005 WORLD DRUG REPORT, UNITED NATIONS OFFICE ON DRUGS AND CRIME.

Kafukufuku wasonyeza kuti wachinyamata amene waona munthu akuwomberedwa ndi mfuti, angachite kwambiri zachiwawa m’zaka ziwiri zotsatira kuposa wachinyamata amene sanaone munthu akuwomberedwa.—SCIENCE MAGAZINE, U.S.A.

Ku São Paulo, m’dziko la Brazil, anthu pafupifupi 17 pa anthu 100 alionse amene anawapeza ndi khansa ya m’mawere pa chipatala china m’chaka chimodzi anali azimayi osakwanitsa zaka 35. Khansayi akaitulukira msanga, pamakhala mwayi waukulu woti akhoza kuichiza.—FOLHA ONLINE, BRAZIL.

Kuthana ndi Kunyong’onyeka

Anthu ochita kafukufuku wokhudza kunyong’onyeka akuti, kunyong’onyeka ndi “amodzi mwa matenda aakulu kwambiri a m’nthawi yathu ino,” inatero nyuzipepala yotchedwa The Vancouver Sun. Pa kafukufuku wina, anapeza kuti “anthu pafupifupi atatu pa anthu anayi alionse ku North America amafuna pamoyo wawo patamachitika zinthu zatsopano ndi zosangalatsa.” Zina mwa mfundo zomwe nyuzipepalayo inanena zomwe zingakuthandizeni kuthetsa kunyong’onyeka ndi izi: “Muzichita zinthu zosiyana ndi zimene mumachita nthawi zonse,” “phunzirani zinthu zatsopano,” gwirani “ntchito mongodzipereka pothandiza anthu ena,” “chitani zinthu zolimbitsa thupi, monga . . . kuyenda,” ndiponso “muziyamikira ena akakuchitirani zabwino.”

Ukapolo wa Masiku Ano

Pa kafukufuku yemwe inachita nthambi ya United Nations ya International Labor Organization (ILO), anapeza kuti “anthu pafupifupi 12.3 miliyoni amagwira ntchito mokakamizidwa padziko lonse lapansi.” Akuti mwa anthu amenewa, anthu opitirira 2.4 miliyoni anachita kugulitsidwa. Zitsanzo za ntchito zimene anthu amagwira mokakamizidwa kapena mowopsezedwa ndizo uhule ndi usilikali. Palinso ntchito zina zimene ogwira ntchitowo amalandira malipiro ochepa kapena salandira kalikonse chifukwa choti malipiro awo amatengedwa ndi makolo awo kapena munthu wina kuti akabwezere ngongole. Malinga ndi mkulu wa bungwe la ILO, Juan Somavia, ntchito yoteroyo “imawalanda anthu ufulu wawo wachibadwidwe ndiponso imawachotsera ulemu.”

Baibulo Lathunthu Loyamba la Chikiriyoli

“Ku Australia, kwa nthawi yoyamba anamaliza kumasulira Baibulo, kuyambira ku Genesis kukafika ku Chivumbulutso, kuti likhale m’chinenero cha mbadwa za m’dzikoli,” inatero nyuzipepala ya The Sydney Morning Herald. Baibulo la Chikiriyoli limeneli, lomwe likuyembekezeka kutulutsidwa mu 2007, lidzathandiza Aaborijini 30,000 okhala m’madera akumidzi kumpoto kwa Australia. “Ntchitoyi yatenga zaka 27,” inatero nyuzipepalayo. Malinga ndi bungwe la United Bible Societies, “mu 2004 Mabaibulo 22 a Chipangano Chatsopano omasuliridwa kumene analembetsedwa” ku bungweli. Panopa, Baibulo lamasuliridwa lonse kapena mbali yake m’zinenero 2,377.

M’magalimoto Oimikidwa Mumatentha

Mu 2004, ku United States ana 35 anafa chifukwa cha kutentha atasiyidwa m’magalimoto oimikidwa, inatero magazini yotchedwa Pediatrics. Kafukufuku wasonyeza kuti kunja kukamatentha kupitirira madigiri seshasi 30, m’galimoto mukhoza kutentha kupitirira madigiri seshasi 57 mpaka 68 pakanthawi kochepa. Ngakhale ngati kunja kukutentha madigiri seshasi 22, m’galimoto mukhoza kutentha ndi madigiri ena 22 kuposa pamenepa, ndipo kuwonjezeka kwa kutenthaku kumachitika mu mphindi 15 mpaka 30 kuchokera pa nthawi imene mwaimika galimotoyo. Kusiya mawindo ali otsekula masentimita anayi, kapena kuyatsa choziziritsira mpweya musanazimitse galimotoyo sikuthandiza kwenikweni. Amene analemba nkhaniyi akukhulupirira kuti kuphunzitsa anthu za kuopsa kwa zimenezi kungapulumutse miyoyo.