“Anaikidwa M’ndende Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo”
“Anaikidwa M’ndende Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo”
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU POLAND
MAWU akuti Arbeit Macht Frei (Ntchito Imamasula) adakalipo mpaka pano pa mageti azitsulo a ndende yozunzirako anthu ya Auschwitz, yomwe ili kum’mwera kwa dziko la Poland, makilomita pafupifupi 60 kuchokera kumalire a dziko la Czech. * Komatu mawu amenewa akutsutsana ndi zomwe zinachitikira ambiri mwa anthu amene analowa pamagetiwa kuyambira mu 1940 mpaka mu 1945. M’zaka zimenezi, anthu oposa wani miliyoni ku Auschwitz anaphedwa ndi a Nazi. Koma, m’ndendeyi munali anthu a gulu lina omwe akanatha kumasulidwa nthawi iliyonse.
Kodi anthu amenewa akanaupeza bwanji ufulu umenewu? Mkaidi aliyense wa Mboni za Yehova amene anasaina chikalata chofotokoza kuti iye wasiya kukhala wa Mboni, ankamasulidwa. Kodi Mboni zambiri zinasankha chiyani? Mkulu wina wolemba mbiri, dzina lake István Deák, ananena kuti Mbonizo “zinafanana ndi Akristu oyambirira omwe ankalolera kudyedwa ndi mikango m’malo mopereka kansembe kakang’ono pa guwa la mfumu ya Roma.” Kunena zoona, anthu a mtima ngati umenewu n’ngofunika kumakumbukiridwa, ndipo n’zimene zakhala zikuchitikadi.
Kwa miyezi iwiri, kuyambira pa September 21, 2004, m’holo yaikulu ya nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi, ya Auschwitz-Birkenau State Museum, munachitikira chionetsero chokhudza Mboni basi. Chionetserocho chinali ndi mutu wogwirizana ndi nkhani yake, wakuti “Anaikidwa M’ndende Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo—Mboni za Yehova mu Ulamuliro wa a Nazi.” Panali mabodi 27 omwe anaonetsapo zimene Mboni, chifukwa cha chipembedzo chawo, zinasankha kusalowerera nawo m’ndale ndiponso nkhondo m’nthawi ya a Nazi.
Ambiri mwa anthu omwe anapita ku chionetserocho anakhudzidwa mtima ndi kalata yomwe inatumizidwa kuchokera ku ndende ndi Deliana Rademakers wa ku Netherlands. Iye analembera banja lake kuti: “Ndinalumbira kuti ndidzachita chifuniro cha Yehova. . . . Ndikukupemphani kuti mulimbe mtima. Yehova ali nafe.” Mu 1942, Deliana anam’samutsira ku Auschwitz, komwe anakamwalira pasanathe milungu itatu.
M’ndende ya Auschwitz munali Mboni pafupifupi 400. Atatu mwa anthu amene anapulumuka m’ndendeyi anali nawo pa mwambo wotsegulira chionetserocho, pomwe anafotokoza zomwe zinawachitikira ndiponso anayankha mafunso a atolankhani. Panthawiyi, anthuwa anasonyeza mtima womwenso unawathandiza kupirira mavuto panthawi yomwe anali kundendeko.
M’buku lake lakuti Imprisoned for Their Faith—Jehovah’s Witnesses in Auschwitz Concentration Camp, Teresa Wontor-Cichy, yemwe amagwira ntchito ya zofufuzafufuza pa nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwiyo, analemba kuti: “Mtima womwe gulu laling’onoli linasonyeza unalimbikitsa akaidi ena ndipo maganizo awo osafuna kugonja tsiku ndi tsiku, analimbikitsa ena kusakayikira m’pang’ono pomwe kuti zingavute bwanji, n’zotheka kuti munthu asasiye mfundo zomwe amayendera.”
Kunena zoona, nkhani yoponyedwa m’ndende ndiponso yophedwa siyachilendo kwa anthu otsatira Yesu Kristu, yemwenso anamangidwa ndi kunyongedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake. (Luka 22:54; 23:32, 33) Nayenso Yakobo, mtumwi wa Yesu, ananyongedwa. Mtumwi Petro anamangidwapo, ndipo mtumwi Paulo anamenyedwa ndi kumangidwa kambirimbiri.—Machitidwe 12:2, 5; 16:22-25; 2 Akorinto 11:23.
Mofanana ndi zimenezi, Mboni za Yehova ku Ulaya zinasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri chokhulupirira Mulungu m’zaka za m’ma 1930 ndi m’ma 1940. N’zosangalatsa kuti anthu ayamikira chikhulupiriro chomwe anthu amenewa anali nacho ku Auschwitz.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Ndende ya Auschwitz inali ndi zigawo zitatu zikuluzikulu, Auschwitz I (ndende yaikulu), Auschwitz II (Birkenau), ndi Auschwitz III (Monowitz). Zambiri mwa nyumba zoipa kwambiri zomwe ankapheramo anthu ndi mpweya wa gasi zinali ku Birkenau.
[Chithunzi patsamba 10]
Anthu atatu amene anapulumuka ku Auschwitz agwira chikwangwani cha mutu wa chionetsero
[Zithunzi patsamba 11]
Deliana Rademakers, ndi kalata yomwe analemba ali ku ndende
[Mawu a Chithunzi]
Inset photos: Zdjęcie: Archiwum Państwowego Muzeum Auschwitz-Birkenau
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Tower: Dzięki uprzejmości Państwowego Muzeum Auschwitz-Birkenau