Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
Kuthandiza Achinyamata Amene Ali Pamavuto (April 8, 2005) Nkhani zimenezi zinali zothandiza kwambiri. Nthawi zina, moyo umakhala wovuta kwa achinyamata, koma kulandira nkhani zolimbikitsa ngati zimenezi kumapepukitsa mavutowo. Zimenezi ndizo nkhani zimene achinyamatafe timafunikadi mu “nthawi zowawitsa” zino. (2 Timoteo 3:1) Mfundo za m’nkhani zimenezi zitithandiza kuti tisapusitsidwe ndi “machenjerero a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11) Zikomo chifukwa chotipatsa chakudya chauzimu chapanthawi yake.
K. S., United States
Zomwe Tonsefe Tingachite Kuti Pakhomo Pazikhala Paukhondo (June 8, 2005) Ndili mwana, makolo anga onse ankagwira ntchito ndipo ana awo, omwe tinalipo atatu, tinkasewerera m’nyumba nthawi zonse. M’nyumbamo simunkaoneka bwino ayi. Mpaka pano ndimadana ndi ntchito yokonza pakhomo kuti pakhale paukhondo. Koma kuwerenga nkhaniyi kunali ngati kumva mayi anga akundiphunzitsa ntchitoyi mokoma mtima. Tsopano ndili ndi ana akuluakulu, ndipo amadana ndi ntchito yokonza pakhomo kuti pakhale paukhondo. Pali zambiri zoti ndiwaphunzitse. Nkhani imeneyi ndiyo yandilimbikitsa.
Y. E., Japan
Madokotala (February 8, 2005) Ndinawerenga nkhani zotithandiza kuwamvetsa bwino madokotala athu. Zikomo pofotokoza momveka bwino mmene madokotala amamvera. Ndine nesi, ndipo ndakhala ndikudzionera ndekha kusamvetsetsana kumene kumakhalapo pakati pa achipatala ndi odwala. Ndikukhulupirira kuti nkhanizi zithandiza ambiri kuwamvetsetsa achipatala ndiponso kuona kufunika kwa ntchito yawo.
L. K., Russia
Dokotala wina anandifotokozera kuti anali ndi chidwi kwambiri powerenga magazini imeneyi. Anayamikira kafukufuku amene anachitika n’kunena kuti akugwirizana kwathunthu ndi nkhanizi. Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani zabwino kwambiri zimenezi.
H. Z., Germany
M’mbuyomu ndikadwala ndinkangoganizira za ineyo basi. Koma magaziniyi yandithandiza kumvetsa mavuto amene madokotala amakumana nawo. Kuyambira tsopano, ndikamalandira chithandizo, sikuti ndizingolongosola za vuto langalo monga mmene ineyo ndikulionera ayi, koma ndizitsatira malangizo amene ali m’bokosi lakuti “Kuchita Zinthu Zoganizira Dokotala Wanu.” Ndikufuna ndikhale munthu woganizira ena ndikadwala.
J. M., Japan
Ndine mkulu mu mpingo ndiponso ndine dokotala. Popeza ndimaonana ndi odwala ambiri patsiku, ndimavutika kwambiri n’kutopa chifukwa cha chisoni. Kukhala wa Mboni za Yehova kwandithandiza kugwira ntchitoyi mwanzeru. Ndimayesetsa kukhala wachangu pantchito n’cholinga choti ndizipeza nthawi yokwanira yokhala panyumba ndi mkazi ndi ana anga komanso yogwira ntchito zachikristu. Magazini a Galamukani! amandithandiza kuchita zinthu mwanzeru ndiponso kuikira mtima pa zinthu zofunika kwambiri.
P. R., United States
Sindikugwirizana ndi zoti “maloya ena amaimba madokotala milandu pa zinthu zazing’ono n’cholinga choti apeze chuma.” Kawirikawiri maloya sapindula chilichonse popanda chigamulo cha akhoti. Kuti mlandu uwayendere bwino amayenera kupereka umboni wosonyeza kuti panali kuswa malamulo pa chithandizo chimene munthu wapatsidwa. Popeza kuti ndatha zaka 30 ndikuimira milandu yokhudza kusagwira bwino ntchito kumene anthu ena akhala akuchita, ndikufuna kukuuzani kuti pali milandu yambirimbiri imene ndakana kuimira kuposa imene ndaimirapo.
J. M., United States
“Galamukani!” ikuyankha: Mfundo yathu yakuti “maloya ena amaimba madokotala milandu pa zinthu zazing’ono” sikuti ikufotokoza mmene mchitidwewu wafalira ayi. Mfundo yathu inali yakuti kufala kwa milandu yokhudza kusagwira bwino ntchito yawo kukuwadetsa nkhawa madokotala ambiri. N’zoona kuti pamakhala milandu ina yopanda umboni. Komabe, mfundo yomwe wowerenga wathuyu akunena ndi yoona. Ogwira ntchito zachilungamo ali ndi malire omwe angapangitse kuti kuzenga munthu mlandu pa zinthu zazing’ono kukhale kosayenerera, kapenanso kukhale kulakwa kumene.