Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungathe Kupeza Chimwemwe Chenicheni

Mungathe Kupeza Chimwemwe Chenicheni

Mungathe Kupeza Chimwemwe Chenicheni

ANTHU ambiri padziko lonse akuoneka kuti amakhulupirira kuti, kuti munthu akhale wachimwemwe, ayenera kukhala ndi galimoto yokongola, ndalama zambiri, ntchito yapamwamba, nyumba yaikulu, ndi zipangizo zamagetsi zamakono, komanso akhale wokongola. Koma kodi chimwemwe chimadaliradi zinthu zimenezi?

Lipoti lapadera la m’magazini ya Time linati, pali “kafukufuku wochuluka amene wachitika pa nkhani ya chimwemwe, kukhala ndi chiyembekezo, ndi kuganizira zinthu zolimbikitsa, komanso kukhala ndi makhalidwe amene amabweretsa thanzi labwino m’thupi ndi m’maganizo.” Zotsatirapo za kafukufuku woteroyo zadabwitsa anthu ambiri. Umboniwo, womwe pafupifupi nthawi zonse umakhala wofanana, wasonyeza kuti anthu amene amakhulupirira kuti ndalama, kutchuka, kapena kukongola kungawabweretsere chimwemwe akungodzinyenga. Ndipotu, akumanga miyoyo yawo pa maziko amene angawasokoneze maganizo ndiponso mwina akhoza kuwachititsa kudwala matenda ovutika maganizo.

Ku United States, anthu ambiri panopa ndi olemera kwambiri kuposa kale lonse. “Koma kulemerako sikunatibweretsere chimwemwe chochuluka,” inatero magazini ya Time. Zinthu zofanana ndi zimenezi zikuchitikiranso anthu m’mayiko ena. Ku China, komwe chuma chake chikupita patsogolo kwambiri, anthu omwe ali osasangalala awonjezeka modetsa nkhawa. M’dziko limeneli, kudzipha kwasanduka “chinthu chachikulu chomwe chikutenga miyoyo ya anthu a zaka zapakati pa 15 ndi 34,” inatero magazini yotuluka kanayi pachaka yotchedwa Access Asia. Zikuoneka kuti chinthu chimodzi chomwe chachititsa zimenezi n’choti achinyamata akukakamizika kuchita bwino m’dziko lovuta ndi lofuna zambiri, lomwe limalimbikitsa kwambiri kukhala ndi ntchito yabwino ndi kupeza chuma.

N’zachionekere kuti kupeza bwino sikuchepetsa nkhawa, m’malo mwake kumaiwonjezera. Pa kafukufuku wina amene yunivesite ina inachita anapeza kuti “mmene tikukhalira moyo wathu panopa n’chinthu chachikulu chimene chikutibweretsera mavuto a m’maganizo.” Malinga ndi zimene ananena katswiri wina woona mmene khalidwe la anthu likusinthira, dzina lake Van Wishard, “matenda a maganizo ndiyo mbali imene ikukula kwambiri pa inshuwalansi imene makampani ambiri akulipira.”

Ngakhale ana akukhudzidwa ndi dziko lathuli, limene likusintha mofulumira. Wishard anati tsopano kuli mabuku a ana a zaka eyiti owalangiza “momwe angadziwire zizindikiro za kupanikizika maganizo ndi zomwe angachite kuti athane nako.” Ndipo malinga ndi zimene chikalata china chonena za kuvutika maganizo chinanena, m’mayiko angapo a Azungu, matenda a kuvutika maganizo amene akuwapeza nawo ana akuwonjezeka kwambiri. Akuwonjezeka ndi 23 peresenti pachaka. Komanso, “ana omwe sanayambe sukulu ndilo gulu limene likuwonjezeka kwambiri pa anthu amene amafunika mankhwala olimbana ndi kuvutika maganizo.”

Manthanso akuchuluka, ndipo sakuchuluka kokha chifukwa cha nkhawa ya zachuma. Chifukwa cha kuwonjezeka kwa anthu amene akuchita zinthu zoipa kwambiri m’dzina la ndale ndi chipembedzo, anthu ambiri amachita mantha akaganizira zomwe zingachitike m’tsogolomu. Kodi pali thandizo lililonse lomwe lilipo?

Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu Kristu anaphunzitsa njira ya moyo yomwe ndi yosiyana ndi zimenezi ndipo imatsitsimula ndi kuchepetsa kuvutika maganizo. Chiphunzitso chake chinagona pa mfundo ya choonadi yosavuta kumvetsa koma yofunika kwambiri. Iye anati: “Odala ali osauka mumzimu [“ozindikira kusowa kwawo kwauzimu,” NW].” (Mateyu 5:3) Zoonadi, Yesu analimbikitsa omvetsera ake kuganizira kwambiri za chosowa chachikulu cha anthu, chomwe ndi mfundo zauzimu zoonadi zokhudza Mlengi ndi zolinga zake kwa ife.

Monga momwe tionere mu nkhani zotsatirazi, mfundo zoonadi zimenezi zingatithandize kuzindikira zinthu zomwe zilidi zofunika, zomwe zingatithandize kukhala ndi moyo wachimwemwe ndiponso watanthauzo kwambiri. Mfundo zauzimu zoonadi zimenezi zimatipatsanso chiyembekezo chabwino kwambiri.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Kodi kuti munthu akhale wachimwemwe amafunika kukhala ndi chuma?