Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizo Poteteza Ana Athu

Thandizo Poteteza Ana Athu

Thandizo Poteteza Ana Athu

Chaka chathachi, mzimayi wina wa ku Virginia, m’dziko la United States, analemba kalata yoyamikira buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, ndipo anati: “Zidzukulu zanga zisanakagone, zimanena kuti: ‘Agogo, tiwerengereni nkhani m’buku la Yesu.’ Anawo ali ndi zaka 4, 6, ndi 7, ndipo amasangalala kwambiri ndi nkhani za m’bukuli.”

Agogowa anafotokoza kuti: “Ndinawerenga mutu 32 wakuti ‘Mmene Yesu Anatetezedwera.’ Ndinachita chidwi kwambiri chifukwa chakuti utalongosola mmene Yehova anatetezera Yesu, mutuwu uli ndi phunziro labwino lopita kwa ana lowathandiza kuti azitha kudziteteza. Mutuwu uli ndi mawu akuti: ‘Ngati munthu wina akufuna kuchita zimenezi, nena mosaopa komanso mofuula kuti: “Osandigwira! Ndikakunenerani!”’”

Ku Mexico mayi wa mwana wina wamkazi, wa zaka zisanu, yemwe dzina lake ndi Betsaida, ananena kuti akuwerenga kachiwiri buku la Mphunzitsi limodzi ndi mwana wakeyo. Mayiyu anati: “Dziko likuipiraipira, ndipo ana athu aang’onoang’ono akukumana ndi mavuto ambiri. Mwana wangayu akuti ndi woyamikira kwambiri chifukwa cha malangizo a mmene angadzitetezere ku zinthu zosayenera, monga amene atchulidwa m’mutu 32.”

Buku la zithunzi zokongola la masamba 256 limeneli, lomwe kukula kwake n’chimodzimodzi ndi magazini ino, lathandiza kwambiri makolo kutsatira malangizo a m’Baibulo ophunzitsira ana awo. (Miyambo 22:6) Maphunziro ake, otengedwa pa ziphunzitso za Yesu Kristu, analongosoledwa m’mawu osavuta, koma nkhani zake ndi zothandiza anthu a misinkhu yonse. Mungaitanitse bukuli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndi kutumiza ku adiresi imene ili pomwepayi kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.