Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukhala Munthu Wamtendere N’kothandiza?

Kodi Kukhala Munthu Wamtendere N’kothandiza?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kukhala Munthu Wamtendere N’kothandiza?

MUULALIKI wake wotchuka wa pa phiri, Yesu Kristu anati: “Odala ali akuchita mtendere.” Ananenanso kuti: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5, 9) Kukhala wamtendere sindiko kungokhala pamtendere kapena kungomva kuti uli ndi mtendere mumtima chabe. Munthu wamtendere amayamba ndi iyeyo kukhala wachifundo ndiponso amayesetsa kulimbikitsa mtendere.

Kodi mawu a Yesu omwe ali mu lemba lili pamwambali amagwira ntchito masiku ano? Ena amaganiza kuti, munthu afunika kukhala wamtopola, wovuta, ngakhalenso wachiwawa kuti zinthu zimuyendere bwino masiku ano. Kodi ndi nzeru kubwezera mtopola ku mtopola kapena chiwawa ku chiwawa? Kapena kodi n’zothandiza kukhala munthu wamtendere? Tiyeni tione zifukwa zitatu zimene tiyenera kuwaganizira mofatsa mawu a Yesu akuti: “Odala ali akuchita mtendere.”

▪ MTIMA WODEKHA Lemba la Miyambo 14:30 limati: “Mtima wabwino [kapena kuti, wodekha] ndi moyo wa thupi.” Malipoti ambiri azamankhwala asonyeza kuti mkwiyo ndi udani ungayambitse matenda a sitiroko ndi matenda a mtima. Posachedwapa, nyuzipepala ina ya zamankhwala, ponena za anthu amene ali ndi matenda a mtima, inati mkwiyo wosalamulirika umakhala ngati poizoni. Nyuzipepalayi inalongosolanso kuti “ngati munthu akwiya kwambiri angadwale kwambiri.” Komabe, anthu amene amafunafuna mtendere amakhala ndi mtima wodekha ndiponso amapindula.

Chitsanzo cha zimenezi ndi Jim, wazaka 61, amene tsopano ndi mphunzitsi wa Baibulo wa anthu omwe amalankhula Chiviyetinamu ku United States. Iye anafotokoza kuti: “Pambuyo pokhala zaka sikisi ku nkhondo ndiponso maulendo atatu okamenya nkhondo ku Vietnam, chiwawa, mkwiyo ndi kupsa mtima ndinkazidziwa bwino. Ndinkavutika maganizo ndi moyo wanga wakale, ndiponso ndinkasowa tulo. Posapita nthawi ndinayamba kupsinjika maganizo ndiponso kudwala m’mimba ndi matenda okhudzana ndi ubongo.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anati: “Kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kunapulumutsa moyo wanga. Kuphunzira za chifuniro cha Mulungu cha dziko lapansi latsopano lamtendere ndiponso mmene ndingavalire ‘umunthu watsopano,’ zandipangitsa kukhala wodekha. Zotsatira zake n’zoti ndili ndi thanzi labwino tsopano.” (Aefeso 4:22-24; Yesaya 65:17; Mika 4:1-4) Anthu ena ambiri, malinga ndi zimene zawachitikira, azindikira kuti kukhala munthu wamtendere kungathandize kuti munthu ukhale ndi thanzi labwino, maganizo abwino, ndiponso moyo wabwino wauzimu.—Miyambo 15:13.

▪ KUGWIRIZANA NDI ANTHU Tikhoza kumagwirizana ndi anthu ambiri ngati tili anthu amtendere. Baibulo limanena kuti “kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe . . . , ndiponso choipa chonse.” (Aefeso 4:31) Anthu amtopola kawirikawiri amathamangitsa ena ndipo amapezeka kuti ali okhaokha, opanda anzawo odalirika. Lemba la Miyambo 15:18 limati: “Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.”

Andy, mkulu wina wachikristu wa zaka 42 wa mu mzinda wa New York City, anakulira ku malo komwe anthu ake anali a mtopola. Anafotokoza kuti: “Anandiika m’bwalo lomenyera nkhonya ndi kuyamba kundiphunzitsa nkhonya ndili ndi zaka eyiti. Sindinkaganiza n’komwe kuti omwe ndinkamenyana nawowo anali anthu. M’malo mwake maganizo anga anali akuti ‘ngati sindimumenya ndiye kuti andimenya.’ Posapita nthawi ndinalowa nawo m’gulu la anyamata ochita zinthu zosokonezeka. Tinkachita ndewu za m’misewu ndiponso mapokoso. Ndakhala ndikulozetsedwa mfuti m’mutu ndiponso kuopsezedwa ndi mipeni. Sindinkagwirizana kwambiri ndi anzanga ndipo tinkangokhalira kuopana.”

Kodi chinamupangitsa Andy kufuna kukhala munthu wamtendere n’chiyani? Anati: “Tsiku lina ndinapita ku msonkhano ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, ndipo mwamsanga ndinaona mmene anthu kumeneko ankasonyezerana chikondi. Kuyambira nthawi imeneyo, kukhala ndi anthu okonda mtendere amenewa kunandithandiza kukhala ndi mtima wodekha, ndipo pomalizira pake zinandithandiza kuthetsa maganizo anga akale aja. Tsopano ndili ndi anzanga ambiri odalirika.”

▪ CHIYEMBEKEZO CHA TSOGOLO LABWINO Chifukwa chachikulu kwambiri chokhalira munthu wamtendere ndi ichi: Kusonyeza ulemu ndi kulemekeza chifuniro cha Mlengi wathu chimene watidziwitsa. Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu mwiniwakeyo, limatilimbikitsa kuti: “Funa mtendere ndi kuulondola.” (Salmo 34:14) Kudziwa kuti Yehova Mulungu alipo ndipo kenako n’kuphunzira ndi kumvera ziphunzitso zake zopatsa moyo, kumapatsa munthu mwayi wokhala naye paubwenzi. Ndipo tikakhala pa ubwenzi wolimba ndi iye, tidzapeza “mtendere wa Mulungu.” Tikhoza kukhalabe ndi mtendere umenewu ngakhale ngati titakumana ndi mavuto.—Afilipi 4:6, 7.

Komanso, pokhala amtendere, timam’sonyeza Yehova kuti tikufuna kukhala munthu wotani. Tingamusonyeze Mulungu tsopano kuti tingathe kusintha makhalidwe athu kuti tidzakhale m’dziko lake latsopano ndi lamtendere limene akutilonjeza. Pamene adzachotsa anthu onse oipa ndi kulola anthu ofatsa ‘kulandira dziko lapansi,’ monga mmene Yesu ananenera, tikhoza kudzakhala ndi mwayi woona zimenezi zikuchitika. Amenewa adzakhala madalitso ochititsa chidwi kwambiri!—Salmo 37:10, 11; Miyambo 2:20-22.

Inde, kufunika kwa mawu a Yesu akuti “achimwemwe ali akuchita mtendere” n’koonekeratu. Tingakhale ndi mtima wodekha, anzathu abwino, ndiponso chiyembekezo cha tsogolo labwino. Tingalandire madalitso amenewa ngati titachita zonse zimene tingathe kuti ‘tikhale ndi mtendere ndi anthu onse.’—Aroma 12:18.

[Zithunzi patsamba 28]

“Ndili ndi thanzi labwino tsopano.”—Jim

[Zithunzi patsamba 29]

“Ndili ndi anzanga ambiri odalirika.”—Andy