Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wautali Bwanji?

Kodi Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wautali Bwanji?

Kodi Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wautali Bwanji?

“Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana; adzabwerera ku masiku a ubwana wake.”—YOBU 33:25.

GALU akafa atakhala zaka 10 kapena 20, nthawi zambiri amakhala atachita zinthu zambiri zimene agalu amachita. Mwina amakhala atalera ana, atathamangitsapo amphaka, atakwirirapo mafupa, ndiponso atatetezapo mbuyake. Koma munthu akafa atakhala zaka 70 kapena 80, amakhala atachita zinthu zochepa zokha za zinthu zimene akanatha kuchita. Ngati ankakonda masewera, mwina anali katswiri pa masewera amodzi kapena awiri okha. Ngati ankakonda zoimbaimba, mwina ankaimba bwino chida chimodzi kapena ziwiri zokha. Ngati ankakonda kuphunzira zinenero kuti azilankhula ndi anthu m’zinenero zawo, mwina anadziwa bwino zinenero ziwiri kapena zitatu zokha. Akanakhala ndi moyo wautalipo, akanatha kuchita zambiri, monga kudziwana ndi anthu atsopano, kutulukira zinthu zatsopano, ndi kuyandikana ndi Mulungu.

Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu analenga munthu m’njira yoti akhoza kusangalala ndi zinthu zambirimbiri, kenako n’kumugwiritsa mwala pomupatsa moyo waufupi woti akhoza kusangalala ndi zinthu zochepa zokha?’ Kufupika kwa moyo wa munthu sikukugwirizana ndi mmene zinthu zinapangidwira bwino m’chilengedwe. Mwina mungadzifunsenso kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu anapanga munthu ndi makhalidwe apadera ngati chilungamo ndi chifundo, koma n’kumupatsanso mtima wokonda kuchita zinthu zoipa?’

Mukaona galimoto yokongola itaphwanyika penapake, kodi mumanena kuti inapangidwa choncho? Ayi. Mwachidziwikire mumaganiza kuti, ‘Galimotoyi sinapangidwe chonchi. Iyenera kuti inapangidwa bwino, koma winawake anaiwononga.’ Mofanana ndi zimenezo, tikaganizira za njira yodabwitsa imene tinapangidwira, n’zosachita kufunsa kuti tingaone kuti mmene moyo wathu ulili panopa, si mmene unayenera kukhalira. Kufupika kwa moyo wathu ndiponso mtima wathu wokonda kuchita zinthu zoipa zili ngati kuphwanyika kwa galimoto yokongola. N’zachionekere kuti winawake anawononga moyo wabwino umene anthu anapatsidwa. Ndani anachita zimenezo? Umboni wa m’Baibulo umasonyeza mosapita m’mbali kuti pali munthu mmodzi amene anachita zimenezo.

Ngati anthu anapangidwa m’njira yoti azitha kukhala ndi moyo wosatha, ndani amene pambuyo pake akanawononga moyo wabwino umenewu, umene unapatsidwa kwa mtundu wonse wa anthu? Sangakhalenso wina koma kholo loyamba la anthu onse, mwa amene tonse tinachokera. Kupatula iyeyo, munthu wina aliyense akanawononga mbali yochepa chabe ya anthu, makamaka mbadwa zake. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu, Baibulo, amagwirizana ndi zimenezi, pamene amanena kuti: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu, munthu woyamba], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse.” (Aroma 5:12) Choncho Malemba amasonyeza kuti Adamu ndi amene ali ndi mlandu wowononga cholowa chathu. Nanga kodi poyambirirapo anthu analengedwa kuti akhale ndi moyo wotani?

Kumvetsa Mmene Moyo Unafunikira Kukhalira

Ponena kuti imfa ‘inalowa m’dziko,’ Baibulo likusonyeza kuti anthu sanapangidwe kuti azifa. Ukalamba ndi imfa zinabwera kwa anthu chifukwa choti munthu woyamba anapandukira Mulungu. Koma zinyama sizinapangidwe kuti zizikhala ndi moyo wosatha.—Genesis 3:21; 4:4; 9:3, 4.

Anthu anapangidwa kuti akhale osiyana ndi zinyama. Anthu ndi zamoyo zapamwamba kuposa zinyama, monga momwe angelo alili zamoyo zapamwamba kuposa anthu. (Ahebri 2:7) Mosiyana ndi zinyama, anthu anapangidwa “m’chifanizo cha Mulungu.” (Genesis 1:27) Ndiponso, mosiyana ndi zinyama, Baibulo limati Adamu ndi “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Choncho tili ndi chifukwa chomveka chokhulupirira kuti anthu sanalengedwe kuti azikalamba ndi kufa. Mulungu saafa, ndipo sanalenge ana ake kuti azifa.—Habakuku 1:12; Aroma 8:20, 21.

Mfundo zina zotisonyeza mmene Mulungu analengera anthu pachiyambi timazipeza tikaona mbiri ya mibadwo yoyambirira ya anthu. Anthu kalelo ankakhala zaka mahandiredi angapo asanakalambe. Adamu anakhala zaka 930. Patadutsa mibadwo ingapo, mwana wa Nowa Semu anakhala zaka 600 zokha, ndipo mdzukulu wa Nowa Aripakasadi anakhala zaka 438. * (Genesis 5:5; 11:10-13) Kenaka Abrahamu anakhala zaka 175. (Genesis 25:7) Zikuoneka kuti uchimo wakhala ukusintha kutalika kwa moyo wa anthu mwapang’onopang’ono, ndipo unachititsa moyo kufupika kwambiri pamene nthawi yakhala ikudutsa kuyambira pamene munthu wangwiro anapangidwa. Koma poyambirira penipeni anthu anapangidwa kuti azikhala ndi moyo wosatha. Choncho, m’pomveka kufunsa kuti, ‘Kodi Mulungu akufunabe kuti anthu azikhala ndi moyo wosatha padziko lapansi?’

Kumasuka ku Ukalamba

Popeza Yehova Mulungu ananena kuti aliyense wosamumvera adzalipira uchimo wakewo mwa kufa, ndiye kuti mbadwa za Adamu zinalibe chiyembekezo chilichonse. (Genesis 2:17) Komabe, Malemba ouziridwa anapereka chiyembekezo chakuti winawake adzalipira malipiro kuti anthu amasuke ku ukalamba. Timawerenga kuti: “M’landitse, angatsikire kumanda, ndam’pezera dipo. Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana; adzabwerera ku masiku a ubwana wake.” (Yobu 33:24, 25; Yesaya 53:4, 12) Pamenepa Baibulo linapereka chiyembekezo chochititsa chidwi kwambiri, choti winawake adzapereka dipo kuti anthu amasuke ku ukalamba!

Kodi ndani akanapereka dipo limeneli? Mtengo wake unali woposa umene ndalama zikanalipira. Ponena za anthu opanda ungwiro, Baibulo limati: “Kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kum’perekera dipo kwa Mulungu . . . kuti akhale ndi moyo osafa.” (Salmo 49:7-9) Komabe, Yesu Kristu anali ndi chinachake cha mtengo wapatali kuposa ndalama. Ali pa dziko lapansi, anali ndi moyo wa munthu wangwiro chifukwa pokhala Mwana wa Mulungu, anatetezedwa kuti asatengere uchimo wa Adamu. Yesu anati anabwera “kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” Pa nthawi ina anati: “Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.”—Mateyu 20:28; Yohane 10:10.

Yesu polalikira ankatchulatchula za chiyembekezo cha moyo wosatha. Wotsatira wake wokhulupirika Petro, nthawi inayake ananena kuti: “Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.” (Yohane 6:68) Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena za moyo wosatha?

Moyo Wosatha

Atumwi a Yesu ankayembekezera kukakhala ndi moyo wosatha kumwamba m’boma la Ufumu wa Yesu. (Luka 22:29; Yohane 14:3) Komabe, Yesu nthawi zambiri ankalankhula za cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi. (Mateyu 5:5; 6:10; Luka 23:43) Choncho, zozizwitsa za Yesu ndiponso zimene ankaphunzitsa zokhudza moyo wosatha, zikutsimikizira malonjezo a Mulungu amene ananena kalekale kudzera mwa mneneri Yesaya. Mneneriyo analemba kuti: “Iye wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.” (Yesaya 25:8) Moyo wa anthu sudzakhalanso wa zaka zochepa chabe za unyamata zotsatiridwa ndi zaka za ukalamba za moyo wofooka ndi wazotsinatsina.

M’dziko latsopano la Mulungu, anthu okhulupirika akadzakhala angwiro adzamasuka ku ukalamba. Baibulo limati: “Cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Tangoganizirani zimenezo! Anthu adzapitiriza kuwonjezera nzeru ndi zinthu zomwe akudziwa. Koma zaka mahandiredi zikamadutsa, mphamvu za unyamata wawo sizidzatha. Kodi inuyo mudzakhalapo nthawi imeneyo kuti mudzaone zimenezi?

Kodi Inuyo Mudzakhala ndi Moyo Wautali Bwanji?

Malinga ndi zimene ananena Yesu, padziko lapansi anthu adzachepa kwambiri chifukwa cha tsiku la Mulungu lopereka chiweruzo. (Mateyu 24:21, 22) Yesu anati: “Chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.”—Mateyu 7:13, 14.

Kuti nanunso mudzakhale ndi moyo wosatha, muyenera kuyesetsa kusangalatsa Mulungu. Chiyambi cha zimenezi ndicho kumudziwa bwino Mulungu. Yesu anafotokoza kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) N’zoona kuti pamafunika khama kuti mumudziwe bwino Mulungu, koma khama lake n’lopindulitsa. Mofanana ndi zimenezi, pamafunika khama kuti mupeze ndalama zogulira chakudya tsiku lililonse. Poyerekezera chakudya ndi kudziwa Mulungu, Yesu anati: “Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira ku moyo wosatha.” (Yohane 6:27) Ndithudi, khama lililonse lomwe mungachite kuti mupeze moyo wosatha n’lopindulitsa.—Mateyu 16:26.

Yesu anati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Choncho kutalika kwa moyo umene mudzakhale nawo, kukudalira pa zomwe muchite chifukwa cha chikondi cha Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Anthu ena amanena kuti zaka zotchulidwa mu nkhani ya m’Baibulo imeneyi kwenikweni ndi miyezi. Komabe, nkhaniyo imati Aripakasadi anabereka Sela ali ndi zaka 35. Ngati zimenezi zikutanthauza miyezi 35, ndiye kuti Aripakasadi anakhala tate asanakwanitse zaka zitatu, zomwe mwachidziwikire n’zosatheka. Ndiponso, machaputala oyambirira a Genesis amasiyanitsa zaka, zomwe zimayendera dzuwa, ndi miyezi, yomwe imayendera mwezi.—Genesis 1:14-16; 7:11.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Pomatha zaka 80, munthu amakhala atachita zinthu zochepa chabe za zimene akanatha kuchita

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Anthu anapangidwa kuti akhale ndi moyo wapamwamba kuposa zinyama

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi galimoto iyi inapangidwa ili yophwanyika?

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Mawu a Mulungu amati anthu adzabwerera ku unyamata