Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

KODI ZINACHITIKIRA KUTI?

1. Kodi n’kuti kumene mwamuna wosapenya chibadwire uyu anayamba kupenya?

Lembani mzera kuzunguliza yankho lanu pa mapupa.

YERUSALEMU

Thamanda la Betesda

Kasupe wa Gihoni

Thamanda la Siloamu

◆ Kodi Yesu anamuchitira chiyani asanam’tumize kumeneko?

․․․․․

◆ Kodi mwamuna ndi mkazi achikulire amene akuoneka pa chithunzichi ndi ndani ndipo kodi n’chifukwa chiyani akuchita mantha?

․․․․․

Kambiranani: Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhaniyi?

ZINACHITIKA LITI?

Lembani mzera kuchokera pa malo alionse olambirira kufika pa chaka chimene anatha kumangidwa.

1513 1512 1473 1027 515 455 B.C.E.

2. 1 Mafumu 6:1, 37, 38

3. Eksodo 40:1, 2, 33

4. Ezara 6:15

NDINE NDANI?

5. Ndinkatumikira mfumu yachikunja, koma luso langa linagwiritsidwa ntchito kumanga kachisi.

NDINE NDANI?

6. Agogo anga aamuna anagwiriziza dzanja la Mose, ndipo ntchito imene ndinagwira inachirikiza chihema.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani mavesi kapena vesi la m’Baibulo lomwe likusowapo.

Tsamba 3 Kodi anthu ambiri amakhala ndi moyo wautali bwanji masiku ano? (Salmo 90:․․․)

Tsamba 9 Kodi Yehova adzaitani imfa? (Yesaya 25:․․․)

Tsamba 17 Kodi kuwerenga Baibulo kwakuthandizani kuchita chiyani? (Machitidwe 17:․․․)

Tsamba 24 Kodi masiponji a m’nyanja ndi umboni wa chiyani? (Salmo 104:․․․)

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? M’mawu anuanu, fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

(Mayankho ali pa tsamba 12)

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Thamanda la Siloamu.—Yohane 9:7.

◆ Yesu anakanda thope ndi malovu n’kulipaka m’maso mwa munthu wosaona.—Yohane 9:6.

◆ Makolo a munthu wosaonayo. Akuopa kuti achotsedwa m’sunagoge.—Yohane 9:18-23.

2. 1027 B.C.E.

3. 1512 B.C.E.

4. 515 B.C.E.

5. Hiramu.—1 Mafumu 7:13, 14; 2 Mbiri 2:12-14.

6. Bezaleli.—Eksodo 17:11, 12; 35:30, 31.