Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Mmene Mungapezere Ntchito ndi Kukhalitsa Pantchitopo (July 8, 2005) Ndikuthokoza chifukwa cha malangizo akuti tizifufuza ntchito iliyonse, ngakhale ngati ntchitoyo ingaoneke yonyozeka. Posachedwapa ndinkafuna kusiya ntchito imene ndimagwira, kuti ndiyambe ntchito yogwira masiku ochepa chabe, n’cholinga choti ndizitha kukhala ndi nthawi yambiri yochita utumiki wachikristu. Komano ndinkasankha mtundu wa ntchito imene ndimafuna. Kenaka ndinapeza ntchito. Koma ntchitoyo ndi yonyozeka, ndipo ndikuyesetsa kuti ndiizolowere. Kukomera kwake n’kwakuti sindikhala wotopa kwambiri ndikamafika kunyumba, ndipo ndimatha kuphunzira Baibulo bwinobwino.

M. I., Japan

Mafoni a M’manja Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani yakuti “Kodi Mafoni a M’manja Ndi Abwino Kapena Oipa?” (February 8, 2005) Ndili ndi zaka 14, ndipo sindinkatha kukhala wopanda foni ya m’manja. Nkhaniyi inandithandiza kumvetsetsa kuti foni isamakhale chinthu chofunika kwambiri pa moyo, makamaka poganizira za mmene mafoni a m’manjawa amakhudzira thanzi. Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani yanu yosangalatsayi.

M. B., Romania

Kwalembedwa . . . Ndine wosangalala kuti ndinawerenga nkhani yakuti “Kwalembedwa kuti Ndidzawaonanso.” (January 8, 2005) Ndili ndi zaka 11, ndipo zimandivutabe kuuza ena za Ufumu wa Mulungu. Koma nditawerenga mbiri ya moyo wa Rosalía Phillips, ndinazindikira kuti Yehova angandithandize. Ndikufuna nditakhala wofalitsa uthenga wabwino, wolimba mtima ngati Rosalía.

P. P., Poland

Ndili ndi zaka 27, ndipo mayi anga anamwalira zaka 24 zapitazo. Kuchokera pamene ndinakhala wa Mboni za Yehova, ndakhala ndi chiyembekezo cholimba chakuti ndidzawaonanso. Ndikuthokoza chifukwa cha nkhani ngati imeneyi, ndikuyamika Yehova, Galamukani!, ndiponso Rosalía potiuza nkhani yake yosangalatsayi.

A. F., Venezuela

Amayi Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani zolembedwa bwino zofotokoza udindo wa amayi pa ntchito yophunzitsa ana. (March 8, 2005) Nkhaniyi inandikhudzadi mtima, ndipo inandipangitsa kuwaimbira foni amayi anga nditangotha kuiwerenga. Ine ndi mchimwene wanga tinaleredwa ndi mayi okha. Anakayambiranso sukulu n’cholinga choti azitha kutisamalira. Ankaonetsetsa kuti nthawi zonse timapezeka ku misonkhano yachikristu ndiponso kokalalikira. Ntchito yawo inapindula. Zikomo kwambiri chifukwa chondikumbutsa chitsanzo chawo chabwino.

M. S., United States

Ndinakumbukira za khama lodzimana la amayi pondiphunzitsa zinthu zauzimu ndiponso khalidwe labwino. Ngakhale kuti abambo sankawapatsa thandizo la ndalama komanso sankawalimbikitsa maganizo, amayi anandiphunzitsa kukonda Yehova. Anandilimbikitsanso kuti ndidzakhale mlaliki wa nthawi zonse. Ndikuganiza kuti sindinkayamikira kwambiri khama la amayi, koma monga mmene nkhaniyi yalongosolera, mayiwa akufunika kuyamikiridwa. Ndinawaimbira foni ndili kutali kwambiri kuwayamikira.

C.H.K., Republic of Korea

Bambo anga sanali Mkristu ngati ifeyo. Mayi anga anandilera “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Poganizira mmene ndinkachitira zinthu nthawi zina, zimenezi sizinali zophweka. Tsopano ndili ndi zaka 24, ndipo ndikuthokoza kuti sanataye mtima, koma anapirira pondiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo.

D. M., Italy