Munda Wokongola Mogometsa
Munda Wokongola Mogometsa
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU GUADELOUPE
ANTHUWO ankakhala m’malo okongola koma anali otanganidwa kwambiri moti analibe nthawi yosangalala ndi kukongola kwakeko. Kuyambira m’zaka za m’ma 1600 kupita m’tsogolo, zimenezi n’zimene zinachitikira anthu a ku Africa ambirimbiri amene anatengedwa kwawo mokakamizidwa n’kupititsidwa ku Guadeloupe ndi ku Martinique. Anthu amenewa anathera nthawi yawo yonse akugwira ntchito yaukapolo m’minda ya nzimbe ya m’zilumba zimenezi za panyanja ya Caribbean kwa moyo wawo wonse.
Anthu ambiri amene anali ndi mafamu pa zilumbazi ankati akapolowa azidzipezera okha zakudya, choncho akapolowo anadzala minda yawo. Iwo analibe nthawi yogwirira ntchito ina yowonjezereka m’minda yawoyi, koma anatha kudzala zakudya zomwe ankakonda. Ankalima chinangwa, zilazi, ndi zakudya zina zomwe zinali zokoma ndiponso zopatsa thanzi kuposa chakudya chilichonse chomwe mabwana awo akanawapatsa. Ankadzalanso zitsamba za mankhwala ndi zokometsera zakudya pophika.
Mu 1848, boma la France linathetsa ukapolo pa zilumbazo, koma akapolowo atamasulidwa anapitirizabe kulima minda yawo. Masiku ano anthu a ku Guadeloupe ndi ku Martinique, amene ambiri a iwo ali mbadwa za anthu a ku Africa omwe ankalimbikira ntchito aja, akupitirizabe kulima minda imeneyi, imene imatchedwa minda yachikiliyoli.
Tinkhalango Ting’onoting’ono
Mabanja a akapolowo anayamba kukhala ndi minda ya mitundu iwiri. Ankakhala ndi munda wa masamba, womwe nthawi zambiri unkakhala chapataliko ndi nyumba. Ankakhalanso ndi “munda wapanyumba,” (kapena kuti jardin de case, monga momwe eniake amautchulira) womwe unkakhala pafupi ndi nyumba, ndipo munda wachikiliyoli masiku ano umakhala wotere. Munda woterewu umakhala ndi maluwa, udzu, mitengo, ndi zitsamba zambirimbiri zolowanalowana,
zimene zimakhala zothithikana kwambiri ngati mmene zimakhalira zomera za m’nkhalango za ku madera otentha ndi amvula kwambiri. Popeza pampata paliponse pamakhala chomera, poyamba mukhoza kuganiza kuti mundawu ndi wokongola koma wopanda dongosolo. Koma ayi ndithu, umakhala wolongosoka bwino ndipo umakhala ndi magawomagawo. Mwinimundawo amatha kufika pafupi ndi zomera zake zonse podutsa m’tinjira ting’onoting’ono.Mundawo umayambira kumbuyo kwa nyumba kufika kumaso, kumene umakhala malo okongola kwambiri olandirira alendo. Kukabwera alendo, eninyumba amawalandirira m’mundawu, momwe mumakhala maluwa ndi masamba osiyanasiyana okongola.
Kumbali ina ya munda wachikiliyoli, makamaka kumene kumafika mthunzi wa nyumbayo, kumakhala zitsamba zamankhwala. M’minda ya pa zilumbazi mumakhala zitsamba zosiyanasiyana zamankhwala monga sinamoni, zomera zinazake zokhala ngati chisoso, ndi zina zotero. M’mundamo mumameranso udzu wonunkhira ngati mandimu, ndipo masamba ake ouma akawawotcha amathamangitsa udzudzu.
Anthu ambiri pa zilumbazi amanyadira kuti amadziwa mankhwala a zitsamba. Kale munthu akadwala kapena akavulala, nthawi zambiri dokotala ankakhala ali kutali. Choncho chifukwa cha zitsamba zimene zinkamera m’minda yachikiliyoliyi, anthu ankadzichiza okha. Zitsamba zimenezi zimagwiritsidwabe ntchito ngati mankhwala, koma kudzichiza wekha kukhoza kukhala koopsa. Mukamupatsa chitsamba cholakwika wodwalayo, mukhoza kungomuwonjezera matenda m’malo momuchiritsa. Choncho masiku ano, anthu okhala pa zilumbazi akadwala nthawi zambiri amapita kwa munthu wophunzitsidwa bwino zamankhwala.
Mbali yaikulu ya munda wachikiliyoli yomwe imakhala kuseri kwa nyumba, amadzalamo zakudya. Mbali imeneyi kumakhala zilazi, mabilingano, chimanga, letesi, ndi zomera zina, komanso zomera zimene zimakometsa kapena kununkhiritsa zakudyazi. Mukhozanso kupezamo mitengo ya nthochi, mapeyala, magwafa, mango, ndi zipatso zina.
Bwerani Mudzionere Nokha
Mukamayenda pafupi ndi munda wachikiliyoli, mwina mungafune kupita pafupi kuti mukasirire kukongola kwake. Mukalowa m’kati mwake, mukhoza kusirira kukongola kwa maluwa ndi masamba amene amaoneka amitundumitundu akamamenyedwa ndi dzuwa. Panthawi imodzimodziyo, kamphepo kakamawomba mumamva fungo losiyanasiyana labwino, lonunkhira bwino kuposa mafuta onunkhiritsa thupi. Indedi, mungasangalale ndi mundawo, ngakhale kuti mwangobwera chabe kudzauona. Tangoganizirani mmene amasangalalira mwinimundawo, yemwe anaudzala yekha ndipo amabweramo tsiku lililonse!
Kodi minda yachikiliyoli idzakhalako mpaka liti? Anthu ena okhala pa zilumbazi akudandaula chifukwa choti achinyamata sakukhala ndi chidwi chosamalira minda yokongola ndi yothandiza imeneyi, imene yakhalapo kuyambira kalekale. Komabe, achinyamata ambiri, komanso achikulire, amayamikira kukongola kwa mindayi ndi kufunika kwake pa chikhalidwe chawo. Munda wachikiliyoli uliwonse umatikumbutsa momwe akapolo ochokera ku Africa anagwirira ntchito yotamandika yolima minda yokongola ndi yothandizayi, ngakhale kuti moyo wawo unali wovuta.
[Bokosi patsamba 27]
KODI MAWU OTI “KILIYOLI” AMATANTHAUZA CHIYANI?
Mawu akuti “Kiliyoli” poyambirira ankatanthauza anthu omwe makolo awo anachokera ku Ulaya amene anabadwira ku America, koma masiku ano ali ndi matanthauzo osiyanasiyana. Anthu ena a ku Haiti amagwiritsa ntchito mawu oti “Kiliyoli” kutanthauza chinthu chokongola kwambiri ndiponso chapamwamba. Zinenero zina za ku Jamaica, ku Haiti, ndi ku malo ena zimatchedwa Chikiliyoli. Mwachidule, chikiliyoli ndi chinenero chimene chinachokera ku chinenero chosakanizana ndi zinenero zina, koma tsopano chasanduka chinenero cha gulu linalake la anthu.
Mawu oti “Kiliyoli” tsopano amatanthauzanso moyo winawake wapadera, kapena kuti chikhalidwe cha anthu a pa zilumba zambiri za panyanja ya Caribbean. Ku Puerto Rico ndi ku Dominican Republic, mawu achisipanishi ofanana ndi kiliyoli akuti criollo ali ndi tanthauzo limenelinso. M’zilumba za panyanja ya Caribbean, ana a mbadwa za pa zilumbazi, a anthu ochokera ku Africa, ndi a anthu ochokera ku Ulaya, anasakanikirana ndi kukwatirana pa zaka mahandiredi apitawa, ndipo anabereka ana okongola okhala ndi zikhalidwe zochititsa chidwi. Minda yachikiliyoli ya ku Guadeloupe ndi ku Martinique inapatsidwa dzina limeneli chifukwa cha zikhalidwe zochititsa chidwi zimenezi.
[Zithunzi patsamba 26]
Zithunzi zomwe azizunguliza mzere (kuchokera pamwamba): chomera chotchedwa “alpinia,” tsabola, nanazi, koko, ndi khofi.