Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Ku Brazil, anthu omwa mankhwala enaake, amene amapangitsa kuti munthu asamafune kudya, n’cholinga chofuna kuwonda, anawonjezereka ndi 500 peresenti kuchokera m’chaka cha 1997 kufika 2004.—FOLHA ONLINE, BRAZIL.

Anthu oyendetsa ndege atha kupezeka ndi ng’ala nthawi zowirikiza katatu kusiyana ndi anthu wamba, chifukwa choti amayang’ana kwambiri cheza choipa mlengalenga.—THE WALL STREET JOURNAL, U.S.A.

Pa zaka zina 10 zikubwerazi, pafupifupi theka la ana 1.27 biliyoni a ku Asia adzakhala alibe zinthu zofunikira kwambiri pamoyo monga madzi abwino, chakudya, mankhwala, maphunziro ndi pogona.—PLAN ASIA REGIONAL OFFICE, THAILAND.

Utsi umene timapuma anthu ena akamasuta fodya ndi “wowopsa kwambiri kuposa mmene aliyense ankaganizira.” Patatha miyezi 18 kuchokera pamene analetsa kusuta fodya m’maofesi, m’malesitilanti, ndi m’malo ena okhala anthu ambiri ku Pueblo, Colorado, ku United States, chiwerengero cha anthu odwala matenda amtima ku derali chinachepa ndi 27 peresenti.—TIME, U.S.A.

Mabanja Amene Akutha ku Spain Akuwonjezereka

M’chaka cha 2000, chiwerengero cha mabanja amene analipo ku Spain chinali chowirikiza kawiri chiwerengero cha mabanja amene amapatukana kapena kusudzulana. Koma pofika m’chaka cha 2004, mabanja amene amasudzulana amakhala awiri pa maukwati atatu aliwonse amene amamangidwa. Kuchokera m’chaka cha 1981 pamene kunapangidwa malamulo ololeza kusudzulana, ana oposa 1 miliyoni aona makolo awo akuthetsa ukwati. Kodi n’chiyani chimene chikuchititsa kutha kwa mabanjaku? Malinga ndi kunena kwa katswiri wina wa zamaganizo dzina lake Patricia Martínez, “mabanja sakukhazikika chifukwa cha kusintha kwa chikhalidwe cha anthu, kutha ntchito kwa malamulo a chipembedzo ndi makhalidwe abwino, chifukwa choti akazi ayamba kugwira ntchito zolembedwa, komanso chifukwa chakuti amuna akukana kumagwira nawo ntchito zapakhomo.”

Anthu Akunenepa Kwambiri ku China

Dziko la China “lidzakhala ndi anthu onenepa kwambiri okwanira 200 miliyoni pakutha pa zaka 10,” inatero nyuzipepala ya ku London yotchedwa The Guardian. Malesitilanti ogulitsa chakudya chonenepetsa “ali paliponse m’mizinda yambiri, anthu opeza bwino aleka kuchita zinthu zolimbitsa thupi, akukonda kumangoyenda pagalimoto ndipo nthawi zambiri amangokhala pansi kuonerera TV, kugwiritsa ntchito kompyuta ndi kuchita masewera a pavidiyo.” Chiwerengero cha ana amene akunenepa kwambiri chikumawonjezeka ndi 8 peresenti chaka chilichonse, ndipo ku Shanghai ana a m’sukulu za pulayimale opitirira 15 peresenti ndi onenepa kale kwambiri.

Mtsinje Wasonyeza Kuti Anthu Ambiri Akugwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo

Madzi amene anawatenga mu mtsinje wa ku Italy wotchedwa Po asonyeza kuti anthu ambiri okhala pafupi ndi mtsinjewu akugwiritsa ntchito kwambiri mankhwala osokoneza bongo a kokeni kuposa mmene boma linkaganizira, anasonyeza choncho kafukufuku wina amene anafalitsidwa m’magazini yotchedwa Environmental Health. Anthu amene amagwiritsa ntchito kokeni amakodza mkodzo wokhala ndi mankhwala ena ake. Munthu akapezeka ndi mankhwala amenewa mu mkodzo wake, umakhala umboni wokwanira wakuti munthuyo anamwa kokeni. Kuchuluka kwa mankhwalawa mu mtsinjewu kuchokera ku zimbudzi za anthu kukusonyeza kuti pa tsiku limodzi anthu ozungulira malowa amamwa pafupifupi makilogalamu 4 a kokeni, kapena kuti kokeni woti munthu mmodzi akhoza kumumwa maulendo 40,000. Ameneyu ndi kokeni wochuluka kuwirikiza nthawi 80 kuposa kafukufuku amene anapangidwa m’mbuyomu.

Imfa Zoti Zitha Kupewedwa

“Chaka chino, ana oposa 11 miliyoni osakwana zaka zisanu adzafa ndi matenda oti siovuta kuchiza,” linatero Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse mu lipoti lake la chaka cha 2005. Zambiri mwa imfa zimenezi, zimachitika chifukwa cha zinthu zochepa chabe, monga kubadwa masiku asanakwane, matenda opatsirana, kulephera kupuma bwino ndi kubanika pobadwa, chibayo, kutsegula m’mimba, malungo, chikuku, ndi Edzi. “Zambiri mwa imfa zimenezi ndi zoti zitha kupewedwa mwa kugwiritsa ntchito njira zosavuta, zotchipa komanso zothandiza kwambiri zimene zilipo panopa,” linatero lipotilo. Komanso, amayi oposa 500,000 amafa chifukwa chokhala ndi pakati kapena chifukwa cha mavuto a uchembere chaka chilichonse. Zimenezi zimachitika makamaka chifukwa cha “kusowa zipatala zabwino.”