Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ambiri Adzapita Kodi Inunso Mudzapita Nawo?

Anthu Ambiri Adzapita Kodi Inunso Mudzapita Nawo?

Anthu Ambiri Adzapita Kodi Inunso Mudzapita Nawo?

▪ Kupita kuti? Ku Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wakuti “Chipulumutso Chayandikira.” Misonkhano yokwana mahandiredi angapo ya masiku atatu yotereyi, yomwe inayamba ku United States mlungu womalizira wa May, yakonzedwa kuti ichitike m’malo osiyanasiyana kwa miyezi ikubwerayi padziko lonse lapansi. M’chaka china chaposachedwapa, anthu pafupifupi 11 miliyoni anapita ku misonkhano yachigawo yotereyi yokwana 2,981!

M’malo ambiri, misonkhanoyi idzayamba 9:30 m’mawa ndi nyimbo. Lachisanu padzakhala nkhani ngati zakuti “Labadirani Malonjezo a Yehova Opulumutsira Anthu” ndi “Mmene Yehova Amapulumutsira ‘Waumphawi Wofuulayo.’” Nkhani yaikulu, yakuti “Yehova Wakonza ‘Zotiwombola Kosatha’” idzamaliza chigawo cham’mawa.

Lachisanu masana kudzakhala nkhani ngati zakuti “Yehova Amasamalira Anthu Okalamba Mwachikondi,” “Kupulumutsidwa ku Mavuto Opweteka,” ndi “Ntchito ya Angelo Potumikira Anthu.” Nkhani yosiyirana ya mbali zinayi yakuti “Yehova Ndi ‘Mpulumutsi’” idzatsogozana ndi nkhani yomaliza ya chigawo chimenechi yakuti “Palibe Chida Kapena Lilime Lotsutsana Nanu Limene Lidzapambana.”

Pulogalamu yam’mawa Loweruka ikuphatikizapo nkhani yosiyirana ya mbali zitatu ya mutu wakuti “Pitirizani Kuchita Utumiki ‘Mosaleka’” komanso nkhani zakuti “Kuwonjoledwa ku Msampha wa Wosaka Mbalame,” ndi “Kufufuza Zinthu ‘Zakuya za Mulungu.’” Chigawo cham’mawa chidzatha ndi nkhani yotsatizana ndi ubatizo wa m’madzi kwa onse oyenerera.

Nkhani za Loweruka masana ndi monga zakuti “Samalirani Thanzi Lanu M’njira Yogwirizana ndi Malemba,” “Kodi Moyo Wanu Umalamulidwa ndi Mzimu Wotani?,” “Pitirizani Kukhala ndi ‘Chingwe cha Nkhosi Zitatu’ mu Ukwati Wanu,” ndi “Achinyamata, ‘Kumbukirani Mlengi Wanu Wamkulu.’” Nkhani yomaliza yoti, “Kodi Mukukumbukira Tsiku la Yehova?” ili ndi malangizo othandiza m’masiku athu ano.

Pulogalamu ya Lamlungu m’mawa idzaphatikizapo nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Ufumu wa Kumwamba Uli Wofanana ndi . . . ” Nkhani zinayi zidzafotokoza mwachidule ena a mafanizo a Yesu.

Pulogalamu yam’mawa idzapitirira ndi nkhani yofotokozera imodzi mwa mbali zofunika kwambiri za msonkhano, yomwe ndi sewero lokhala ndi zovala zapadera lochokera pa chaputala 13 cha buku la m’Baibulo la Mafumu Woyamba. Gawo lomaliza la msonkhano wachigawo Lamlungu masana lili ndi nkhani ya onse yakuti “Chipulumutso Kudzera mu Ufumu wa Mulungu Chayandikira!”

Konzani panopa zokapezekapo. Kuti mudziwe malo a msonkhano apafupi kwambiri ndi kwanu, funsani ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kapena lembani kalata kwa ofalitsa a magazini ano. Magazini ya March 1 ya Nsanja ya Olonda, yomwe ndi magazini inzake ya ino, ili ndi mndandanda wa malo amene kukachitikire misonkhano yonse ku Malawi ndi misonkhano ya Chichewa ku Mozambique.