Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ Ana 60 pa ana 100 alionse ku Brazil amakhala atawola mano akamafika zaka zitatu. Chinthu chimodzi chomwe chimachititsa zimenezi n’choti makolo amakonda kumwetsera ana m’botolo, ndipo nthawi zambiri amawamwetsa zinthu zotsekemera usiku koma akatha sawatsuka bwinobwino m’kamwa.—FOLHA ONLINE, BRAZIL.
▪ Ana 25 pa ana 100 alionse omwe akubadwa ku United States masiku ano akubadwa mwa njira ya opaleshoni. Mu mzinda wa New York City, chiwerengero cha ana amene akubadwa mwa njira ya opaleshoni chakwera kuwirikiza kasanu chiwerengero cha mu 1980. Chifukwa chimodzi chomwe azimayi akuchitira zimenezi n’choti amatha kubereka pa nthawi imene akufuna, koma kuopsa kochita maopaleshoni osafunikira oterowo “n’kwakukulu.”—THE NEW YORK TIMES, U.S.A.
▪ Pa zaka 100 zapitazi, kutentha kwa mu mzinda wa Mexico City kwawonjezeka ndi madigiri seshasi pafupifupi anayi, pamene padziko lonse lapansi kutenthaku kwawonjezeka ndi madigiri seshasi osakwana ndi imodzi yomwe. Akatswiri akuti zomwe zikuchititsa zimenezi ndi kudula mitengo mwachisawawa ndi kuwonjezeka kwa matawuni.—EL UNIVERSAL, MEXICO.
▪ Anthu opitirira theka amene amachita ukwati ku United States amakhala oti akukhalira kale limodzi. Anthu oterowo amakhala oti ukwati wawo ukhoza kutha mosavuta kusiyana ndi amene amakwatirana asanayambe akhalirapo limodzi.—PSYCHOLOGY TODAY, U.S.A.
Zinthu Zimene Zimakwiyitsa Kwambiri Anthu Ogwira Nawo Ntchito
“Kucheza mokuwa, [kugwiritsa ntchito] foni yotulutsa mawu mokweza ndi kumangokhalira kudandaula za kuchuluka kwa ntchito ndi zina mwa zinthu zimene zimatikwiyitsa kwambiri, zomwe anzathu ogwira nawo ntchito amachita,” inatero nyuzipepala ya Washington Post. Zizolowezi zina zimene zimakwiyitsa ogwira nawo ntchito ndi “kukhala ndi timagulu ta anthu ogwirizana kuntchito, kubwera mochedwa kuntchito, kudzilankhula wekha, kulankhula ndi antchito anzako mokuwa ali m’kachipinda kawo iwenso uli m’kachipinda kako, uve, ndi kudya mwaphokoso.” Zizolowezi zoipa zoterezi zimalowetsanso pansi kagwiridwe ntchito ka anthu. Koma ambiri mwa anthu amene anayankha mafunso a anthu ochita kafukufuku anati sanawalankhulepo anzawo ogwira nawo ntchito amene amachita zinthu zokwiyitsawo. Ndipo nyuzipepalayo inati, “Pali chifukwa chabwino chomwe sanawalankhulirepo. Nawonso mwina amachita zomwezo.”
Anthu Ambiri Akukhala M’mizinda
“Pomatha zaka ziwiri zikubwerazi, theka la anthu padziko lapansi azidzakhala m’mizinda,” inatero nkhani ina yofalitsidwa ndi bungwe la CBC News. Malinga ndi lipoti lina la bungwe la United Nations, ku United States n’kumene kuli anthu ambiri okhala m’mizinda padziko lonse lapansi, chifukwa anthu pafupifupi 9 pa anthu 10 alionse m’dzikoli amakhala m’mizinda. Zaka 55 zokha zapitazo, mizinda iwiri yokha, New York ndi Tokyo ndiyo inali ndi anthu 10 miliyoni kapena kuposa. Masiku ano, nambala imeneyo yafika pa mizinda 20 yokhala ndi anthu oposa 10 miliyoni, kuphatikizapo mzinda wa Jakarta, Mexico City, Mumbai, ndi São Paulo. Kofi Annan, mkulu wa bungwe la United Nations, anati: “Kuchuluka kofulumira kotereku kwa anthu okhala m’mizinda, kudzafuna kuti zinthu zokhudza chuma ndi chikhalidwe zisinthe kwambiri m’mayiko ochuluka.”
Kukana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Chikumbumtima
Komiti yoona za ufulu wa anthu m’dziko la Republic of Korea inati, kukana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima ndi ufulu umene munthu sayenera kulandidwa. Komitiyo inati ufuluwu uyenera kulemekezedwa mwa kukhazikitsa ntchito zina zomwe munthu angagwire ngati sakufuna kulowa usilikali. Nyuzipepala ya The Korea Times inati zomwe yanena komitiyi “zikusiyana” ndi chigamulo chaposachedwapa cha khoti linalake m’dzikolo chomwe chinagwirizana ndi mfundo za m’malamulo ausilikali. Malamulowa saloleza zokhala ndi njira ina yothandizira anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Khoti lalikulu kwambiri m’dzikolo linanena kuti malamulo a dzikolo, osati makhoti, ndi amene ayenera kukhazikitsa ufulu umenewu. Chaka chilichonse, anyamata pakati pa 500 ndi 700 a Mboni za Yehova m’dziko la Republic of Korea amapita kundende chifukwa chokana kulowa usilikali. Pa zaka zapitazi, Mboni pafupifupi 10,000 zamangidwapo pa chifukwa chimenechi.