Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndidzagwire Ntchito Yotani Pamoyo Wanga?

Kodi Ndidzagwire Ntchito Yotani Pamoyo Wanga?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndidzagwire Ntchito Yotani Pamoyo Wanga?

“Poyambirira sindinkaganizako n’komwe za tsogolo langa. Koma nditatsala pang’ono kutsiriza sukulu, ndinayamba kuzindikira kuti tsopano ndikukayamba moyo wina, wofuna kugwira ntchito zolimba komanso wongokhalira kulipira mabilu.”—Anatero Alex, wa zaka 17.

MULI mwana, kodi munayamba mwaganizirapo za ntchito imene muti mudzagwire mutakula? Kodi mukuganizabe za zolinga zimenezo mpaka tsopano? Kapena, kodi mumasokonezeka maganizo mukamaganizira mmene mungamadzapezere zinthu zofunika pamoyo wanu? Ngati n’choncho, simuli nokha. “Kusankha zinthu zoti mudzachite mutakula, n’chinthu chovuta kwambiri kwa achinyamata,” linatero buku lakuti Career Coaching Your Kids.

Komabe, n’kutheka kuti panopo simukuganizirako n’komwe zimene muti mudzachite mutakula, mwinanso ndinu wotanganidwa kwambiri n’kusangalala basi. Ngati n’choncho, palibe chilichonse cholakwika, chifukwa Baibulo limati: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe.” (Mlaliki 11:9) Komabe, inoyi ndi nthawi yabwino kwambiri yoti muyambepo kuganizira za ntchito imene muti mudzachite mutakula. “Wochenjera asamalira mayendedwe ake,” limatero lemba la Miyambo 14:15. Kodi mungasamalire motani mayendedwe anu?

“Dziwani Bwino Kumene Mukupita”

Taganizirani kuti mukufuna kuyenda ulendo wina wautali kwambiri. Mwina mungayambe mwaona kaye mapu kuti mutenge njira yoyenera. N’chimodzimodzinso ndi kukonza tsogolo lanu. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kusankha mwanzeru? Mnyamata wina, dzina lake Michael, amene panopa akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova anati: “Aliyense amakhala ndi zosankha zambirimbiri, koma nkhani yagona pa cholinga chimene mukufuna kukwaniritsa.”

Muziganizira za cholinga chanu monga ngati kuti ndi malo amene mukufuna kupita. Zingakhale zovuta kukafika kumalo amene mukufuna ngati mukungoyenda m’chimbulimbuli. Tinganene kuti mukufunikira kuyang’ana pa mapu anu kuti muone bwino kumene mukupita. Mukatero ndiye kuti mukutsatira malangizo a pa Miyambo 4:26 akuti: “Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako.” Pa lemba lomweli, Baibulo la Contemporary English Version limati: “Dziwani bwino kumene mukupita.”

Zaka zikubwerazi, mudzafunikira kupanga zosankha zofunika kwambiri pamoyo wanu zokhudza kulambira, ntchito, ukwati, kukhala ndi ana, ndi zinthu zinanso zofunika kwambiri. Zidzakhala zosavuta kusankha zinthu mwanzeru ngati mukudziwa bwino kumene mukupita. Koma dziwaninso kuti pali chinthu china chofunika kwambiri kuchikumbukira pamene mukupanga zosankha zokhudza moyo wanu.

‘Ukumbukire Mlengi Wako’

Ngati mukufunadi kukhala ndi moyo wachimwemwe, muyenera kumvera mawu anzeru a Mfumu Solomo akuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.” (Mlaliki 12:1) Chilichonse chimene mungasankhe kuchita chiyenera kugwirizana ndi cholinga chanu chofuna kukondweretsa Mulungu.

N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika? Pa Chivumbulutso 4:11, Baibulo limati: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” Inde, zolengedwa zonse zakumwamba ndi padziko lapansi zili ndi zifukwa zabwino zothokozera Mlengi wawo. Kodi inuyo mumathokoza kuti Mlengi anakupatsani “moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse”? (Machitidwe 17:25) Kodi simumva ngati kuti pali chinthu chinachake chimene muyenera kumupatsa Yehova Mulungu, pothokoza zinthu zonse zabwino zimene amakuchitirani?

Popeza kuti achinyamata ambiri pakati pa Mboni za Yehova amaganizira kwambiri Mlengi wawo, ambiri asankha kuchita utumiki wa nthawi zonse. Mfundo yofunikira kuidziwa n’njakuti, utumiki wa nthawi zonse ndi ntchito yolemekezeka kwambiri, ndipo umabweretsa madalitso osawerengeka. (Malaki 3:10) Koma kuti muchite utumiki umenewu mufunikira kukonzekera kaye. Mwachitsanzo, mungadzifunse kuti: ‘Kodi n’chiyani chimene ndingakwanitse kuchita ndipo ndili ndi luso lotani limene lingadzandithandize kudzipezera zinthu zofunika pa moyo pamene ndili mu utumiki wa nthawi zonse?’

Kelly, amene tsopano ndi mtsikana wa zaka 27, anayamba kukonzekera ali wamng’ono ndithu. Anali ndi cholinga chodziwikiratu chodzachita utumiki wa nthawi zonse. Atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20, anayamba kukonzekereratu za ntchito imene adzagwire. Iye anati: “Ndinafunikira kusankha ntchito yoti idzandithandize kudzipezera zinthu zofunika pa moyo pochita utumiki.”

Adakali kusukulu ya sekondale, Kelly anaphunzira ntchito yokhudzana ndi za mano. Anali kuchita bwino pa ntchito imeneyi mpaka anapambana mpikisano winawake wokonzedwa ndi boma. Koma kupambana kwake sikunamuchititse kusintha cholinga chake choyambirira. Moti Kelly ananena kuti: “Cholinga changa chachikulu chinali kudzachita utumiki wa nthawi zonse, ndipo zinthu zina zonse zinali zocheperapo poyerekezera ndi cholinga chimenechi.” Mpaka pano, Kelly akuchitabe utumiki wa nthawi zonse mosangalala. “Palibe ntchito ina imene ndikanasankha yoposa imeneyi,” anatero Kelly.

Muzifunsa

Ngakhale mutakhala ndi mapu, koma ngati mukupita kumalo amene simukuwadziwa, mungachite bwino kufunsa. Mungachitenso chimodzimodzi pokonzekera tsogolo lanu. Muzifunsa ena. Lemba la Miyambo 20:18 limati: “Uphungu utsimikiza zolingalira.” N’zosachita kukayikira kuti choyambirira mufunikira kufunsa makolo anu. Mungapemphenso malangizo kwa Akristu achikulire omwe amagwiritsa ntchito bwino nzeru za Mulungu pamoyo wawo. “Pemphani malangizo kwa anthu achikulire a mumpingo wanu kapena ongoyandikana nawo achitsanzo chabwino. Anthu amenewa angakuuzeni zinthu zoti simunaziyembekezere n’komwe,” anatero Roberto.

Koposa munthu wina aliyense, Yehova Mulungu akufuna kukuthandizani kusankha zinthu zimene zingakubweretsereni chimwemwe chachikulu pamoyo wanu. Choncho m’pempheni kuti akuthandizeni ‘kuzindikira chifuniro chake,’ posankha zinthu zokhudza tsogolo lanu. (Aefeso 5:17, NW) Ngati mumakhulupiriradi Yehova ndi mtima wanu wonse, ‘Iye adzawongola mayendedwe anu.’—Miyambo 3:5, 6.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi muli ndi luso lotani?

▪ Kodi mukuganiza kuti mungagwiritse ntchito motani luso limenelo potamanda Yehova?

▪ Kodi ndi utumiki wa nthawi zonse uti wotchulidwa m’nkhani ino umene mumafuna mutachita?

[Bokosi patsamba 23]

ZILIBE TSOGOLO

Baibulo limati: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.” Njira yotsogolera ku chuma ili ndi maenje ambiri, ndipo ilibe tsogolo! Nthawi zambiri imathera m’ngongole, nkhawa, ndi mu imfa ya uzimu.—1 Timoteo 6:9, 10.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 24, 25]

KUCHITA UPAINIYA

Mpainiya ndi wofalitsa wachitsanzo chabwino, Mkristu wobatizidwa amene amathera maola 70 mwezi uliwonse akulalikira za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Popeza kuti apainiya amaphunzitsidwa bwino komanso amathera nthawi yochuluka m’ntchito yolalikira, amakhala aluso zedi pophunzitsa ena Baibulo.

KUTUMIKIRA PA BETELI

Anthu a pabanja la Beteli amatumikira pa maofesi a nthambi a Mboni za Yehova, kumene amagwira ntchito yokonza, kusindikiza, ndi kutumiza mabuku ofotokoza Baibulo. Ntchito iliyonse imene imachitika pa Beteli ndi utumiki wopatulika.

KUTUMIKIRA KUMADERA KOMWE KULI KUSOWA KWAKUKULU

Apainiya ena amasamukira kumadera kumene kuli ofalitsa Ufumu ochepa. Ena amaphunzira chinenero china n’kukatumikira kumayiko ena m’mipingo imene imalankhula chinenero chimenecho.

UTUMIKI WA M’MAYIKO ENA

Abale amene amachita utumiki umenewu amapita kumayiko ena kukathandiza pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi maofesi a nthambi. Umenewu ndi utumiki wopatulika wofanana ndi wa anthu amene anamanga kachisi wa Solomo.—1 Mafumu 8:13-18.

SUKULU YOPHUNZITSA UTUMIKI

Sukulu ya milungu isanu ndi itatu imeneyi imaphunzitsa akulu ndi atumiki othandiza osakwatira mmene gulu limayendera ndiponso luso lolankhula pagulu. Ena amene amamaliza sukulu imeneyi amawatumiza kukatumikira ku dziko la kwawo, ndipo ena amatumizidwa kukatumikira m’mayiko ena.

UTUMIKI WAUMISHONALE

Apainiya oyenerera, omwe ali ndi moyo wathanzi ndi wamphamvu, amaphunzitsidwa n’cholinga choti akatumikire kumayiko ena. Amishonale amakhala osangalala ndipo moyo wawo ndi wosangalatsa.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]

KODI NDINGACHITE CHIYANI PAMOYO WANGA?

Vidiyo yotulutsidwa ndi Mboni za Yehova imeneyi, ikusonyeza achinyamata ochokera ku Brazil, Britain, Germany, ndi ku United States akufunsidwa mafunso okhudza moyo wawo. Posachedwapa itulutsidwa mu zinenero zinanso zambiri.

[Chithunzi patsamba 23]

“Nkhani yagona pa cholinga chimene mukufuna kukwaniritsa.”—Anatero Michael, amene akutumikira pa Beteli

[Chithunzi patsamba 24]

“Palibe ntchito ina imene ndikanasankha yoposa imeneyi.”—Anatero Kelly, amene wakhala akuchita upainiya kwa zaka zisanu ndi chimodzi

[Chithunzi patsamba 25]

“Pemphani malangizo kwa anthu achitsanzo chabwino.”—Anatero Roberto, amene akutumikira pa Beteli