Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Mgwirizano Ndi Wofunika Kwambiri pa Moyo (September 8, 2005) Ndinene mosabisa mawu kuti nditangoona chikuto cha magaziniyi, sindinaganize kuti idzandisangalatsa. Koma ndinawerenga nkhani zonse zonena za kufunika kwa mgwirizano, ndipo zinandisangalatsa. Pamene ndinkawerenga nkhanizi, nthawi zambiri ndinkaima kaye kuti ndithokoze Yehova chifukwa cholenga zinthu modabwitsa kwambiri. Zinali zodabwitsa kuona mmene nyama zilili zogwirizana.

B. K., United States

Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndingatani Kuti Ndisayambe Kucheza ndi Anthu Olakwika? (September 8, 2005) Ndinayamba kucheza ndi munthu wolakwika amene sankakonda kwenikweni choonadi cha Baibulo. Nkhaniyi inandithandiza kudziwa kuopsa kocheza ndi munthu wofooka mwauzimu. N’zolimbikitsa kuona kuti Yehova amatisamalira. Zikomo kwambiri chifukwa cha thandizo la panthawi yake.

A. B. K., Zambia

Nkhaniyi inandithandiza kuona kufunika kosintha anthu ocheza nawo. Ngakhale kuti zimenezi zinali zovuta kuchita, nkhaniyi imandilimbikitsabe ndipo ndimaiika pamalo oti n’savutike kuipeza n’kafuna kuiwerenga. Zikomo kwambiri chifukwa chothandiza ndiponso kulimbikitsa achinyamatafe.

L. R., United States

Zimene Baibulo Limanena—Kodi Kupemphera kwa Mariya Virigo N’koyenera? (September 8, 2005) Ndimasirira Mboni za Yehova chifukwa muli ndi khalidwe labwino ndipo magazini anu andithandiza kwambiri. Koma n’chifukwa chiyani mumanena kuti tisamapemphe thandizo kwa Mariya? Iye amatipempherera kwa Atate kuti tikhale ndi mtendere.

E. R., Spain

Yankho la “Galamukani!”: Monga momwe nkhaniyi inafotokozera, Baibulo silitiuza kuti tizipemphera kwa munthu wina aliyense kusiyapo Mulungu. Malinga n’kunena kwa Andrew Greeley, yemwe ndi wansembe ndiponso mlembi wachikatolika, “chizindikiro cha Mariya chimagwirizanitsa mwachindunji Chikristu ndi zipembedzo zakale za milungu yachikazi.” Chotero, kulambira Mariya kunayambira ku chikunja osati Chikristu. Imeneyi ingakhale mfundo yatsopano kwa anthu ambiri owerenga magazini athu, ndipo tikulimbikitsa anthu otero kuphunzira Baibulo kuti apeze zimene kwenikweni limaphunzitsa. A Mboni za Yehova ambiri anali Akatolika, koma ataphunzira Mawu a Mulungu, iwo anaona kuti Mulungu safuna kuti tizipemphera kudzera mwa munthu wina aliyense kusiyapo Yesu Kristu. (Ahebri 7:25) Kuti mudziwe zambiri, onani buku lakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?” * Mutu 15, wakuti “Kupembedza Kumene Mulungu Amavomereza,” umafotokoza chifukwa chake kuli kofunika kuti zimene timakhulupirira zikhale zogwirizana ndi Malemba Oyera.

Makolo (September 8, 2004) Tikuyamikira malangizo omwe ali mu nkhani zofotokoza udindo wa bambo zomwe zili m’magaziniyi. Tazindikira tsopano mmene tingathandizire mwana wathu kukhala ndi mtima wokonda zinthu zauzimu, n’cholinga chokhomereza m’maganizo mwake mfundo za Yehova adakali wamng’ono. Nkhani zimenezi zinangokhala ngati mwalembera ifeyo. Nthawi zonse timalandira thandizo lauzimu limeneli panthawi yake.

K. ndi M. P., Poland

Kuchokera kwa Owerenga Nthawi zonse ndimayembekezera mwachidwi kuwerenga danga lakuti “Kuchokera kwa Owerenga.” Nthawi zina ndikamawerenga kalata yochokera kwa winawake ndimaganiza kuti, ‘Inenso ndikumva chimodzimodzi!’ Panthawi zina ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi mfundoyi sindinaione m’nkhani imene ija?’ Ndiyeno ndimawerenganso nkhaniyo, ndipo nthawi zambiri ndikachita zimenezi ndimasangalala ndiponso kulimbikitsidwa.

M. T., Japan

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.