Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinali Wotaya Mtima Koma Tsopano Ndine Wosangalala

Ndinali Wotaya Mtima Koma Tsopano Ndine Wosangalala

Ndinali Wotaya Mtima Koma Tsopano Ndine Wosangalala

YOSIMBIDWA NDI VICENTE GONZÁLEZ

Anthu oyandikana nane nyumba atamva kuti ndinadziwombera ndi mfuti maulendo anayi koma osafa, anayamba kunditchula kuti Chitsulo. Koma sikuti ndinalidi ngati mmene iwo ankandioneramo ayi. Ndikufotokozereni chifukwa chake ndinkafuna kudzipha.

NDINABADWA mu 1951 ku Guayaquil, m’dziko la Ecuador. Makolo athu anamanga nyumba kumalo ena omwe anthu ankamangako nyumba popanda chilolezo. Uku ndi komwe ankakhala ndi ana awofe, omwe tinalipo asanu ndi anayi. Mabanja osauka anasamukira m’derali, n’kumanga nyumba za nsungwi ndi madenga a malata. Chifukwa choti anamanga nyumbazi m’zithaphwi ndi m’madambo a mitengo ya mizu yoyangayanga, nyumbazi anazisanjika pa mitengo. Tinalibe magetsi, tinkaphikira mbaula ya makala, ndipo tinkayenda mtunda wa kilomita imodzi kukatunga madzi akumwa.

Pofuna kuti azithandiza nawo panyumba, akulu anga anayamba ntchito ali ang’onoang’ono. Ndili ndi zaka 16, nditasiyira panjira sukulu, ndinayamba ntchito yaumesenjala pa fakitale ina. Ine ndi anzanga tinayamba kumwa mowa ndi kumachita makhalidwe oipa. Chikumbumtima changa chikandivutitsa, ndinkapita kukalapa. “Walapa bwino kwambiri,” wansembe ankakonda kutero asanandiuze kuti ndizipita kwathu, popanda kundipatsa thandizo lililonse lauzimu. Motero ndinangopitiriza kuchita zomwezo. M’kupita kwa nthawi, kuchimwa n’kupita kolapa kunakhala kopanda tanthauzo lililonse, ndipo ndinasiya kupita ku tchalitchi. Chapanthawi yomweyo ndinazindikira kupanda chilungamo komwe kunkachitika m’dera lathulo. Kwa anthu osauka, omwe anali ambiri, moyo unali wovuta kwambiri, pamene anthu olemera, omwe anali ochepa, ankakhala moyo wawofuwofu. Sindinkaona phindu lokhalira ndi moyo. Ndinkaona kuti ndilibe tsogolo kapenanso cholinga m’moyo.

Kenako tsiku lina ndinatulukira kuti alongo anga anayi anali kuwerenga mabuku a Mboni za Yehova. Nanenso ndinayamba kuwawerenga. Ndinachita chidwi makamaka ndi buku lina, lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Bukuli linanditsegula maso pa mfundo zambiri za m’Baibulo, ndipo linazifotokoza mogwira mtima. ‘Ichi ndiye choonadi!’ Ndimakumbukira kuti ndinanena ndekhandekha mawu amenewa. Koma ndinadzionera ndekha m’zaka 15 zotsatira, kuti kutsatira choonadi kunali kovuta kwambiri.

Ndili ndi zaka 22 ndinayamba kugwira ntchito m’banki. Tsiku lina mnzanga amene ndinkagwira naye ntchito anandisonyeza mmene ankadzibwerekera yekha ndalama mwakabisira m’bankimo, ndi kuzibwezera pambuyo pake. Nanenso ndinayamba kuchita zimenezi, mpaka zinachuluka kwambiri moti sindinathenso kubisa kulakwa kwanga. Ndinasowa mtendere nditadziwa kuti sindithanso kubweza ndalamazo. Motero ndinaganiza zoulula kulakwa kwanga, n’kudzipha pambuyo pake monga chilango.

Nditalemba kalata ku bankiyo, ndinagula mfuti yam’thumba, n’kupita kudoko, pamalo omwe sipafikafika anthu, n’kudziombera kawiri m’mutu ndi kawiri kena pachifuwa. Ngakhale kuti ndinavulala kwambiri, koma sindinafe. Mwamuna wina amene anali panjinga ndiye anandipeza ndipo mwamsangamsanga anakonza zondipititsa kuchipatala. Nditachira, anandiimba mlandu wa kuba ndipo kenako ananditsekera m’ndende. Nditatuluka ku ndendeko, ndinkachita manyazi komanso ndinali ndi nkhawa chifukwa chakuti ndinali ndi mbiri yakuti ndine wakuba. Chifukwa choti sindinafe ndi mabala anayi a zipolopolo, anthu oyandikana nane nyumba anayamba kunditcha kuti Chitsulo.

Mwayi Wosintha

Panthawiyi, ndinacheza ndi mmishonale wa Mboni za Yehova, dzina lake Paul Sánchez. Chinthu choyamba chomwe ndinaona chinali chakuti ankamwetulira kwambiri. Paul anali munthu wosangalala, wolimbikitsa moti ndinavomera atandipempha kuti ndiziphunzira Baibulo. Ndinaganiza kuti, ‘Mwina angandithandize kupeza chimwemwe komanso cholinga cha moyo.’

Mothandizidwa ndi Paul, ndinaphunzira kuti Mulungu ali nawo cholinga anthu ndipo tsiku lina, anthu amene amam’konda ndi kum’mvera adzakhala m’paradaiso padziko lapansi. (Salmo 37:29) Ndinaphunziranso kuti si Mulungu amene amachititsa kuti pakhale kupanda chilungamo ndi umphawi, koma izi zimachitika chifukwa chakuti anthu anapandukira Mulungu. (Deuteronomo 32:4, 5) Mfundo za choonadi zimenezi zinali ngati muuni wa moyo wanga. Komabe, kusintha umunthu wanga kunali kovuta kwambiri kusiyana ndi kuphunzira Baibulo.

Ndinalowa ntchito ya mu ofesi yokhudzana ndi kusamalira ndalama za kampani. Apanso ndinalephera kupirira ndipo ndinayamba kuba. Zitafika pokanika kubisa umbava wanga, ndinathawira ku mzinda wina wa ku Ecuador komwe ndinakhalako chaka chimodzi. Ndinayesa kuthawira m’dziko lina, koma sizinatheke, motero ndinabwerera kunyumba.

Ndinakumananso ndi Paul ndipo tinayambiranso kuphunzira. Apa ndinakonza zoti ndiyesetse kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pamoyo wanga komanso kuti nditumikire Yehova. Poganizira zimenezi, ndinamuululira Paul chinyengo chomwe ndinachita, ndipo iye anandilangiza mosapita m’mbali. Anandifotokozera mavesi a m’Baibulo monga Aefeso 4:28, lomwe limati: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito.” Ndinaona kuti m’pofunika kuvomereza kuti ndinalakwa ndi kuvomereza zotsatirapo zake.

Ndili m’kati moganizaganiza za moyo wanga, ndinayamba zojambulajambula. Tsiku lina bambo wina anabwera kunyumba yomwe ndinkagwirira ntchitoyi, n’kufotokoza kuti wachita chidwi ndi chithunzi chinachake. Koma anali mtekitivi, ndipo anali ndi chikalata cholamula kuti ndimangidwe. Motero ndinapitanso ku khoti ndipo kenako kundende. Paul anabwera kudzandiona, ndipo ndinamulonjeza kuti, “Sudzadandaula kuti unangotaya nthawi yako pachabe pondithandiza kumvetsa Baibulo.” Tinapitiriza kuphunzira kundende komweko.

Ndinasinthadi Zenizeni

Nditatuluka kundende, ndinaganiza zoti nditumikire Yehova ndi mtima wonse, ndipo m’zaka ziwiri zotsatira ndinasinthadi. Mu 1988, ndinabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova. Pofuna kubwezeretsa nthawi imene inangopita pachabe, ndinayamba utumiki wa nthawi zonse waupainiya, ndipo ndinkayesetsa kulankhula ndi magulu a achinyamata ovutitsa.

Kagulu kena kankakonda kulembalemba Nyumba ya Ufumu yathu. Popeza ndinkadziwa anthu a m’kagulu kameneko komanso komwe ankakhala, ndinawapitira, n’kuwafotokozera ntchito za Nyumba ya Ufumu, ndi kuwapempha bwinobwino kuti azilemekeza malo athuwo. Kuchokera nthawi imeneyo, nyumbayi sinalembedwenso.

Nthawi ina, tikukonzanso nyumbayo, ndi kupala penti wakale, mnyamata wina wa Mboni, dzina lake Fernando, anakanganula penti pamalo pena pomwe panali mawu akuti “Chule” (La Rana, m’Chisipanishi). “Ndinali ine uyu,” iye anatero. Popeza anali nawo m’kagulu kenakake ka achinyamata ovutitsa, Fernando anapenta dzina lake lantchedzera pa nyumbayo. Koma panthawiyi, mwiniwakeyo anali kufufuta dzinali.

Nthawi yoyamba yomwe ndinaona Fernando, n’kuti bongo wake utasokonekera chifukwa anali atamwa mankhwala osokoneza bongo. Amayi ake anali atam’tumizapo ku malo awiri ophunzitsira ana ovuta, koma sizinathandize. Amayiwo anafika posowa choti achite naye, mpaka anangom’siya yekhayekha panyumba. Pofuna kupeza ndalama zogulira mankhwala akewo, Fernando anagulitsa chilichonse chomwe chinali chofunika, ngakhale zitseko, mawindo, malata ndi zinthu zonse za denga la nyumbayo. Tsiku lina ndinalankhula naye mu msewu, n’kum’patsa botolo la zakumwa zoziziritsa kukhosi, n’kumufotokozeranso kuti angathe kuphunzira Baibulo. Anavomera kutero, ndipo ndinasangalala kwambiri kumuona akulabadira choonadi. Anachoka m’kagulu ka achinyamata ovutitsa, anasiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, anayamba kufika pamisonkhano yachikristu, ndipo pasanapite nthawi yaitali anabatizidwa.

Ine ndi Fernando tikamalalikira kukhomo ndi khomo, nthawi zambiri anthu ankatizindikira n’kufuula kuti, “Chule!” kapena “Chitsulo!” ndi kutifunsa zomwe tikuchita. Sankamvetsa kuona munthu yemwe kale anali m’kagulu ka achinyamata ovutitsa ali limodzi ndi munthu yemwe kale anali mbava, akufika panyumba pawo ndi Mabaibulo m’manja.

Tsiku lina ine ndinkalalikira kwa bambo wina, Fernando ankalankhula ndi munthu wina woyandikana nyumba ndi bambo amene ndinkalankhula nayeyo. Akuloza Fernando, bamboyo anandifunsa kuti: “Mwamuona uyo? Tsiku lina anandilozetsapo mfuti m’mutu amene uja.” Ndinam’tsimikizira bamboyu kuti Fernando anasintha moyo wake ndipo tsopano amatsatira mfundo za m’Baibulo. Ndipo Fernando atatha kulankhula ndi munthu uja, ndinamuitana ndi kufotokozera bamboyo za Fernando. Bamboyo anati: “Ndikukuyamikira mnyamata iwe chifukwa choti unasintha moyo wako.”

Sindingathe kukumbukira kuti ndi maulendo angati amene anthu ananena mawu ngati amenewa kwa ineyo ndi Fernando. Izi zakhala zikutipatsa mpata wabwino wolalikira, zomwe zinkathandiza kuti tikhale ndi maphunziro ambiri a Baibulo. Inde, tonse awirife, ineyo ndi Fernando, timaona kuti ndi ulemu waukulu kudziwika kuti ndife Mboni za Yehova.

Chinthu Chosaiwalika Pamoyo Wanga

Mu 2001, nditakwanitsa zaka 50, ndinadzidzimuka komanso kusangalala kwambiri nditaitanidwa kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki yomwe inachitikira m’dziko la Peru. M’sukulu imeneyi, Mboni zoyenerera zimalandira malangizo auzimu ozama kwambiri ozithandiza mu utumiki wawo, ndipo ndi sukulu ya milungu isanu ndi itatu.

Ndinasangalala ndi chilichonse m’sukuluyi, kupatulapo chinthu chimodzi. Ndinkachita mantha kwambiri ndi kulankhula pamaso pa anthu. Ambiri mwa ophunzira achinyamata anakamba nkhani zabwino kwambiri ndipo ankaoneka kuti ndi olimba mtima. Koma n’taimirira kuti ndikambe nkhani yanga yoyamba, maganizo omwe ndinali nawo paubwana wanga, odziona kuti ndine wopanda pake, anandibwerera. Maondo anga anali kunjenjemera, manja omwe anali thukuta lokhalokha ankanjenjemeranso, ndipo mawu anga sankamveka bwinobwino. Komabe, Yehova anandithandiza kudzera mwa mzimu wake woyera ndiponso abale achikondi. Mmodzi mwa alangizi pa sukuluyi anafika mpaka pokhala nane ndi chidwi chapadera ndipo titaweruka m’kalasi anandithandiza kukonzekera nkhani zanga. Chinthu chachikulu chomwe anandiphunzitsa ndicho kudalira Yehova. Pomaliza sukuluyi, kwa nthawi yoyamba m’moyo wanga, ndinasangalala kulankhula pamaso pa anthu.

Kulimba mtima kwanga kunayesedwa kwambiri pa msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova womwe unachitikira ku Guayaquil. Ndinafotokozera anthu 25,000 mmene ndinakhalira Mboni. Koma, ndili m’kati molankhula ndinachita mantha kwambiri chifukwa cha mwayi wolimbikitsa anthu ambiri choncho, mawu anga sankamveka bwinobwino. Pambuyo pake, mmodzi mwa anthu omwe anali pamsonkhanowo anandipeza n’kundiuza kuti, “Mbale González, pamene mumafotokoza nkhani yanu ija, aliyense analengeza misozi m’maso.” Chomwe ndinkafuna kwambiri chinali choti nkhani yanga idzalimbikitse anthu amene mwina angakhale atavutika kusiya makhalidwe awo akale.

Panopo ndine mkulu ndiponso mpainiya wokhazikika ndipo ndasangalala kuthandiza anthu 16 kuzindikira choonadi cha m’Baibulo. Ndine wokondwa kuti makolo anga ndiponso alongo anga anayi nawonso anapereka moyo wawo kwa Yehova. Amayi anga anamwalira m’chaka cha 2001, ali okhulupirika kwa Mulungu. Ndimam’thokoza kwambiri Yehova chifukwa chondilola kuti ndim’dziwe, ndipo sindikudziwa kuti ndingam’thokoze bwanji koposa kuitana ena kuti nawonso akhale mabwenzi ake.—Yakobo 4:8.

[Chithunzi patsamba 12]

Fernando, Chule, kale anali m’kagulu ka achinyamata ovutitsa, ndipo ndinam’thandiza

[Chithunzi patsamba 12]

Paul Sánchez, mmishonale amene anaphunzira nane Baibulo

[Chithunzi patsamba 13]

Vicente González masiku ano