Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Uthenga Uyenera Kuperekedwa

Uthenga Uyenera Kuperekedwa

Uthenga Uyenera Kuperekedwa

KALE, asanatulukire kapangidwe ka matelegalamu, nthawi zambiri zinali zovuta ndiponso zochedwa kuti munthu alankhulane ndi anthu akutali, malinga ndi kayendedwe komanso dera lodutsamo. Taonani mavuto amene Amwenye a ku America otchedwa Ainka, omwe anali ndi ufumu waukulu ku South America, ankakumana nawo.

Ufumu wa Ainka utafika pachimake kumapeto kwa zaka za m’ma 1400 C.E. ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1500 C.E., ena mwa madera ake anali mayiko omwe lero ndi Peru, komwe kunali likulu lakale la ufumuwu lotchedwa Cuzco, ndi mayiko enanso monga Argentina, Bolivia, Chile, Colombia, ndi Ecuador. Kayendedwe kanali kovuta chifukwa cha midadada ya mapiri aataliatali, nkhalango zowirira, ndi kutalika kwa mitunda. Komanso, kupatula nyama zonga ngamila zotchedwa llama, Ainka analibe nyama zina zonyamula katundu, analibe galimoto, ndipo chinenero chawo sichinkalembedwa. Ndiyeno, kodi ankalankhulana motani mu ufumu wawo waukulu ndiponso wa madera osiyanasiyanawu?

Ainka anakonza zoti chinenero chawo chotchedwa Quechua ndicho chizilankhulidwa mu ufumu wawowo. Komanso analambula misewu yambiri. Msewu wawo waukulu unali wa makilomita oposa 5,000, womwe unadutsa m’mapiri a Andes, ndipo msewu wina wa makilomita pafupifupi 4,000 unadutsa kugombe la nyanja ya Pacific. Panalinso misewu ina yomwe inkalumikiza misewu iwiriyi. Ainka analambulanso misewu yowaka ya masitepe, yodutsa m’malo okwera, milatho yoyandama m’madambo, ndi milatho ya zingwe yodutsa mitsinje yoopsa kwambiri. Mlatho wina wotere unali wa mamita 45, ndipo unali ndi zingwe zikuluzikulu ngati thunthu la munthu, ndipo unakhala ukugwira ntchito kwa zaka 500, kufikira mu 1880.

Ainka ankatha kulankhulana chifukwa cha kagulu ka othamanga omwe ankawatcha achasqui, ndipo ankakhala pamalo osiyanasiyana m’misewu ikuluikulu. Aliyense mwa anthu amenewa ankathamanga makilomita atatu kapena anayi n’kumapatsirana mauthenga ndipo akuti patsiku ankathamanga mtunda wa makilomita oposa 160. Mauthenga ambiri ankangowapereka pakamwa koma nkhani zosiyanasiyana za mmene zinthu zikuyendera m’boma zinkakhala pa kachipangizo kochititsa chidwi kotchedwa quipu. Kachipangizo kameneka, komwe kanali ka zingwe za nkhosi zamitundumitundu, kankawathandiza kwambiri kukumbukira zinthu. Nkhosizo zinkakhala ndi mfundo zomwe zinkaimira mawani, mateni, ndi mahandiredi. Anthu ochoka ku Spain atalanda ufumu wa Ainka, quipu inatha ntchito ndipo anthu anaiwala matanthauzo a mfundo zake zija.

‘Akongolatu Mapazi M’mapiri’

Masiku ano anthu mamiliyoni ambiri olankhula chinenero cha Quechua akulandira uthenga wofunika kwambiri. Umenewu ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, boma la dziko lonse lomwe lidzabweretse mtendere kwa anthu ake onse. (Danieli 2:44; Mateyu 24:14) Kuyenda m’madera omwe kale anali kulamulidwa ndi Ainka kudakali kovuta, ndipo palibe mabuku ambiri a chinenero cha Quechua. Koma Mboni za Yehova, ndipo zambiri mwa izo zaphunzira chinenero cha Quechua, zikusangalala kugawa mabuku ndi matepi a zinenero zosiyanasiyana za masiku ano zochokera ku chinenerochi.

Ntchito ya olalikira amenewa ikutikumbutsa mawu ouziridwa awa, akuti: “Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”—Yesaya 52:7.