Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Bwato la ku Galileya—Chuma Chochokera M’nthawi za M’Baibulo

Bwato la ku Galileya—Chuma Chochokera M’nthawi za M’Baibulo

Bwato la ku Galileya—Chuma Chochokera M’nthawi za M’Baibulo

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU ISRAEL

PA Nyanja ya Galileya panachitika zina mwa zinthu zochititsa chidwi kwambiri zokhudza utumiki wa Yesu. Panali pa nyanja imeneyi kapena m’mphepete mwake pamene Mwana wa Mulungu anayenda pamadzi, anachititsa bata mafunde oopsa, anadyetsa anthu ambiri mozizwitsa, ndi kuchiritsa odwala.

Mu 1986, pansi pa nyanjayi kufupi ndi Karpenao wakale anapezapo chinthu chomwe sankayembekezera. Anapezapo bwato lomwe linkayenda panyanjapa kale mu nthawi ya utumiki wa Yesu. Kodi analipeza bwanji? Ndipo kodi tingaphunzire chiyani kuchokera ku bwatoli?

Linapezeka Chifukwa cha Chilala

Chifukwa choti kwa zaka zambiri mvula sinagwe mokwanira, ndipo kenaka m’chaka cha 1985 kunali nyengo yotentha kwambiri, nyanja ya Galileya inaphwa kwambiri. Komanso, m’nyanja ya madzi opanda mchereyi anali kupopamo madzi othirira mbewu. Madzi a m’nyanjamo anaphwera kwambiri, zomwe zinachititsa kuti malo aakulu amatope, omwe kale anali m’madzi, ayambe kuoneka. Amuna awiri apachibale ochokera ku mudzi wina wapafupi anaona kuti umenewu ndi mwayi wawo woti afunefune zinthu zamtengo wapatali zakale. Akuyenda pa matope omwe kale anali m’madziwo, anaona ndalama zachitsulo zingapo ndi misomali yakale ingapo. Kenaka anaona chinthu chooneka ngati chozungulira chili m’matope, chosonyeza malo amene panakwiririka bwato lakale. Anapezadi chinthu chamtengo wapatali!

Anthu okumba m’mabwinja sankayembekezera kuti angapeze bwato la zaka 2000 m’nyanja ya Galileya. Ankaganiza kuti tizilombo tingakhale titawononga kalekale matabwa onse. Komabe, atagwiritsa ntchito njira yodziwira zaka za chinthu chakale, komanso ndalama zimene anazipeza pamalowo, anazindikira kuti bwatolo linali lochokera m’zaka za 100 B.C.E. kapena 100 C.E. Zinali zodabwitsa kuti bwatolo linali losungidwa bwino. Kodi zimenezo zinatheka bwanji?

Zikuoneka kuti bwatolo linasiyidwa pamalo abata, zomwe zinachititsa kuti mbali yake yonse yammunsi ikutidwe ndi matope. Patapita nthawi, matopewo anauma. Choncho, bwato lakaleli linasungika kwa zaka pafupifupi 2000!

Nkhani yoti apeza bwatoli itafala, analitcha Bwato la Yesu. N’zoona kuti palibe amene anaganizadi kuti limeneli linali bwato lenileni limene Yesu ndi ophunzira ake anagwiritsa ntchito. Komabe, zaka zake ndi kufanana kwake ndi mabwato ofotokozedwa m’Mauthenga Abwino kunachititsa chidwi akatswiri a mbiri yakale ndi a Baibulo omwe.

Bwatolo n’lalikulu mamita 8.2 m’litali ndi mamita 2.3 m’lifupi. Amene analipanga anagwiritsa ntchito njira inayake yapadera. M’malo moyamba aika timatabwa ting’onoting’ono m’kati n’kudzaika matabwa akuluakulu kunja, zikuoneka kuti anaika matabwa akuluakulu mwachindunji ku phaka la bwatolo, kenako n’kupanga bwato lonselo. Njira imeneyi inali yofala popanga mabwato oti aziyenda pa nyanja ya Mediterranean. Komabe, mwina bwato la ku Galileyali analisintha kuti lizitha kuyenda panyanja yaing’ono.

Zikuoneka kuti poyamba bwatolo analiika thanga limodzi la makona anayi. Nkhafi zake zinayi zikusonyeza kuti munkakwera anthu osachepera asanu, anayi opalasa bwatolo ndi mmodzi wowongolera. Komabe, bwatolo linkatha kunyamula anthu eyiti kapena kuposa pamenepo. N’zosavuta kuganiza za bwato la saizi yomweyo powerenga za ophunzira seveni amene ankasodza pamene anaona Yesu ataukitsidwa.—Yohane 21:2-8.

Bwato la ku Galileyalo mosakayikira linali ndi malo kumbuyo kwake osungira maukonde akuluakulu osodzera nsomba. Pansi pa malo oterowo pankakhala malo a phe amene asodzi otopa ankatha kukapumulako. Mwina Yesu anali pa malo oterowo, ‘kutsigiro, akugona tulo pamtsamiro’ pamene kunja kunali mphepo ya mkuntho. (Marko 4:38) Akuti mwina ‘mtsamiro’ umenewo unali thumba la mchenga lomwe ankalisunga m’bwatolo kuti bwatolo lizikhazikika bwino pamadzi. *

Asodzi a ku Nyanja ya Galileya

Tangoyerekezerani kuti mwakwera nawo bwato ngati limeneli kalelo m’zaka 100 zoyambirira. Mukamayenda pa nyanja ya Galileya, kodi mungaone chiyani? Pali asodzi, ena ali m’mabwato ang’onoang’ono ndipo ena akuyenda m’madzi osaya, akuponya maukonde awo. Mosonyeza kuti ndi odziwa bwino ntchito yawo, akuponya ndi dzanja limodzi maukonde ozungulira okhala ndi makalanje pansi, amene ankakhala aakulu mamita 6 mpaka 8 m’mimba mwake. Maukondewo amatambasuka pamwamba pa madziwo, kenako amamira n’kugwira nsomba. Msodzi amachotsa nsombazo mwa kukokera ukondewo kumtunda kapena mwina kupita pansi pa madzi n’kukatenga ukondewo nsomba zili m’kati mwake. Baibulo limafotokoza kuti Simoni ndi Andreya ‘anali kuponya’ maukonde awo panyanja, mwina mwa njira yofanana ndi imeneyi.—Marko 1:16.

Mwinanso mungaone gulu la asodzi akucheza mwansangala kwinaku akukonza makoka. Ukonde umenewu ukhoza kukhala wotalika mamita 300, ndipo umakhala choimirira m’madzi kufika mpaka mamita 8 pakati pake, komanso umakhala ndi zingwe zokokera ku mbali zake zonse ziwiri. Asodziwo amasankha malo amene akufuna kuikapo khokalo, ndipo theka la asodziwo amapita kumtunda ndi chingwe chimodzi chokokera. Bwatolo limayenda mwachindunji kupita panyanjapo, ndipo limafunyulula ukonde wonsewo, kenako limatembenuka, n’kumakoka ukondewo pang’onopang’ono kuti ukhale ngati ukuzungulira gombelo. Akatha zimenezi, asodzi otsalawo amatsika m’bwatolo atagwira chingwe chokokera chachiwiri chija. Magulu awiri a asodziwo akamayandikirana, amakoka nsomba zomwe agwira.—Mateyu 13:47, 48.

Chapataliko, mutha kuona msodzi ali yekha ndi mbedza. Yesu nthawi inayake anauza Petro kuti aponye mbedza m’nyanja yomweyi. Mungathe kuganizira za momwe Petro analili wodabwa pogwira nsomba n’kupeza ndalama ya siliva m’kamwa mwake, yokwanira ndendende kulipirira msonkho wa kachisi.—Mateyu 17:27.

Madzulo, panyanjapo sipakumvekanso phokoso lililonse. Mwadzidzidzi, batalo likutha pamene asodzi akuponda m’bwato ndi kumenyetsa nkhafi zawo pamadzi kuti zizichita phokoso kwambiri. Chifukwa chiyani? Aika matchera okhala ngati msampha m’madzi kuti nsomba zikamachita mantha ndi phokosolo, zizikakodwa mu msamphawo. Ukonde wokhala choimirira umenewu, umene suoneka mumdima, umapangidwa m’njira yoti nsomba zizikodwamo mosavuta. Matcherawo amawalowetsa m’madzi kambirimbiri usiku. M’mawa amawatsuka n’kuwayanika kuti aume. Mukuganiza kuti, ‘Kodi pogwira nsomba mozizwitsa, zomwe zafotokozedwa pa Luka 5:1-7, anagwiritsira ntchito matchera?’

Ntchito Yokonzanso Bwatolo

Tiyeni tibwererenso ku nthawi zamakono. Kodi bwato lomwe linafukulidwa lija analitani? Ngakhale kuti linali losawonongeka, matabwa ake anali osalimba, ngati katoni yonyowa. Sakanatha kungolikumba n’kulichotsa m’matopewo. Zikanakhala zomvetsa chisoni kwambiri kuti bwatolo, litapulumuka zaka zambiri choncho, liwonongeke polichotsa m’matopemo. Popeza madzi a m’nyanjayo akanatha kukweranso, anakumba nthumbira mozungulira malo amene panali bwatolo kuti kusafike madzi. Anakumba ngalande pansi pa bwatolo kuti aikepo zinthu zolimba zolichirikizira. Kenako, atachotsa mosamala matopewo, anapopera penti yolimba yoteteza matabwa m’kati ndi kunja kwa bwatolo.

Ntchito ina yovuta yotsatira inali yonyamula bwatolo, lomwe silikanachedwa kuphwasuka, kupita nalo ku malo ena omwe anali pa mtunda wa mamita 300 kuti akayambe ntchito yolikonzanso. Penti anapopera ija inali yolimba, koma kulikhutchumula mwadzidzidzi kukanatha kuphwanya matabwa osalimba a m’kati mwake. Anthu okonzawo anaganizira zogwiritsa ntchito njira inayake yochenjera. Anagumula nthumbira ija n’kulowetsamo madzi. Kwa nthawi yoyamba pa zaka zambiri, bwatolo, litapakidwa penti yamakono, linayandama pa nyanja ya Galileya.

Anamanga thanki ya konkire kuti mukhale bwatolo panthawi imene anali kulikonzanso. Ntchitoyi inatenga zaka 14. Panabuka vuto pamene nyongolotsi zochokera ku mazira a udzudzu zinalowa m’thankilo, zomwe zinavutitsa kwambiri anthu amene ankalowa m’madzi a m’thankimo pokonza bwatolo. Komabe, anthu okonza bwatolo anatulukira okha njira yothetsera vuto limeneli yomwe inali yachikale. Anaikamo nsomba za mtundu winawake, zomwe zinadya nyongolotsizo n’kuyeretsa madziwo.

Kenaka nthawi inafika yoti aumitse bwatolo. Linali likadali losalimba moti sakanangolisiya kuti liume lokha. Madzi amene anali m’matabwa mwake anayenera kulowedwa m’malo ndi chinthu china. Anthuwo anagwiritsa ntchito phula lotha kusungunuka m’madzi kuti lilowe m’malo mwa madziwo, zomwe zinachititsa matabwa a bwatolo kuuma popanda kusintha kaonekedwe.

Atamaliza kukonzanso bwatolo, linaoneka kuti linali bwato la munthu wamba. Linapangidwa ndi matabwa a mitundu 12 yosiyanasiyana. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi chikhoza kukhala choti panthawi imeneyo, matabwa ankasowa. Koma mwina chifukwa chenicheni chingakhale choti mwiniwakeyo sanali wolemera. Bwatolo analikonza maulendo ambirimbiri lisanamire m’nyanjamo.

Bwato la ku Galileyalo mwina silokhudzana m’njira iliyonse ndi Yesu. Komabe kwa anthu ambiri, bwatolo ndi chuma chamtengo wapatali. Likutipatsa mwayi woyang’ana m’mbuyo zaka zambiri n’kuona momwe moyo unkakhalira pa nyanja ya Galileya m’masiku ofunika kwambiri a utumiki wa Yesu pa dziko lapansi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Onani nkhani yakuti “Pa Nyanja ya Galileya,” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2005, tsamba 8, yofalitsidwanso ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 15]

Anthu ogwira ntchito anavutika kuchotsa matope m’kati mwa bwatolo

[Chithunzi patsamba 15]

Atalipaka penti yolimba

[Chithunzi patsamba 15]

Patapita zaka pafupifupi 2,000, bwatolo linayandamanso

[Chithunzi patsamba 15]

Chitsanzo cha mmene bwatolo mwina linkaonekera kalelo

[Chithunzi patsamba 15]

Bwato la ku Galileyalo akulionetsa kwa anthu, ntchito yolikonzanso itatha

[Mawu a Chithunzi patsamba 15]

All photos except model and sea: Israel Antiquities Authority - The Yigal Allon Center, Ginosar