Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikhulupiriro cha Mwana

Chikhulupiriro cha Mwana

Chikhulupiriro cha Mwana

DUSTIN anayamba kukhala nawo nthawi zina mayi ake akamaphunzira Baibulo ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Ngakhale anali ndi zaka 11 zokha, ankaganiza mozama ndipo ankafunsa mafunso ambiri abwino. Pasanapite nthawi anapempha kuti akhale ndi phunziro la Baibulo lakelake ndi mlongo amene anaphunzira Baibulo ndi mayi ake, yemwe kale anali mmishonale. Anayambanso kuuza anzake a ku sukulu zinthu zomwe anali kuphunzira.

Dustin anayamba kupita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu yakwawo, ndiponso ankayankha nawo akafunsa mafunso oti omvetsera aperekepo ndemanga. Iye ndi azibale ake aang’ono atapita kukacheza ndi bambo awo, bambowo anaumirira kuti onse apitire limodzi kutchalitchi. Dustin anafotokoza zifukwa zimene ankafunira kupita ku Nyumba ya Ufumu. Bambo akewo anavomera kuti Dustin apite ku Nyumba ya Ufumu.

Tsiku lina madzulo misonkhano itatha ku Nyumba ya Ufumu, mayi ake a Dustin anamuyang’anayang’ana koma sanamupeze. Popanda kuwauza mayi akewo, Dustin anapita kwa woyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu n’kumufunsa ngati angalembetse m’sukuluyo. Mayi ake anavomereza. Iye ankayembekezera mwachidwi kukamba nkhani yake yoyamba. Koma panthawi yomweyo, anayamba kumva ululu woopsa polumikizira ntchafu yake, ndipo anamutengera kwa madokotala osiyanasiyana kuti akamuyeze. Kenaka, tsiku lofunika kwambiri kwa Dustin linafika, loti akambe nkhani yake yoyamba ku Nyumba ya Ufumu. Panthawi imeneyi ankayendera ndodo. Ngakhale zinkachita kuonekeratu kuti akumva ululu, anayenda wopanda ndodozo popita ku pulatifomu.

Patangopita nthawi yochepa, Dustin anamupeza ndi mtundu winawake wa khansa yam’mafupa wosaonekaoneka. Chaka chotsatira anathera nthawi yambiri ali m’chipatala cha ana mu mzinda wa San Diego, ku California. Ngakhale kuti anapatsidwa mankhwala amphamvu a khansa, ndi chithandizo china chogwiritsa ntchito magetsi, ndipo pamapeto pake anadulidwa mwendo wake wakumanja ndi fupa la m’chiuno, zonsezi sizinafooketse chikhulupiriro chake cholimba mwa Yehova ndi chikondi chake pa Iye. Dustin atafooka kwambiri moti sangathenso kuwerenga, mayi ake, amene ankakhala naye nthawi zonse, ankamuwerengera mokweza mawu.

Ngakhale kuti matenda a Dustin anaipiraipira, sankadandaula. Nthawi zonse ankakhala wotanganidwa, ndipo ankayendayenda pa njinga yake ya anthu olumala kumalimbikitsa odwala ena ndi makolo awo, kuphatikizapo wodwala wina wa Mboni. Anthu ogwira ntchito m’chipatalamo ankatha kuona kuti Dustin ndiponso mwana wina wa Mboniyo anali osiyana ndi ena. Ankaoneka kuti chikhulupiriro chawo chikuwalimbikitsa.

Dustin ankafuna kubatizidwa. Choncho atagona pa sofa, ali wofooka kwambiri moti sakanatha kukhala tsonga, akulu achikristu anamufunsa mafunso amene amafunsa anthu amene akufuna kubatizidwa kuti akhale Mboni za Yehova. Pa October 16, 2004, ali ndi zaka 12 ndi theka, Dustin anabatizidwa pa msonkhano wadera.

Nkhani ya ubatizoyo itatsala pang’ono kuyamba, Dustin anamuyendetsa mu holomo pa njinga ya olumala kuti akakhale limodzi ndi anthu ena ofuna kubatizidwa. Atafunsidwa kuti aimirire, Dustin anaimirira ndi mwendo umodzi, atavala suti yake yabwino kwambiri, atagwirira mpando kuti asagwe. Anayankha mafunso a ubatizowo m’mawu omveka bwino. Anthu onse a m’banja la Dustin analipo, kuphatikizapo bambo ake omubereka ndi akazi awo. Anthu ogwira ntchito m’chipatala chija ndi makolo a ana ena odwala khansa m’chipatalamo analiponso.

Atangobatizidwa chadzulo lake, Dustin anagonekedwanso m’chipatala. Khansayo inali itafalikira kale ku mafupa onse a m’thupi mwake. Atayamba kufooka n’kuzindikira kuti watsala pang’ono kufa, anafunsa mayi ake ngati watsaladi pang’ono kufa. Iwo anayankha kuti, “Ukufunsiranji? Kodi ukuopa kufa?”

“Ayi,” anayankha choncho. “Ndingotseka maso anga, ndipo ndikadzawatsegulanso nditaukitsidwa, ndidzangokhala ngati ndinawatseka timphindi tochepa tapitato. Sindidzamvanso ululu.” Kenaka anafotokoza kuti, “Ndikungodera nkhawa anthu a m’banja mwathu.”

Dustin anamwalira mwezi wotsatira. Ku maliro ake kunabwera madokotala, manesi, achibale a anthu ogwira ntchito m’chipatala, aphunzitsi, anthu oyandikana nawo nyumba, ndiponso anthu a m’banja la Dustin, a Mboni za Yehova ndi enanso omwe sanali Mboni. Dustin anapempha kuti onse amene adzabwere ku maliro ake adzapatsidwe umboni wabwino wa zikhulupiriro zake. Woyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu uja, amene anamupatsa Dustin nkhani ya mu sukulu imodzi yokha yomwe anatha kukamba, anakamba nkhani yabwino kwambiri yolimbitsa chikhulupiriro kwa khamu la anthu amene ankachita kusowa pokhala.

Awiri mwa malemba amene Dustin ankakonda kwambiri analembedwa pa mapepala kuti anthu amene anabwera ku maliroko awaone. Malemba ake anali Mateyu 24:14 ndi 2 Timoteo 4:7. Chikhulupiriro chake cholimba ndi kukhulupirika kwake kunalimbikitsa onse amene ankamudziwa. Tikuyembekezera mwachidwi kuti tidzamuchingamire akadzaukitsidwa.—Yosimbidwa ndi Mboni imene inaphunzira ndi Dustin.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

“Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro.”—2 Timoteo 4:7

[Chithunzi patsamba 26]

Pamwamba: Dustin asanayambe kudwala

[Chithunzi patsamba 26]

Pansi: Dustin akubatizidwa ali ndi zaka 12 ndi theka