Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Akafa Amasanduka Angelo?

Kodi Anthu Akafa Amasanduka Angelo?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Anthu Akafa Amasanduka Angelo?

KAMTSIKANA kena dzina lake Argyro kanafa kali ndi zaka seveni zokha. Makolo ake ali ndi chisoni chachikulu anaweramira bokosi lake la maliro n’kumamuyang’anitsitsa. Argyro anali atavala zovala zoyera. Pofuna kuwatonthoza, mbusa wa mpingo anawauza kuti: “Mulungu anali kufuna mngelo wina, choncho watenga Argyro kuti akakhale naye. Panopa mzimu wake ukuuluka mozungulira mpando wachifumu wa Wamphamvuyonseyo.”

Anthu ambiri amakhulupirira kuti angelo ndi mizimu ya anthu amene anafa, ngakhale kuti ndi zipembedzo zochepa zimene zimaphunzitsa zimenezi. Asangalatsi a anthu apititsa patsogolo maganizo amenewa m’mafilimu ndi m’mapulogalamu a pa TV onena za anthu akufa amene anavomerezedwa kukhala angelo atathandiza ndi kuteteza anthu amoyo.

Kodi mungayembekezeredi kuti okondedwa anu akafa angasanduke angelo? Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhani imeneyi? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni choyamba tione zimene Malemba Oyera amanenadi za mmene angelo alili ndi zimene zimachitikira anthu akufa.

Angelo Analengedwa Mwapadera

Angelo ndi atumiki a Mulungu osaoneka, amphamvu, amene amakhala kudziko lamizimu. Kuti akhaleko sadalira anthu. Angelo ndi mizimu imene inalengedwa ndi Mulungu. Baibulo limati: ‘[Angelo] alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo analengedwa.’Salmo 148:2, 5.

Baibulo limasonyeza kuti angelo okhulupirika mamiliyoni ambiri, kuphatikizapo aserafi ndi akerubi, amatumikira mokhulupirika pogwira ntchito zapadera malinga ndi udindo wawo ndi ntchito zimene anagawiridwa. (Salmo 103:20, 21; Yesaya 6:1-7; Danieli 7:9, 10) Kodi anthu anafunika kufa kuti Mulungu apange angelo onsewo? Zoona zake n’zoti, zimenezo n’zosatheka. Chifukwa chiyani?

Baibulo limasonyeza kuti angelo analengedwa kale kwambiri anthu asanalengedwe. Yehova atalenga dziko limene patsogolo pake anthu anadzakhalapo, angelo, amene mwandakatulo amatchedwa nyenyezi za m’mawa, ‘anaimba limodzi mokondwera, nafuula ndi chimwemwe.’ (Yobu 38:4-7) Choncho anakhalako zaka zambirimbiri anthu asanalengedwe.

Ndiponso, angelo amasiyana kwambiri ndi anthu pa kapangidwe kawo ndi ntchito yawo pa cholinga cha Yehova. * Mulungu analenga anthu kukhala ‘ochepa pang’ono ndi angelo,’ choncho zolengedwa zauzimu zimenezo ndi zapamwamba kuposa anthu ndipo zili ndi nzeru ndi mphamvu zambiri kuposa anthu. (Ahebri 2:7) “Pokhala pawo” pa angelo ndi kumwamba. (Yuda 6) Ponena za anthu, cholinga choyambirira cha Mulungu chinali choti anthu akhale ndi moyo kosatha pa dziko lapansi. (Genesis 1:28; 2:17; Salmo 37:29) Mwamuna ndi mkazi woyamba akanamvera Mulungu, sakanafa. Choncho kuyambira pachiyambi, anthu ndi angelo akhala ndi malo osiyana pa cholinga cha Mulungu.

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akafa?

Mafunso ena ofunika amene tiyenera kuwaona ndi akuti: Kodi anthu akafa chimawachitikira n’chiyani? Kodi amapitirizabe kukhalako koma mwamtundu wina, mwina ngati angelo ku dziko lamizimu? Baibulo lili ndi yankho losavuta ndiponso lomveka bwino ili: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Choncho anthu akafa, sakhalakonso. Anthu akufa sadziwa chilichonse, samva chilichonse, ndiponso sachita chilichonse.

Kodi pali chiyembekezo chilichonse cha anthu akufa? Inde! Baibulo limasonyeza kuti chiyembekezo cha anthu ambiri amene anafa n’choti adzaukitsidwa. Anthu ambiri akufa adzaukitsidwa kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansi laparadaiso.—Luka 23:43; Yohane 5:28.

Anthu ochepa ali ndi chiyembekezo chodzaukitsidwira ku moyo wakumwamba. Chiwerengero chawo n’chochepa, alipo 144,000 basi. Komabe, anthu 144,000 amenewa ndi osiyana ndi zolengedwa zimene zimatchedwa angelo. Mwachitsanzo, a 144,000 adzalamulira ngati mafumu ndi ansembe osafa limodzi ndi Kristu, ndipo ali ndi ulamuliro monga oweruza. (1 Akorinto 6:3; Chivumbulutso 20:6) Kodi amenewa ndi ana amene anafa? Ayi. Ndi otsatira a Kristu amene ayesedwa mpaka pamapeto!—Luka 22:28, 29.

Taganiziraninso kusiyana komwe kulipo pakati pa anthu akufa ndi angelo amoyo. Anthu akufa “sadziwa kanthu bi,” pamene angelo ali ndi chikumbumtima chokwanira, maganizo, ndi nzeru zotha kusankha zochita. Ndi zolengedwa zomwe zili ndi ufulu wodzisankhira zochita. (Genesis 6:2, 4; Salmo 146:4; 2 Petro 2:4) Anthu akufa amafotokozedwa kuti “atha,” kapena kuti, alibe mphamvu, pamene angelo ndi “a mphamvu zolimba.” (Yesaya 26:14; Salmo 103:20) Ndipo anthu ochokera kwa Adamu amafa chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro, pamene angelo oopa Mulungu ndi angwiro, ndipo ndi ovomerezeka kotheratu pamaso pa Yehova.—Mateyu 18:10.

Maganizo oti angelo ndi mizimu ya anthu akufa mwina angachititse anthu kupanga mafilimu ndi mapulogalamu osangalatsa a pa TV, koma maganizo amenewa m’Malemba mulibe. Mfundo zoona za m’Baibulo zomwe tafotokoza mu nkhani ino zimatithandiza kupewa maganizo olakwika alionse a zomwe zimachitikira okondedwa athu akafa. Ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti angelo okhulupirika, omwe analengedwa mwapadera, ndipo ndi atumiki amphamvu a Mulungu, ndi apamwamba kuposa anthu, ndipo nthawi zonse amakhala okonzeka kuchita chifuniro cha Yehova. N’zosangalatsa kuti chifuniro cha Mulungu chimaphatikizapo kugwiritsa ntchito angelo kuti ateteze ndi kuthandiza anthu amene amalemekeza Yehova ndi mtima wonse ndipo amafuna kumutumikira.—Salmo 34:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mawu oti “mngelo” amene amatanthauza “mthenga,” nthawi zina amatanthauza zambiri, kuphatikizapo zolengedwa zauzimu za Mulungu ndi anthu amene anali atumiki ake. Koma mu nkhani ino, tikunena za zolengedwa zauzimu zimene Baibulo limazitcha angelo.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi okondedwa anu amene anamwalira, panopa ndi angelo amene akutumikira Mulungu kumwamba?—Mlaliki 9:5, 10.

▪ Kodi ana amafa chifukwa choti Mulungu akufuna kuwonjezera chiwerengero cha angelo?—Yobu 34:10.

▪ Kodi anthu akufa angabwerenso kudzateteza amoyo?—Yesaya 26:14.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

‘[Angelo] alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo analengedwa.’—Salmo 148:2, 5